“N’labwino Kwabasi!”
“N’labwino Kwabasi!”
“N’lokoma kuwerenga, zithunzi zake n’zabwino kwambiri, nkhani zowonjezera za kumapeto n’zothandiza kwambiri, ndipo bukuli limamufikadi munthu pamtima. N’labwino kwabasi!”—Anatero John ndi Paula.
“Buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? n’lochititsa chidwi kwabasi chifukwa n’losavuta kumva komanso n’lolembedwa momveka bwino. Ndithudi lithandiza ophunzira Baibulo atsopano onse kusiya zinthu zonse zomwe zimawalepheretsa kupita patsogolo kuti afike potumikira Yehova ndi mtima wonse. Mwina mukutha kuona kuti bukuli landigometsa kwambiri moti ndikuchita kulephera kuthokoza kwake.”—Anatero Joe.
“Mwalemba bwino zinthu zimene anthu akuganizadi, zimene zili m’maganizo mwawo. Ndipo mayankho onse amene mwapereka achokera m’Mawu a Mulungu, Baibulo.”—Anatero Robert.
“Ndi buku labwino kwambiri ndipo lalembedwa ndi ziganizo zosavuta kumva ndiponso lafotokoza bwino zinthu. Mosakayikira, likhudza mitima ya anthu ambiri.”—Anatero Norma.
Buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lili ndi zithunzi zokongola ndipo n’la masamba 224. Tsopano mukhoza kuitanitsa bukuli m’zinenero zoposa 140 ngati mukulifuna. Mukhoza kuitanitsa bukuli mwa kulemba zofunika m’mizere ili m’munsiyi ndipo tumizani ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ino.
Itanitsani lanu!
□ Popanda kulonjeza kuti ndidzachita chilichonse, ndikupempha kuti munditumizire buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.