Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kufunika Kwenikweni kwa Magazi

Kufunika Kwenikweni kwa Magazi

Kufunika Kwenikweni kwa Magazi

“Anthu onse moyo wawo unayambira ku chinthu chimodzi: ku magazi. Magazi ndi amene ali mphamvu ya moyo wa anthu onse, kaya akhale a mtundu, fuko, kapena chipembedzo chanji.”—Anatero Pulezidenti wa Msonkhano Waukulu wa Bungwe la United Nations.

MOSAKAYIKIRA, mbali zina za mawu ogwidwa kumanzerewa ndi zoona. Magazi ndi ofunika pa moyo wa anthu onse. Inde, ndi amtengo wapatali. Koma kodi mukukhulupirira kuti n’chinthu chabwino ndiponso chanzeru kuti anthu azigawana magazi kuti achize odwala?

Monga momwe taonera, malamulo oona kuti magazi ali bwino amasiyanasiyana padziko lonse lapansi, ndipo kuchiza anthu ndi magazi kuli ndi zoopsa zambiri kuposa mmene anthu ambiri akuganizira. Kuwonjezera apo, madokotala amasiyana kwambiri pa kagwiritsidwe ntchito kawo ka magazi chifukwa cha maphunziro awo, luso lawo, ndi maganizo awo. Komabe, ambiri ayamba kusamala kwambiri asanaike munthu magazi. Madokotala ambiri ayamba kusonyeza kuti akukonda njira zochizira anthu zimene sizigwiritsa ntchito magazi.

Zimenezi zikutifikitsa ku funso lomwe linafunsidwa kumayambiriro kwa nkhani yoyamba ya nkhani zino. Funso lake linali loti, Kodi n’chiyani chimachititsa magazi kukhala ofunika kwambiri? Ngati anthu ambiri masiku ano akukayikira kugwiritsa ntchito magazi pochiritsa odwala, kodi pali ntchito ina imene magazi amagwira?

Mmene Mlengi Wathu Amaonera Magazi

Kalelo m’masiku a Nowa, kholo la anthu onse, Mulungu anakhazikitsa lamulo lochititsa chidwi kwambiri. Ngakhale kuti anapatsa anthu ufulu wodya nyama, anawaletsa kudya magazi. (Genesis 9:4) Anawapatsanso chifukwa chake, ndipo anasonyeza kuti magazi ndi ogwirizana kwambiri ndi moyo wa nyama. Kenaka anadzanena kuti: “Moyo wa nyama ukhala m’mwazi.” Mlengi amaona kuti magazi ndi opatulika. Amaimira mphatso yamtengo wapatali ya moyo imene chamoyo chilichonse chili nayo. Mulungu anabwereza mfundo imeneyi kambirimbiri.—Levitiko 3:17; 17:10, 11, 14; Deuteronomo 12:16, 23.

Chikristu chitangoyamba kumene zaka pafupifupi 2000 zapitazo, Akristu anapatsidwa lamulo ndi Mulungu kuti ‘asale . . . mwazi.’ Lamulolo linaperekedwa, osati poganizira za thanzi lawo, koma poganizira kupatulika kwa magazi. (Machitidwe 15:19, 20, 29) Anthu ena amati lamulo loperekedwa ndi Mulungu limeneli limakhudza kudya magazi kokha, koma mawu oti “musale” ndi odziwikiratu tanthauzo lake. Dokotala atatiuza kuti tisale mowa, sitingaganize kuti tikhoza kuulowetsa m’thupi mwathu kudzera m’mitsempha.

Baibulo limafotokozanso chifukwa china chomwe magazi alili opatulika. Magazi okhetsedwa a Yesu Kristu, amene amaimira moyo waumunthu umene anapereka m’malo mwa anthu, ndiwo maziko a chiyembekezo cha Akristu. Ndiwo amatheketsa kuti munthu akhululukidwe machimo ndi kukhala ndi chiyembekezo chokhala ndi moyo wosatha. Mkristu akasala magazi, ndiye kuti akusonyeza chikhulupiriro chake choti magazi okhetsedwa a Yesu Kristu okha ndi amene angamuwomboledi ndi kupulumutsa moyo wake.—Aefeso 1:7.

Mboni za Yehova zimadziwika bwino kuti zimatsatira kwambiri malamulo a m’Baibulo amenewa. Zimakana kuikidwa magazi athunthu kapena mbali zake zinayi zikuluzikulu, zomwe ndi maselo ofiira, madzi a m’magazi, maselo oyera, ndi maselo othandiza magazi kuundana. Ponena za tizigawo ting’onoting’ono tochokera ku mbali zimenezi, ndiponso mankhwala okhala ndi tizigawo timeneti, Baibulo silinenapo kalikonse. Choncho Mboni iliyonse imasankha yokha chochita pa nkhani zimenezi. Kodi kutsatira mfundo za m’Baibulo kumeneku kumatanthauza kuti Mboni zimakana mankhwala kapena zimapeputsa thanzi lawo ndi moyo wawo? Ayi!—Onani bokosi lakuti “Mmene Mboni za Yehova Zimaonera Nkhani Zokhudza Thanzi.”

M’zaka zaposachedwapa, madokotala ambiri aona kuti Mboni zapindula pa nkhani zamankhwala chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo. Mwachitsanzo, dokotala wina wochita maopaleshoni a minyewa ndi ubongo posachedwapa analankhulapo zoti akugwirizana ndi kusankha njira zina m’malo moika anthu magazi. Iye anati: “Ndi chinthu chabwino kwambiri kuchita, osati kwa Mboni za Yehova zokha, koma kwa aliyense.”

Nkhani zazikulu zokhudza thanzi zikhoza kubweretsa nkhawa yaikulu ndipo zimakhala zovuta kusankhapo zochita. Ponena za chizolowezi chofala choika anthu magazi, tamvani zimene ananena katswiri wina wodziwa za mapapo ndiponso mkulu wapachipatala dzina lake Dr. Dave Williams. Anati: “M’pofunika kuti tizilemekeza zofuna za anthu, . . . ndipo tiyenera kusamala kwambiri ndi zimene timaika m’matupi mwathu.” Mawu amenewo ndi oona, makamaka masiku ano kuposa kale lonse.

[Bokosi/Zithunzi patsamba 11]

Kodi Mankhwala Otchedwa HBOC N’chiyani?

Mu selo lofiira lililonse la m’magazi muli tinthu tinatake totchedwa himogulobini tokwana 300 miliyoni. Himogulobini amapanga mbali imodzi mwa mbali zitatu zilizonse za selo lofiira lomwe lamaliza kukula. Himogulobini aliyense amakhala ndi puloteni lotchedwa gulobini ndiponso zinthu zimene zimabweretsa mtundu wofiira zotchedwa heme, zomwe zimakhalanso ndi atomu ya ayironi. Selo lofiira la magazi likadutsa m’mapapo, mpweya wa okosijeni umalowa mu selolo n’kumamatizika ku himogulobini. Pakadutsa masekondi angapo, okosijeniyo amachoka n’kulowa m’minofu ya m’thupi, zomwe zimathandiza kuti maselo apitirirebe kukhala ndi moyo.

Anthu ena opanga zinthu tsopano akumapanga himogulobini, kumuchotsa m’maselo ofiira a anthu kapena a ng’ombe. Himogulobini yemwe amupezayo amamusefa kuti achotsemo zoipa, amamusintha ndi kumuyeretsa ndi mankhwala, kenaka amamusakaniza ndi madzi n’kumusunga m’paketi. Mankhwala amene amapangidwa mwa njira imeneyi, omwe sanavomerezedwebe kuti agwiritsidwe ntchito m’mayiko ambiri, amatchedwa HBOC. Popeza heme ndi amene amachititsa magazi kuoneka ofiira, botolo la HBOC limaoneka ngati botolo la maselo ofiira a magazi, omwe ndi mbali yaikulu ya magazi kumene HBOC amatengedwa.

Mosiyana ndi maselo ofiira a magazi, amene amafunika kuikidwa m’firiji ndi kutayidwa pakatha milungu yochepa, HBOC akhoza kusungidwa kunja kwa firiji ndi kugwiritsidwa ntchito patadutsa miyezi ingapo. Ndipo popeza chinthu chimene chimakuta maselo, chomwe chimakhala ndi mphamvu imene thupi limatha kuikana, chimakhala chitachoka, sipakhala vuto loti munthu akhoza kudwala akamupatsa mtundu wa magazi osiyana ndi ake. Komabe, poyerekezera ndi tizigawo tina ta magazi, HBOC amadzutsa mafunso ambiri kwa Akristu ofuna kutsatira chikumbumtima chawo, amene amafuna kumvera lamulo la Mulungu pa nkhani ya magazi. Chifukwa chiyani? Popeza HBOC amatengedwa ku magazi, pali mfundo ziwiri zomwe zingafune kuziona bwino. Yoyamba ndi yoti HBOC amagwira ntchito ya mbali yaikulu ya magazi, yomwe ndi maselo ofiira. Yachiwiri ndi yoti himogulobini, amene amapangira HBOC, amapanga mbali yaikulu ya maselo ofiira. Choncho ponena za mankhwala amenewa ndi ena ofanana nawo, Akristu amafunika kuganiza bwino kwambiri asanasankhe chochita. Ayenera kuyamba kaye apemphera ndi kusinkhasinkha mosamala za mfundo za m’Baibulo zokhudza kupatulika kwa magazi. Kenaka, pofunitsitsa kukhalabe ndi unansi wabwino ndi Yehova, aliyense ayenera kutsatira chikumbumtima chake chophunzitsidwa Baibulo.—Agalatiya 6:5.

[Chithunzi]

HIMOGULOBINI

[Bokosi/Chithunzi patsamba 12]

Njira Ina Yabwino

Nyuzipepala ya The Wall Street Journal inati: “Zipatala zambiri tsopano zikupatsa anthu mpata wosankha njira ina: maopaleshoni osagwiritsa ntchito magazi.” Nyuzipepalayo inati: “Njira zimenezi poyamba zinakonzedwa kuti zithandize Mboni za Yehova, koma tsopano aliyense akhoza kuzigwiritsa ntchito, ndipo zipatala zambiri zikulimbikitsa anthu ena onse kuti azichitidwa maopaleshoni osagwiritsa ntchito magazi.” Zipatala padziko lonse lapansi zikuzindikira kuti pamakhala ubwino wosiyanasiyana, makamaka kwa odwala, zikamagwiritsa ntchito njira zomwe zimachepetsa kuika anthu magazi. Panopa, madokotala ambiri akuchiza odwala popanda kuwaika magazi.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 12]

Mmene Mboni za Yehova Zimaonera Nkhani Zokhudza Thanzi

Mboni za Yehova, zomwe zina mwa izo ndi madokotala ndi manesi, zimadziwika padziko lonse lapansi kuti zimakana kuikidwa magazi athunthu kapena mbali zikuluzikulu za magazi. Kodi kugwirizana kwawo pankhani yokana magazi kumachokera pa chiphunzitso chochita kupangidwa ndi anthu kapena maganizo oti chikhulupiriro cha munthu chikhoza kuchiritsa matenda? Ayi, zimenezo si zoona.

Poyamikira moyo wawo monga mphatso yochokera kwa Mulungu, Mboni zimayesetsa kuchita zonse zomwe zingathe kuti zitsatire Baibulo, lomwe zimakhulupirira kuti “adaliuzira Mulungu.” (2 Timoteo 3:16, 17; Chivumbulutso 4:11) Baibulo limalimbikitsa anthu olambira Mulungu kuti apewe zizolowezi ndi makhalidwe amene amawononga thanzi kapena kuika moyo pachiswe, monga kudya kwambiri, kusuta kapena kudya fodya, kumwa mowa mopitirira muyeso, ndi kumwa mankhwala pongofuna kusangalala.—Miyambo 23:20; 2 Akorinto 7:1.

Mwa kukhala ndi matupi ndi malo okhala aukhondo komanso kuchitako zinthu zolimbitsa thupi kuti zikhale ndi thanzi labwino, zimakhala zikuchita zinthu mogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. (Mateyu 7:12; 1 Timoteo 4:8) Mboni za Yehova zikadwala, zimasonyeza kuti zimachita zinthu mwanzeru mwa kupita kuchipatala ndi kuvomera kulandira ambiri mwa mankhwala amene amaperekedwa. (Afilipi 4:5) N’zoona kuti zimamvera lamulo la m’Baibulo loti “musale . . . mwazi,” ndipo zimafuna chithandizo chosagwiritsa ntchito magazi chokha. (Machitidwe 15:29) Ndipo zikasankha kuchita zimenezi, nthawi zambiri zimalandira chithandizo chapamwamba kwambiri kuposa anthu ena.