Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuchokera kwa Owerenga

Kuchokera kwa Owerenga

Kuchokera kwa Owerenga

Kodi Mukhoza Kukodwa mu Msampha Womwa Mowa? (October 8, 2005) Ndawerenga makalata ambiri ochokera kwa owerenga amene ananena kuti: “Nkhani imeneyo inabwera pa nthawi yake.” Sindinayembekezere kuti inenso ndingadzamve choncho, koma zimenezo n’zimene ndinkadziuza pamene ndinali kuwerenga nkhani za m’magazini imeneyi. Kwa kanthawi ndithu, sindinkasangalala chifukwa choti ndinkamwa mowa tsiku lililonse, ngakhale kuti sindinafike pomwa mowa mwauchidakwa. Kenaka nkhani zimenezi zinabwera. Nditawerenga za kuopsa kwake, ndinaona kuti tsopano inali nthawi yoti ndiwonjoke mu msampha umenewu.

K. W., Germany

Nkhani zimenezi zinafotokoza zomwe zinamuchitikira Hilario, amene anakhala akumwa mowa kwa zaka 30 ndipo ‘nthawi zambiri ankayambiranso kumwa.’ Iye anati anthu a mu mpingo ‘sankamuthawa, ndipo anali kumulimbikitsa.’ Koma kodi sanafunika kumudzudzula, kapena ngakhale kumuchotsa kumene mu mpingo?

R. L., United States

“Galamukani!” akuyankha: Nkhani yachidule yofotokoza zomwe zinamuchitikira Hilario sinanene kuti kodi pa zaka 30 zimene iye ankalimbana ndi uchidakwa, anakhala liti Mkristu wobatizidwa. Ndiponso sinafotokoze ngati anadzudzulidwapo ndi akulu mu mpingo. Nkhaniyo inanena kuti Hilario anapatsidwa “malangizo apanthawi yake a m’Baibulo,” amene nthawi zina amaperekedwa ndi komiti ya chiweruzo. Anthu akamalimbana ndi uchidakwa nthawi zina amayambiranso kumwa, ngati momwe Hilario anachitira. Ponena za momwe nkhani zimenezi zimasamalidwira ngati amene ali ndi vutoyo ndi Mkristu wobatizidwa, onani “Nsanja ya Olonda” yachingelezi ya May 1, 1983, tsamba 8 mpaka 11.

Zimene Achinyamata Amadzifunsa—N’chifukwa Chiyani Ndimacheza ndi Anthu Olakwika? (August 8, 2005) Nkhani imeneyi inandithandiza kuona kuti sindiyenera kukhala wogawanika pa zolinga zanga. Inandithandiza kutsimikiza mtima kuti ndisiyane ndi mayanjano oipa. Tsopano ndapanga maubwenzi olimba ndi anthu ambiri mumpingo, achinyamata ndi achikulire omwe. Zimenezi zandichititsa kuona kuti ndimakondedwa ndi anthu amene amakonda Yehova ndiponso amene amandilimbikitsa kupitirizabe kuyenda pa njira ya ku moyo.

M. D., Mexico

Ndinafunitsitsa Kukwanitsa Cholinga Changa (July 8, 2005) Pamene ndinkawerenga nkhani ya Martha, misozi inayenderera m’masaya mwanga. Inenso ndimadwala khunyu. Ndakhala mlaliki wa nthawi zonse kwa zaka teni zapitazi, ndipo nthawi zina zimakhala zovuta, makamaka ndikakomoka. Nkhani ya Martha yandithandiza kukhalabe wotsimikiza mtima kuti ndipitirizebe kuchita utumiki wanga. Inandilimbikitsa kwambiri.

J. S., Poland

Ndili ndi matenda ngati a Martha. Nditawerenga nkhani yake, nanenso ndayamba kusamala zinthu zimene ndimadya. Kwa zaka zoposa teni, ndinalola kuti matenda a khunyu andilepheretse kutumikira Yehova mokwanira. Koma pafupifupi zaka zitatu zapitazo, ndinaganiza zoti ndikhale mlaliki wa nthawi zonse, ndipo sindinong’oneza bondo chifukwa chochita zimenezi. Yehova akudalitseni chifukwa chofalitsa nkhani zolimbikitsa ngati zimenezi!

B.C.C., Brazil

Zimene zinandilimbikitsa kwambiri pa nkhani imeneyi n’zoti Martha anapitirizabe kupirira. Ndinalimbikitsidwa poona kuti ngakhale kuti anafunika kusiya utumiki wake, anali ndi maganizo abwino ndi chikhulupiriro choti Yehova amasangalala ndi utumiki wathu wochokera pansi pa mtima.

S. H., Japan

Ndakumanapo ndi zinthu zofanana ndi zimene Martha anakumana nazo, ndipo ndaphunzira kuzindikira zinthu zimene sindingakwanitse kuchita. Mofanana ndi Martha, ndakwanitsa kutumikira monga mlaliki wa nthawi zonse. Choncho nkhani yake inali yolimbikitsa kwambiri kwa ine.

F. G., Switzerland