Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Dongosolo Lodabwitsa la Zomera

Dongosolo Lodabwitsa la Zomera

Dongosolo Lodabwitsa la Zomera

KODI munaonapo kuti zomera zambiri zimamera motsatira dongosolo linalake? Mwachitsanzo, makoko a nanazi akhoza kukhala ndi mamba 8 amene amayenda mozungulira kupita mbali imodzi ndi mamba 5 kapena 13 amene amayenda mozungulira kulowera mbali ina. (Onani chithunzi 1.) Mukaona nthanga za mpendadzuwa, mukhoza kuona kuti zimakhala m’mizere yoyenda mozungulira yokhala ndi nthanga 55 ndi ina yokhala ndi nthanga 89 zopingasana nazo, mwinanso zoposa pamenepa. Mukhozanso kuona mizere yoyenda mozungulira pa ndiwo zamasamba zotchedwa kolifulawa. Mukayamba kuona mizere yozungulirayi, mungayambe kumachita chidwi kwambiri mukapita ku msika kumene amagulitsako zipatso kapena masamba. Kodi zomera zimakula mwanjira imeneyi chifukwa chiyani? Kodi nambala ya mizere yoyenda mozungulira ili ndi tanthauzo lililonse?

Kodi Zomera Zimakula Bwanji?

Mbali zatsopano za chomera monga thunthu, masamba, ndi maluwa, zimamera pamalo amodzi aang’ono kwambiri pa chomeracho. Mbali iliyonse yatsopanoyo imakula kuchoka pathunthu la chomeracho kulowera ku mbali zina zatsopano, ndipo imakula mopendekeka mwanjira inayake kuchokera pa mbali ina imene inamera kale. * (Onani chithunzi 2.) Mbali zatsopano za zomera zambiri zimamera mopendekeka mwanjira inayake yapadera imene imatulutsa mizere yozungulira. Kodi kupendekeka kwapadera kumeneku kumakhala kwakukulu bwanji?

Taganizirani vuto ili: Yerekezerani kuti mukufuna kupanga chomera kuti mbali zatsopano zikamamera zizidzadzana bwino pakati pake popanda kusiya mpata wosagwiritsidwa ntchito. Tiyerekezere kuti mukufuna kuti mbali iliyonse yatsopano ikamamera izimera mopendekeka ndi magawo awiri a magawo asanu alionse kuchokera pa mbali yakale. Vuto lomwe mungakhale nalo n’loti mbali yachisanu iliyonse ingamamere kuchokera pamalo amene panamera kale mbali ina ndiponso ingamalowere kofanana ndi mbali yakale ija. Mbali zosiyanasiyanazo zingamapange mizere yowongoka n’kumasiya mipata yosagwiritsidwa ntchito pakati pa mizereyo. (Onani chithunzi 3.) Zoona zake n’zakuti, mbalizi zikamamera mopendekeka ndi madigiri omwe nambala yake mungathe kuilemba ngati chigawo cha zigawo zingapo, mbalizo zidzalowera kumalo amodzi m’malo mokhala ndi mbali zodzadzana bwino mozungulirazungulira. Kupendekeka kumeneku kokha, kumene amakutcha “kupendekeka kwapadera,” kwa madigiri pafupifupi 137.5, n’kumene kumachititsa zomera kumera modzadzana bwino. (Onani chithunzi 5.) Kodi n’chiyani chimachititsa kuti kupendekeka kwa madigiri amenewa kukhale kwapadera?

Kupendekeka kwapaderaku n’kwabwino chifukwa simungathe kukulemba ngati nambala yomwe ndi chigawo cha zigawo zina zingapo. Kupendekeka kwa nambala ngati 5/8 n’kosatalikirana kwambiri ndi kupendekeka kwapadera, pamene kwa 8/13 kuli pafupiko, ndipo kwa 13/21 kuli pafupi kwambiri, koma palibe nambala yomwe ndi chigawo cha zigawo zingapo yomwe ili ya madigiri ofanana ndendende ndi madigiri a kupendekeka kwapadera kumene kumachititsa kuti zomera zimere modzadzana bwino kwambiri. Choncho mbali yatsopano ikamera motsatira kupendekeka kwapaderaku poyerekezera ndi mbali ina yakale, palibe mbali ziwiri zimene zizidzalowera kofanana. (Onani chithunzi 4.) Choncho m’malo momera m’mizere yowongoka yochokera pamalo amodzi apakati, mbalizo zimamera m’mizere yozungulirazungulira.

N’zochititsa chidwi kuti akagwiritsa ntchito kompyuta kuti asonyeze kakulidwe ka mbali za zomera kuchokera pamalo amodzi apakati pa chomeracho, mbalizo zimapanga mizere yozungulirazungulira kokha ngati digiri ya kupendekeka imene agwiritsa ntchito pakati pa mbalizo ili yofanana molondola kwambiri ndi digiri ya kupendekeka kwapadera kuja. Akangosemphanitsa nambalayi, ngakhale pang’ono kwambiri, mbalizo sizipanga mizere yozungulirazungulira.—Onani chithunzi 5.

Kodi Paduwa Pamakhala Timasamba Tingati?

N’zochititsa chidwi kuti kuchuluka kwa mbali zomera mozungulira zimene zimakhalapo zomera zikamamera motsatira kupendekeka kwapadera kuja, nthawi zambiri kumakhala nambala yochokera mu manambala amene amagwa m’gulu linalake lapadera. Manambalawa amatchedwa manambala a Fibonacci. Manambala amenewa anafotokozedwa koyamba m’zaka za m’ma 1200 ndi Mtaliyana wina wodziwa masamu dzina lake Leonardo Fibonacci. M’gulu la manambala amenewa, nambala iliyonse yobwera patsogolo pa 1 imakhala nambala imene mumapeza mukaphatikiza manambala awiri apambuyo pake. Manambala ake amayenda chonchi: 1, 1, 2, 3, 5, 8, 13, 21, 34, 55, kumangopita choncho.

Maluwa a zomera zambiri zimene mbali zake zimakula m’mizere yozungulirazungulira amakhala ndi timasamba ta maluwa tochuluka kukwana nambala ya m’gulu la manambala a Fibonacci. Malinga n’zomwe anenapo ofufuza ena, nthawi zambiri maluwa otchedwa ma buttercup amakhala ndi timasamba 5 pa duwa limodzi, ma bloodroot amakhala ndi timasamba 8, ma fireweed amakhala ndi timasamba 13, ma aster timasamba 21, ma daisy am’tchire timasamba 34, ndipo ma Michaelmas daisy amakhala ndi timasamba 55 kapena 89 pa duwa limodzi. (Onani chithunzi 6.) Zipatso ndi ndiwo zamasamba nthawi zambiri zimakhala ndi mbali zina zimene zimatsatira manambala a Fibonacci. Mwachitsanzo, nthochi mukaidula cham’lifupi mwake, nthawi zambiri imaoneka kuti ili ndi mbali zisanu.

“Chilichonse Anachikongoletsa”

Akatswiri odziwa zojambulajambula anadziwa kalekale kuti mbali za zomera zikamakula motsatira kupendekeka kwapadera kuja, m’pamene zimaoneka zokongola kwambiri. Kodi n’chiyani chimachititsa zomera kumamera mbali zatsopano motsatira kupendekeka kwapaderaku? Anthu ambiri amazindikira kuti ichi ndi chitsanzo chimodzi chokha chosonyeza kuti zinthu zamoyo zinachita kupangidwa mwanzeru.

Poona mmene zinthu zamoyo zinapangidwira mwaluso ndi mmene ifeyo timathera kusangalalira nazo, anthu ambiri amaona kuti zinachita kulengedwa ndi Mlengi amene amafuna kuti tisangalale ndi moyo. Ponena za Mlengi wathu, Baibulo limati: “Chinthu chilichonse anachikongoletsa pa mphindi yake.”—Mlaliki 3:11.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 N’zochititsa chidwi kuti mpendadzuwa amasiyana ndi maluwa ena ambiri chifukwa timaluwa take ting’onoting’ono timene timadzakhala nthanga timayamba kupanga mizere yoyenda mozungulira kuchokera m’mphepete mwa duwalo m’malo mochokera pakati.

[Zithunzi pamasamba 24, 25]

Chithunzi 1

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Chithunzi 2

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Chithunzi 3

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Chithunzi 4

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Chithunzi 5

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Chithunzi 6

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

[Chithunzi patsamba 24]

Mmene pomerera mbali zatsopano za chomera pamaonekera tikapaonera pafupi

[Mawu a Chithunzi]

R. Rutishauser, University of Zurich, Switzerland

[Mawu a Chithunzi patsamba 25]

White flower: Thomas G. Barnes @ USDA-NRCS PLANTS Database