Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Ndidzadumpha Ngati Nswala’

‘Ndidzadumpha Ngati Nswala’

‘Ndidzadumpha Ngati Nswala’

YOSIMBIDWA NDI FRANCESCO ABBATEMARCO

“N’chifukwa chiyani Mulungu analola kuti zimenezi zichitike? N’chifukwa chiyani zinandichitikira ineyo?” Ndinafunsa mafunso amenewo kambirimbiri! Zoti ndidzakhala moyo wanga wonse ndikuyenda pa njinga ya anthu olumala, osatha kugwiritsa ntchito manja ndi miyendo yanga, zinkandiipira kwambiri.

MU 1962, m’tawuni yaing’ono m’chigawo chotchedwa Basilicata m’dziko la Italy, moyo wanga unatsala pang’ono kutha tsiku lomwe unayamba. Mayi anga anavutika pondibereka ndipo adokotala anawabaya jakisoni amene mankhwala ake anandivulaza kwambiri. Patatha masiku atatu, kathupi kanga kakang’ono kanayamba kunjenjemera kwambiri. Manja ndi miyendo yanga zinafa, ndipo minofu yanga yapakhosi yotulutsa mawu inawonongeka.

Pamene ndinali kukula, ndinali wokhumudwa kwambiri chifukwa cha mmene thupi langa linalili. Sindinkachedwa kukwiya ndipo nthawi zambiri ndinkakalipira anthu amene ndinkakhala nawo. Ndinkamva ngati ndili ndekhandekha m’dziko lonseli, ndipo palibe chimene chinkandisangalatsa pamoyo wanga. Pofika zaka 25, maganizo anga anali atawonongekeratu. Posamvetsa chifukwa chimene Mulungu ankalolera kuti ndizivutika chonchi, ndinafika pa mfundo imene inkaoneka yomveka kwa ine, yoti kunja kuno kulibe Mulungu.

Kuona Zinthu Mosiyana

Tsiku lina m’mawa chakumapeto kwa chaka cha 1987, nditakhala pa njinga ya anthu olumala panja pa nyumba yathu, amuna awiri achinyamata ovala bwino anabwera kufupi nane. Ndinaganiza kuti ankafuna kulankhula ndi mchimwene wanga, ndipo ndinawauza movutikira kwambiri kuti mchimwene wangayo kulibe. Iwo anayankha kuti: “Koma tikufuna kulankhula ndi inuyo.” Zimenezo zinali zodabwitsa chifukwa ndi anthu ochepa chabe amene ankafuna kulankhula nane.

Anandifunsa kuti: “Kodi mumakhulupirira Mulungu?” Ndinayankha mwamwano kuti, “Mmene ndililimu ndingamukhulupirire bwanji?” Tinayamba kukambirana, ndipo ndinazindikira kuti anali Mboni za Yehova. Anandipatsa buku la mutu wakuti Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? * lomwe ndinalitenga monyinyirika. Anandiuza kuti adzabweranso koma ndinkafuna kuti asadzabwerenso.

Mboni ziwirizo zinabweranso monga zinalonjezera, ndipo tinapitiriza kukambirana. Ndikukumbukira mavesi a m’Baibulo amene anandiwerengera, monga lemba la Yesaya 35:5, 6, lomwe limati: “Pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzaimba.” Mawu amenewo anali okoma kwambiri, koma osiyana kwambiri ndi mmene moyo wanga unalili. Sindinkatha kuimirira, ndipo ponena za kudumpha ngati nswala, sindinkaganizako n’komwe. Ndinavomera kuphunzira nawo Baibulo, koma sindinkakhulupirira kuti Baibulo lingandithandize pa mavuto amene ndinali nawo nthawi imeneyo. Ndipo chiyembekezo choti zilema zanga zidzatha tsiku lina chinkaoneka chosatheka.

Patapita kanthawi, Mbonizo zinandiitanira ku Nyumba ya Ufumu. Sindikukumbukira kuti nkhani ya m’Baibulo imene inakambidwa tsiku limenelo inali yonena za chiyani, koma sindidzaiwala mtima waubwenzi ndi chikondi chimene Mbonizo zinandisonyeza. M’malo mongondimvera chisoni, anandichititsa kumva kuti ndinedi wolandiridwa. Lamlungu limenelo ndinazindikira kuti ndiyenera kumapita ku Nyumba ya Ufumu, ndipo ndinayamba kupita ku misonkhano nthawi zonse.

Chopinga Chachikulu Chomwe Ndinafunika Kuthana Nacho

Kuphunzira Mawu a Mulungu kunasintha kwambiri mtima wanga. Zinali ngati madzi ayambanso kuyenda mu mtengo wofota. Ndinayamba kumva zinthu mumtima mwanga zomwe ndinkaganiza kuti sindikanathanso kumva. Zinali zosangalatsa kwambiri kumvanso ngati munthu wamoyo! Ndinafunitsitsa kuuza ena za chiyembekezo chochititsa chidwi chomwe ndinali n’tayamba kuchikhulupirira. (Mateyu 24:14) Koma kodi ndikanayamba bwanji kulalikira? Ndinapemphera ndi mtima wonse kwa Yehova za nkhani imeneyi, kumupempha kuti andionetse njira.

Mu September 1991, mpainiya wina (kapena kuti, mlaliki wa nthawi zonse) anatumizidwa ku mpingo wathu. Tsiku lina ndili ku nyumba kwake, ndinamuuza za cholinga changa chofuna kulalikira. Sindinkatha kulankhula bwinobwino, choncho tinakambirana zoti ndizigwiritsira ntchito taipilaita kulemba makalata. Koma vuto linali loti manja anga anali akufa. Mothandizidwa ndi mpainiyayo, ndinayesera njira zambiri. Ndinayesera kugwira pensulo ndi mano n’kumakhudza zilembo za pa taipilaita ndi pensuloyo. Kenaka ndinayesera kugwiritsa ntchito chipewa chokhala ndi ndodo n’kumasuntha mutu wanga kuti ndikhudze zilembozo. Palibe chimene chinathandiza.

Kenaka, tikukambirana za vutolo, mpainiya yemweyo moseka anati: “Uli ndi mphuno yabwino kwambiri.” Nthawi yomweyo ndinayesera kukhudza zilembozo ndi mphuno yanga ndipo ndinaona kuti zikutheka. Ndinayambano kutha kulemba. Tangoganizirani chintchito chimene chinkakhalapo kuti ndikonze ndi mphuno yanga masipelo olakwika! Kenaka tinaona kuti kugwiritsa ntchito kompyuta kungakhale kophwekerako. Koma kodi ndalama zogulira kompyuta ndikanazipeza kuti? Ndinadikira kuti nthawi yabwino ikwane kenaka ndinalankhula ndi makolo anga. Posakhalitsa, ndinayamba kugwiritsa ntchito kompyuta polemba makalata.

Cholinga Changa Chinakwaniritsidwa

Poyamba ndinkalembera makalata anzanga ndi achibale, kenaka ndinayamba kulembera anthu amene ankakhala m’tawuni yathu ndi matawuni ena oyandikana nafe. Pasanapite nthawi yaitali ndinayamba kulemberana makalata ndi anthu okhala m’dziko lonse la Italy. N’zovuta kupeza mawu ofotokoza bwino chimwemwe chimene ndinkakhala nacho nthawi iliyonse yomwe ndinalandira yankho la kalata yanga. Mu December 1991, ndinavomerezedwa kukhala mlaliki wosabatizidwa wa uthenga wabwino. Ndinalembetsanso mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, yomwe ndi sukulu imene imachitika mlungu uliwonse m’mipingo ya Mboni za Yehova. Ndikapatsidwa nkhani yoti ndikakambe, ndinkaikonzekera bwino kunyumba pakompyuta. Pamsonkhanowo, mnzanga ankapita ku pulatifomu n’kukawerenga zomwe ndakonzekerazo.

Poyamikira chikondi chimene Yehova anali kundisonyeza, ndinazindikira kuti ndinafunika kupereka moyo wanga kwa Mulungu ndi kubatizidwa kuti ndipite patsogolo mwauzimu. Ndinalimba mtima n’kuuza makolo anga za chosankha changa. Sanasangalale, koma mtima wanga wofuna kubatizidwa unali wamphamvu kuposa mantha anga. Mothandizidwa ndi Yehova ndi Mboni zinzanga, ndinabatizidwa mu August 1992. Ndinasangalala kwambiri kuti mkulu wanga ndi mlamu wanga anabwera kudzaonerera ubatizo wanga!

Kusintha Kaganizidwe Kanga

Pang’ono ndi pang’ono, nditayamba kumvetsa bwino mfundo za m’Mawu a Mulungu, ndinaona kuti ndifunika kusintha mbali zosasangalatsa za umunthu wanga. Ndinazindikira kuti chifukwa cha kulumala kwanga, ndinali munthu womana ndi wodzikonda. Ndinavutika kuti ndithetse makhalidwe oipawa. Ndinafunika kudzichepetsa kwambiri ndi kuyesetsa kuti ndisiye kumakhumudwa nthawi zonse chifukwa chodalira anthu ena.

Ndinayesetsanso kusiya kudzimvera chisoni ndi kudziona kuti ndine munthu wovutika. Ndinayamba kumaseka pakachitika zinthu zina zosasangalatsa. Tsiku lina ndikulalikira ku nyumba ndi nyumba, kamtsikana kanatsegula chitseko. Mboni imodzi imene inali nane inakafunsa ngati makolo ake analipo. Kamtsikanako kanakuwa kuti, “Amayi, pakhomo pabwera amuna awiri ndi mwamuna wina wodwala.” Atandiona, amayiwo anachita manyazi kwambiri moti anasowa chonena. Mmodzi mwa anzangawo anati: “Zoona zake n’zoti ndife amuna awiri odwala ndi mmodzi wathanzi.” Tonsefe tinamwetulira, ndipo tinakhala ndi macheza abwino.

Kufuna Kutumikira Mokwanira

Nditabatizidwa ndinatumikira monga mpainiya wothandiza kwa miyezi nayini, kumathera maola 60 mu ntchito yolalikira. Koma ndinkafuna kuchita zowonjezereka. Posakhalitsa ndinayamba kutumikira monga mpainiya wokhazikika, kumatha nthawi yowonjezereka mu ntchito yolalikira. Miyezi ingapo yoyambirira yautumiki waupainiya inali yovuta. Anthu ambiri ankaganiza kuti ndabwera pakhomo pawo kudzapempha ndalama, ndipo zimenezi zinkandichititsa manyazi ineyo ndi Mboni zomwe zinali nane.

Kuwonjezera apo, anthu ambiri mumpingo ankavutika kumva zonena zanga ndipo sankadziwa kuti angandithandize bwanji. Koma mothandizidwa ndi Yehova, komanso chifukwa cha kudzipereka kwa abale ndi alongo anga auzimu, m’kupita kwa nthawi zinthu zinasintha. Anthu tsopano amandiona ngati mmodzi wa Mboni za Yehova amene amayesetsa kuthandiza ena kuphunzira zolinga za Mulungu, osati chabe mwamuna amene ali pa njinga ya olumala.

Mu July 1994, ndinakachita nawo maphunziro a milungu iwiri a apainiya. Ku maphunziro amenewo, tinaphunzira mfundo za m’Malemba zomwe timatsatira pa ntchito yolalikira ndi kupanga ophunzira. Anatiphunzitsanso zinthu zothandiza mu utumiki. Ndinayenera kuthana ndi zopinga zina kuti ndithe kukapezekapo, popeza sukuluyo inachitikira kudera lomwe linali pa mtunda wa makilomita 60 kuchokera kwathu. Zinali zosatheka kuti ndizigona konko, choncho Mbonizo zinkasinthana kundipititsa ku sukuluko m’mawa ndi kundibweretsa kunyumba madzulo. Pa nthawi ya chakudya chamasana, mmodzi mwa iwo ankandinyamula kundipititsa pa nsanjika yachiwiri, pomwe tonse tinkadyera limodzi.

Ndinapatsidwa Udindo Waukulu

Mu March 2003, ndinaikidwa kukhala mkulu mu mpingo. Udindo umenewo umafuna kuti ndizigwira ntchito mwakhama kutumikira anthu ena. Tsopano ndimamvetsa bwino zimene Yesu ankatanthauza pamene ananena kuti: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Ndimagwirira ntchito limodzi ndi bungwe la akulu labwino kwambiri, ndipo andithandiza kuzolowera udindo wanga. Ndimamva kuti mpingo wonse umandiyamikira, makamaka achinyamata, ndipo amandiitana akamachita zinthu zosiyanasiyana. Amaona momwe ndagonjetsera zopinga kuti nditumikire Yehova, ndipo ambiri amandipempha kuti ndiwathandize akamalimbana ndi mavuto awo.

Ndaphunzira kuti thanzi la munthu si chinthu chachikulu chimene chingamubweretsere chimwemwe. M’malo mwake, chofunika ndi kukhala wovomerezeka pamaso pa Yehova ndi kuchita chifuniro chake. Ndimamuthokoza kwambiri chifukwa cha chiyembekezo chodabwitsa choti posachedwapa ndidzasiya kuyendera njinga ya olumala. Zoonadi, ndikuyembekezera mwachidwi nthawi imene ‘ndidzadumphe ngati nswala’ ndi kutumikira Mulungu woona kwamuyaya.—Yesaya 35:5, 6.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mawu Otsindika patsamba 22]

Anthu tsopano amandiona ngati mmodzi wa Mboni za Yehova amene amayesetsa kuthandiza ena kuphunzira zolinga za Mulungu, osati chabe mwamuna amene ali pa njinga ya olumala

[Chithunzi patsamba 21]

Kutaipa ndi mphuno pokonzekera msonkhano wa mpingo