Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingathandize Bwanji Anthu Amene Akufunika Thandizo?

Kodi Ndingathandize Bwanji Anthu Amene Akufunika Thandizo?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndingathandize Bwanji Anthu Amene Akufunika Thandizo?

“Ndikufuna kuti ndikadzamaliza sukulu, ndidzapeze ntchito yabwino ya zamagetsi. Ndikufuna kudzathandiza nawo kumanga Nyumba za Ufumu.”—Anatero Tristan, wa zaka 14.

“Ndikupereka ndalama zokwana madola 20 kuti zithandize kulipirira makina atsopano osindikizira. Zimenezi zinali ndalama zanga zodyera, koma ndikufuna kukupatsani inuyo.”—Anatero Abby, wa zaka 9.

MU NTHAWI imene anthu ambiri amafulumira kunena kuti achinyamata ndi odzikonda, achinyamata ambiri, kuphatikizapo amene atchulidwa pamwambawa, akusonyeza kuti ndi osiyana ndi zimenezo. Pakati pa Mboni za Yehova, anyamata ndi atsikana ambiri amagwiritsa ntchito nthawi yawo, mphamvu zawo, ndi ndalama zawo kuthandiza ena. (Salmo 110:3) Taganizirani zitsanzo zina.

Jirah wa zaka seveni wa ku Australia, agogo ake aakazi atangomwalira kumene, anapatsidwa mphatso ya ndalama zokwana madola 50 a ku Australia ndi agogo ake aamuna. Kodi Jirah anatani nazo ndalamazo? Pa msonkhano wampingo wotsatira, anaika ndalama zonsezo m’bokosi la zopereka. Chifukwa chiyani? Jirah anafotokozera mayi ake kuti: “Ndili ndi zidole zokwanira, koma ndinali ndi agogo aakazi amodzi okha. Ndikudziwa kuti agogowo akanakonda kuti ndipereke ndalama zimenezi, chifukwa ankakonda Yehova kwambiri.”

Hannah wa zaka zisanu wa ku United States amakonda mahatchi. Ankafuna kugula chidole chokhala ngati hatchi, chomwe mtengo wake unali madola 75. Pofuna kumuphunzitsa phindu losunga ndalama, makolo a Hannah nthawi ndi nthawi ankamupatsa ndalama zoti aziika m’banki. Banki yake inali yachitini. Pasanapite nthawi yaitali, Hannah anali ndi ndalama zokwanira kugula chidole chokhala ngati hatchi chija.

Koma chapanthawi yomweyo, mphepo ya mkuntho ya Katrina inasakaza zinthu ku gombe la Gulf Coast. Hannah ankadera nkhawa anthu amene anavutika ndi mphepo ya mkunthoyo, choncho anapereka ndalama zonse zomwe anasunga, zoposa madola 100, kuti zithandize anthuwo. Hannah analemba kalata ku likulu la Mboni za Yehova kuti: “Ndikufuna kukupatsani ndalamazi chifukwa ndimakonda Yehova ndipo ndikufuna kuthandizako.” Kodi Yehova amaona kuolowa manja koteroko? Baibulo limati: “Musaiwale kuchitira chokoma ndi kugawira ena; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo.”—Ahebri 13:16.

Ku Florida kutachitika mphepo za mkuntho ziwiri mu 2004, mtsikana wina dzina lake Tiffany, nayenso wa ku United States, analembera kalata ku likulu la Mboni za Yehova. Iye analemba kuti: “Ine ndi mchimwene wanga Timothy tikufuna kupereka ndalama zokwana madola 110. Nyumba yathu sinawonongeke kwambiri, koma tinaona momwe mphepo za mkunthozo zinawonongera nyumba zina. Tinafuna kuthandizapo, choncho tinayamba kusunga ndalama zathu. Timothy anapeza madola 10 atathandiza kuchotsa makoma a makatoni pa nyumba inayake, ndipo ine ndinasunga madola 100.” Tiffany ali ndi zaka 13 ndipo mchimwene wake Timothy ali ndi zaka seveni zokha! Kodi chimachitika n’chiyani tikaika zosowa za ena patsogolo pa zosowa zathu? Lemba la Miyambo 11:25 limati: “Wothirira madzi nayenso adzathiriridwa.”

Gulu la ana a Mboni ku United States, a zaka zapakati pa 4 ndi 15, anamva kuti okhulupirira anzawo ku Africa akufunika Nyumba za Ufumu. Choncho anaganiza zochitapo kanthu. Iwo anati: “Tinagulitsa mabisiketi ndi masikono kunyumba, ndipo tinapeza madola 106.54. Tinauza anthu kuti ndalamazo mwina zidzagwiritsidwa ntchito kumanga malo ochitira misonkhano ku Africa, kumene anthu angamaphunzirireko Baibulo. Anthu ambiri anatigula malonda athu. Zinatitengera maola nayini, koma zinali zaphindu, chifukwa zinali zopita kwa Yehova!”

Mungathe Kuthandiza

Achinyamata amene nkhani zawo zalembedwa pamwambapa aphunzira kuti mawu amene Yesu ananena ndi oona. Iye anati: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Nanunso mukhoza kupeza chimwemwe chimene chimabwera chifukwa chopatsa. Kodi mungapatse m’njira zotani?

Kodi mwamvapo nkhani za okhulupirira anzanu amene akufunika thandizo? Mwachitsanzo, kodi kwinakwake kwagwa tsoka lachilengedwe? Tayerekezerani mmene mungamvere mutatayikiridwa nyumba yanu, katundu wanu, ngakhalenso wokondedwa wanu atafa? Mtumwi Paulo analembera Akristu kuti munthu aliyense “asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.” (Afilipi 2:4) Ngakhale ngati mukukhala kutali ndi kumene kwagwa tsoka lachilengedwe, mwina mungapereke ndalama zimene zingathandize pa ntchito yopereka thandizo, imene Mboni za Yehova zimachita. *

Pali njira zina zimene mungathandizire anthu amene akufunika thandizo. Mwachitsanzo, ngati ndinu mmodzi wa Mboni za Yehova, bwanji osaganizira za anthu amene mumasonkhana nawo m’Nyumba ya Ufumu kwanuko? Kodi pali achikulire ena amene angafunike kuwathandiza? Kodi mungawathandizeko ntchito zina? Paulo analembera Aroma kuti: “M’chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu.” (Aroma 12:10) Choncho mukaona kuti penapake pakufunika kupereka thandizo, chitanipo kanthu. Khalani okonzeka kuchita ngakhale ntchito zonyozeka. Ndipo kumbukirani kuti kutumikira ena n’kogwirizana ndi kutumikira Mulungu. Baibulo limati: “Wochitira waumphawi chifundo abwereka Yehova; adzam’bwezera chokoma chakecho.”—Miyambo 19:17.

Komatu, njira yaikulu kwambiri imene mungathandizire ena ndiyo kuwauza zimene mukudziwa zokhudza Mawu a Mulungu, Baibulo. Yesu anati: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.” (Yohane 17:3) Panopa, kuposa kale lonse, anthu akufunika kumva uthenga wa choonadi wa m’Baibulo wopatsa moyo. Choncho pitirizani kulalikira nthawi zonse ndiponso mwachangu, muli ndi chikhulupiriro kuti ‘ntchito yanu sikupita pachabe.’—1 Akorinto 15:58.

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 13 Zopereka zoti zigwire ntchito yapadera timaziyamikira. Komabe, zingakhale bwino ngati zoperekazo ziperekedwa ku thumba lothandiza pa ntchito yapadziko lonse ya Mboni za Yehova, chifukwa ndalama zimachotsedwa m’thumba limeneli n’kugwiritsidwa ntchito ngati pagwa zinazake zofunika kuchitapo kanthu.

ZOTI MUGANIZIRE

▪ Kodi mungaganizireko munthu wina amene angafunike kumuthandiza?

▪ Kodi mungachite chiyani kuti mumuthandize?

[Mawu Otsindika patsamba 25]

“Musaiwale kuchitira chokoma ndi kugawira ena; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo.”—Ahebri 13:16

[Bokosi/Zithunzi pamasamba 24, 25]

KODI UBWINO WOPHUNZIRA KUPATSA NDI WOTANI?

“Kuona makolo anga akugwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zawo kutumikira Yehova ndi anansi awo kunandichititsa ineyo kufuna kuchita zomwezo pamoyo wanga. Bambo anga anandiuza kuti: ‘Zingachepe bwanji, zimene umachitira Yehova zimakhala mpaka muyaya. Yehova adzakhalapo kwamuyaya, ndipo adzazikumbukira kwamuyaya. Koma kungodzisangalatsa wekha n’kopanda phindu. Ukafa, zomwe unachita zimafera nawe limodzi.’”—Anatero Kentaro, wa zaka 24, wa ku Japan.

“Kunena zoona, sindinkafuna kuthandiza ntchito anthu okalamba kunyumba kwawo Loweruka masana. Ndinkangofuna kusangalala basi, kukhala ndi anzanga. Koma ndinaona kuti ndikamacheza ndi okalamba, ndinkasangalala. Ndinawadziwa ngati anthu amene ali ofanana ndi ine, amene analinso achinyamata panthawi ina. Zimenezi zinandilimbikitsa kuti ndiziwathandiza.”—Anatero John, wa zaka 27, wa ku England.

“Ndili mwana, ndinkathandiza nawo poyeretsa Nyumba ya Ufumu ndi ntchito zina. Ndinkakondanso kugwira ntchito zamanja pothandiza anthu ena a mu mpingo. Ukathandiza munthu wina, umaona chimwemwe chimene amakhala nacho. Mwachitsanzo, nthawi inayake ndinapita limodzi ndi anthu ena kukakuta mapepala khoma la nyumba ya mlongo wina wachikulire. Mlongoyo anasangalala koopsa! Ukasangalatsa munthu wina, nawenso umasangalala.”—Anatero Hermann, wa zaka 23, wa ku France.

[Chithunzi patsamba 24]

Achinyamata ambiri amapereka ndalama kuti zithandize anthu amene akuvutika chifukwa cha masoka