Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Chisinthiko Chinachitikadi?

Kodi Chisinthiko Chinachitikadi?

Kodi Chisinthiko Chinachitikadi?

PULOFESA RICHARD DAWKINS, wasayansi wotchuka wokhulupirira chisinthiko, anati: “Zoti chisinthiko chinachitikadi n’zoona, monga momwe zilili zoona kuti dzuwa limatentha.” N’zoona kuti kafukufuku komanso zimene timaona zimatsimikizira kuti dzuwa ndi lotentha. Koma kodi njira zimenezi zimatsimikiziranso kuti chisinthiko chinachitikadi?

Tisanayankhe funso limenelo, tiyenera kufotokoza kaye zinthu zina. Asayansi ambiri aona kuti nthawi ikamapita zamoyo zimene zikubadwa zimatha kusintha pang’ono. Charles Darwin anati kusintha kumeneku ndi “kusintha kwapang’onopang’ono” kwa zinthu zamoyo. Kusintha koteroko anthu akuona kukuchitika, akusonyeza m’zotsatirapo za kafukufuku wawo, ndipo alimi a zomera ndi zinyama akugwiritsa ntchito kuti kuwathandize pa ulimi wawo. * Kusintha kumeneku tinganene kuti kumachitikadi. Komabe, asayansi akaona kusintha koteroko amakutcha “kusintha kochitika m’zamoyo za mtundu umodzi.” Ngakhale mawu omwe amafotokozera kusintha kumeneku akusonyeza zimene asayansi ambiri amakhulupirira, zoti kusintha kochitika m’zamoyo za mtundu umodzi kumeneku kumapereka umboni woti palinso kusintha kwina kosiyana kwambiri ndi kumeneku. Kusintha kwinako palibe amene anakuona, ndipo amakutcha kusintha kochoka ku mtundu wina wa chamoyo kupita ku mtundu wina.

Zoona zake n’zoti, Darwin anatchula zinthu zina zomwe n’zosiyana kwambiri ndi zinthu zomwe anthu amatha kuziona. M’buku lake lotchuka la The Origin of Species, iye analemba kuti: “Ndimaona zamoyo zonse osati monga zinthu zomwe zinachita kulengedwa mwapadera, koma monga ana a makolo ochepa oyambirira.” Darwin anati m’kupita kwa nthawi yaitali, “makolo ochepa oyambirira” amenewa, omwe amati ndi mitundu ya zamoyo zotsika kwambiri, anasintha pang’onopang’ono, mpaka kusanduka mitundu mamiliyoni angapo yosiyanasiyana ya zamoyo zomwe zili padziko lapansi. Anthu okhulupirira chisinthiko amati kusintha kwa pang’onopang’ono kumeneku kutaphatikizana kunapanga kusintha kwakukulu komwe kunachititsa kuti nsomba zisanduke zamoyo zotha kukhala m’madzi ndi pamtunda pomwe, ndi kuti anyani asanduke anthu. Kusintha kwakukulu kumeneku n’kumene amati ndiko kunachititsa kuti mtundu umodzi wachamoyo usinthire ku mtundu wina. Anthu ambiri amanena kuti kusintha kwachiwiriku n’kotheka ndithu. Iwo amaganiza kuti, ‘Ngati kusintha kwakung’ono kungachitike m’zamoyo za mtundu umodzi, kodi pali chimene chingalepheretse kuti m’kupita kwanthawi zinthu zisinthike kuchoka ku mtundu wina kupita ku winanso?’ *

Chiphunzitso cha kusintha kochoka ku mtundu wina wa chamoyo kupita ku mtundu wina chimadalira mfundo zazikulu zitatu:

1. Kusintha kwa maselo a zamoyo kumayambitsa mitundu yatsopano ya zamoyo. *

2. Kupulumuka kwa zamoyo zamphamvu zokhazokha kumayambitsa mitundu yatsopano ya zamoyo.

3. Zinthu zakufa zakale zomwe zapezedwa zimasonyeza kusintha kochoka ku mtundu wina wa zomera ndi zinyama kupita ku mtundu wina.

Kodi pali umboni wokwanira wotsimikizira kuti zamoyo zinasintha kuchoka ku mtundu wina kupita ku mtundu wina moti tinganene kuti kusintha kumeneku kunachitikadi?

Kodi Kusintha kwa Maselo Kungayambitse Mitundu Yatsopano ya Zamoyo?

Malangizo onena za chibadwa cha zomera kapena zinyama analembedwa pakatikati pa selo iliyonse ya chamoyocho. * Ochita kafukufuku atulukira kuti kusintha kwa malangizo okhudza chibadwa okhala m’maselo kukhoza kuchititsa kuti ana a zomera ndi zinyama akhale osiyaniranako ndi makolo awo. Mu 1946, Hermann J. Muller, amene anapatsidwapo mphoto yapamwamba ya Nobel ndiponso amene anayambitsa maphunziro okhudzana ndi chibadwa cha zinthu, anati: “Kusintha kochuluka kosachitikachitika kumeneku si kuli chabe chinthu chachikulu chimene chingatithandize kukhala ndi mitundu yabwinopo ya zinyama ndi zomera, komanso, tingangonena kuti n’kumene kunapangitsa chisinthiko cha zamoyo, pogwiritsa ntchito njira ya kupulumuka kwa zamoyo zamphamvu zokhazokha.”

Indedi, chiphunzitso cha kusintha kwa zamoyo kuchoka ku mtundu wina kupita ku mtundu wina chagona pa mfundo yoti kusintha kwa maselo kungayambitse osati kokha mitundu yatsopano ya zamoyo komanso magulu atsopano a zomera ndi zinyama. Kodi pali njira iliyonse yofufuzira zimenezi kuti tione ngati zilidi zoona? Poyamba, taganizirani zomwe anthu apeza atatha zaka pafupifupi 100 akuphunzira za chibadwa cha zamoyo.

M’zaka zakumapeto kwa m’ma 1930, asayansi anayamba kukhulupirira ndi mtima wonse kuti ngati anthu atamasankha okha zamoyo zamphamvu zokhazokha zomwe zasintha maselo, sangavutike kuyambitsa mitundu yatsopano ya zomera. Iwo anayamba kukhulupirira zimenezi poganiza kuti ngati kupulumuka kwa zamoyo zamphamvu zokhazokha kungayambitse mitundu yatsopano ya zamoyo chifukwa cha kusintha kwa maselo ake, ndiye kuti nawonso akhoza kuchita zimenezi. Wolf-Ekkehard Lönnig, wasayansi wina pa bungwe lobereketsa mitundu yosiyanasiyana ya zomera kuti apange mitundu ina la Max Planck Institute for Plant Breeding Research ku Germany amene anacheza ndi olemba Galamukani! anati: “Panali chiyembekezo chachikulu pakati pa akatswiri a sayansi ya zamoyo ndi akatswiri a sayansi ya chibadwa cha zamoyo ndi anthu oweta zamoyo kuti zitulutse mitundu yatsopano ya zamoyo.” N’chifukwa chiyani anali ndi chiyembekezo chachikulu? Lönnig, yemwe watha zaka 28 akuphunzira za kusintha kwa maselo a zomera, anati: “Ochita kafukufuku amenewa ankaganiza kuti tsopano nthawi yakwana yoti asinthe njira zomwe amagwiritsa ntchito pobereketsa zomera ndi zinyama. Ankaganiza kuti ngati atachititsa zomera ndi zinyama kusintha maselo awo, n’kumasankha zamoyo zimene zasintha bwino zokhazokha kuti ziberekane, akhoza kupanga zomera ndi zinyama zatsopano ndiponso zabwino koposa.” *

Asayansi ku United States, ku Asia, ndi ku Ulaya anapatsidwa ndalama zambiri zochitira kafukufuku amene angafulumizitse kusinthika kwa zamoyo, ndipo anayambadi kuchita kafukufukuyo. Patatha zaka zoposa 40 akuchita kafukufuku wotereyu, kodi zotsatirapo zake zinali zotani? Wochita kafukufuku wina dzina lake Peter von Sengbusch anati: “Ngakhale kuti anthu anawononga ndalama zambiri, zoyesayesa zawo zofuna kupanga mitundu yatsopano ya zomera ndi zinyama zobereka kwambiri poyesera kusintha maselo awo ndi mphamvu ya magetsi, zinalepherekeratu.” Lönnig anati: “Pofika m’ma 1980, chiyembekezo chimene asayansi anali nacho padziko lonse lapansi sichinaphule kanthu. Kubereketsa zamoyo posintha maselo awo, monga mbali yapadera ya kafukufuku, kunasiyika m’mayiko a Azungu. Pafupifupi zamoyo zonse zomwe anazisintha maselo zinafa kapena zinali zofooka poyerekezera ndi zomwe zinakula mwachibadwa.” *

Ngakhale ndi choncho, zomwe apeza pa zaka 100 zochita kafukufuku wa kusintha kwa maselo a zamoyo ndiponso zomwe apeza pa zaka 70 za kafukufuku wa njira zobereketsera zamoyo pozisintha maselo, zathandiza asayansi kudziwa ngati zamoyo zosinthidwa maselo zingayambitse mitundu yatsopano ya zamoyo. Ataona umboni womwe ulipo, Lönnig anati: “Zamoyo zosinthidwa maselo sizingasinthe mtundu woyambirira [wa chomera kapena chinyama] kuti ukhale mtundu wina. Mfundo imeneyi ikugwirizana ndi zotsatirapo zonse za kafukufuku wosintha maselo a zamoyo yemwe anachitika m’zaka za m’ma 1900, ndipo ikugwirizananso ndi malamulo a masamu enaake. Choncho lamulo loti zamoyo zimene zimabadwa zitasintha zimakhala zofanana ndi zina zimene zinabadwa zitasinthapo kale, likusonyeza kuti mitundu ya zamoyo ili ndi malire enieni amene sangathe kuchotsedwa kapena kuphwanyidwa chifukwa cha kusinthika kwangozi kwa maselo.”

Taganizirani tanthauzo la mfundo zimenezi. Ngati asayansi odziwa bwino ntchito yawo analephera kupanga mitundu yatsopano ya zamoyo mwa kupanga ndi kusankha zamoyo zosinthika maselo kuti apangire zamoyo zina zabwino, kodi m’pomveka kuti zimenezi zikhoza kungochitika zokha mwangozi? Ngati kafukufuku wasonyeza kuti kusintha kwa maselo a zamoyo sikungayambitse mtundu watsopano wa zamoyo, ndiye tinganene kuti kusintha kochoka ku mtundu wina wa chamoyo kupita ku mtundu wina kunachitika bwanji?

Kodi Kupulumuka kwa Zamoyo Zamphamvu Zokhazokha Kumayambitsa Mitundu Yatsopano ya Zamoyo?

Darwin ankakhulupirira kuti kupulumuka kwa zamoyo zamphamvu zokhazokha kungapangitse kuti mitundu ya zamoyo yogwirizana kwambiri ndi kumalo komwe ili ndi yomwe ingapitirirebe kukhala ndi moyo, pamene mitundu ina yosagwirizana ndi kumaloko pamapeto pake ingafe. Asayansi amakono okhulupirira chisinthiko amaphunzitsa kuti pamene mitundu ya zamoyo inayamba kufalikira n’kumakakhala ku malo awokha, kupulumuka kwa zamoyo zamphamvu zokhazokha n’kumene kunachititsa kuti zamoyo zisinthe mogwirizana kwambiri ndi kumalo kwawo kwatsopanoko. Okhulupirira chisinthikowa amati, chifukwa cha zimenezi, magulu a zamoyo okhala ku malo kwawokha amenewa kenaka anadzasanduka zamoyo za mtundu watsopano kotheratu.

Monga momwe tanenera kale, umboni wochokera ku kafukufuku ukusonyeza moonekeratu kuti kusintha kwa maselo a zamoyo sikungathe kuyambitsa mitundu yatsopano ya zomera kapena zinyama. Ngakhale ndi choncho, kodi okhulupirira chisinthiko amapereka umboni wotani kuti atsimikizire zonena zawo zoti kupulumuka kwa zamoyo zamphamvu zokhazokha kumachititsa zamoyo zokhazo zomwe maselo awo asintha bwino kuti zibereke mitundu yatsopano? Kabuku komwe kanafalitsidwa mu 1999 ndi bungwe la National Academy of Sciences (NAS) ku United States kamati: “Chitsanzo chabwino kwambiri cha kuyambika kwa mitundu yatsopano ya zamoyo ndicho mitundu 13 ya mbalame zomwe zinafufuzidwa ndi Darwin pa zilumba za Galápagos, zomwe panopa zimatchedwa mbalame za Darwin.”

M’ma 1970, gulu lochita kafukufuku lotsogoleredwa ndi Peter ndi Rosemary Grant linayamba kuphunzira za mbalame zimenezi ndipo linaona kuti patatha chaka chimodzi cha chilala, mbalame zomwe zinali ndi milomo yokulirapo zinapulumuka mosavuta poyerekezera ndi zomwe zinali ndi milomo yocheperapo. Popeza kukula ndi kaonekedwe ka milomoyo ndi njira imodzi yaikulu yosiyanitsira mitundu 13 ya mbalamezo, zomwe anapezazi anaziona kuti n’zofunika. Kabukuko kanapitiriza kuti: “Peter ndi Rosemary Grant akuganiza kuti ngati pa zilumbazi patamagwa chilala chaka chimodzi chilichonse pa zaka 10, ndiye kuti pomatha zaka 200 pakhoza kupangika mtundu watsopano wa mbalame.”

Komabe, kabuku ka bungwe la NAS kameneka sikanatchule mfundo zina zofunika zosagwirizana ndi mfundo zawozo. M’zaka zotsatira chilalacho, mbalame za milomo yocheperapo zinachulukanso kuposa za milomo yaikulu. Choncho Peter Grant ndi wophunzira wina wa pa koleji dzina lake Lisle Gibbs analemba m’magazini yasayansi yotchedwa Nature mu 1987, kuti anaona “kuti mbalamezo zinkasintha m’njira yosiyana ndi imene anali kuyembekezera.” Mu 1991, Grant analemba kuti mbalamezi zikumasintha nyengo ikasintha ndipo zikumabwereranso mwakale nyengo ikabwereranso mwakale. Ochita kafukufukuwo anaonanso kuti ina mwa mitundu yomwe ankaiona ngati yosiyana ya mbalamezo inkatha kukumana n’kubereka ana amene ankapulumuka bwino kwambiri kuposa makolo awo. Peter ndi Rosemary Grant anati ngati mitundu yosiyana ya mbalamezo idzapitirizabe kumabereka ana, zingadzachititse kuti mitundu iwiri ya mbalame idzakhale mtundu umodzi pomatha zaka 200.

Mu 1966, katswiri wina wa sayansi ya zamoyo wokhulupirira chisinthiko dzina lake George Christopher Williams analemba kuti: “Ndimaona kuti n’zomvetsa chisoni kuti chiphunzitso cha kupulumuka kwa zamoyo zamphamvu zokhazokha poyamba chinaphunzitsidwa kuti chisonyeze momwe chisinthiko chinachitikira. Ndikuona kuti zikanakhala bwino akanamachiphunzitsa pofotokoza momwe mitundu ya zamoyo imapitirizirabe kukhala ndi moyo ngakhale malo awo okhala akamasintha.” Katswiri wina wofotokoza za chisinthiko dzina lake Jeffrey Schwartz analemba mu 1999 kuti ngati zimene ananena Williams zili zoona, ndiye kuti kupulumuka kwa zamoyo zamphamvu zokhazokha kungakhale kukuthandiza zamoyo kusintha kuti zigwirizane ndi kusintha kwa malo awo okhala, koma “sikukupanga chinthu chilichonse chatsopano.”

Zoonadi, mbalame za Darwin sizikusinthika n’kukhala “chinthu chilichonse chatsopano.” M’malo mwake, izo zikadali mbalame za mtundu womwewo. Ndipo popeza mitundu yosiyana ya mbalamezi ikumatha kubereka ana, zikutipangitsa kukayikira njira zimene okhulupirira chisinthiko ena amagwiritsira ntchito pofuna kusonyeza kusiyana kwa mitundu ya zamoyo. Zikusonyezanso kuti ngakhale mabungwe odziwika bwino asayansi akhoza kufalitsa umboni m’njira yoti ugwirizane ndi zimene iwowo akukhulupirira.

Kodi Zinthu Zakufa Zakale Zomwe Zapezedwa Zikupereka Umboni wa Kusintha Kochoka ku Mtundu Wina wa Chamoyo Kupita ku Mtundu Wina?

Kabuku kofalitsidwa ndi bungwe la NAS komwe tinakatchula kale kaja kamapangitsa wowerenga kuganiza kuti zinthu zakufa zakale zomwe asayansi apeza zimasonyeza mokwanira kusintha kochoka ku mtundu wina wa chamoyo kupita ku mtundu wina. Kabukuko kamati: “Pali mitundu yambiri ya zamoyo yomwe yapezeka pakati pa nsomba ndi zamoyo zokhala m’madzi ndi pamtunda pomwe, pakati pa zamoyo zokhala m’madzi ndi pamtunda pomwe ndi zamoyo za m’gulu la njoka, pakati pa zamoyo za m’gulu la njoka ndi zamoyo zoyamwitsa, ndi pakati pa zamoyo za m’gulu la anyani moti nthawi zambiri zimavuta kudziwa kuti kodi kusintha kochoka ku mtundu umodzi wa chamoyo kufika ku mtundu wina kunachitika liti.”

Mawu olembedwa mopanda chikayikiro chilichonse amenewa ndi odabwitsa ndithu. Chifukwa chiyani? Mu 2004, magazini ya National Geographic inati zinthu zakufa zakale zomwe zapezedwa zili ngati “filimu yofotokoza za chisinthiko yomwe zithunzi 999 pa zithunzi zake 1000 zilizonse zasowa.” Kodi chithunzi chimodzi chilichonse chotsalacho chingasonyezedi motsimikizirika kuti zamoyo zinasinthika kuchoka ku mtundu wina wa chamoyo kupita ku mtundu wina? Kodi zinthu zakufa zakale zomwe zapezeka zimasonyeza chiyani kwenikweni? Niles Eldredge, yemwe amakhulupirira kwambiri chisinthiko, anavomereza kuti zinthu zakufa zakale zomwe apeza zikusonyeza kuti kwa nthawi yaitali, “pankakhala kusintha kochepa, kapenanso sipankakhala kusintha kulikonse m’mitundu yambiri ya zamoyo.”

Pofika panopa, asayansi padziko lonse lapansi afukula ndi kusunga zinthu zakufa zakale zikuluzikulu zokwana 200 miliyoni ndi mabiliyoni angapo a zinthu zakufa zing’onozing’ono. Ochita kafukufuku ambiri amavomereza kuti zinthu zakufa zakale zambirimbiri zomwe apezazi zimasonyeza kuti magulu onse akuluakulu a zinyama anakhalapo mwadzidzidzi ndipo sanasinthe kwambiri m’kupita kwa nthawi, ndipo mitundu yambiri ya zinyama inasowa mwadzidzidzi, mofanana ndi momwe inakhalirapo. Ataona umboni wa zinthu zakufa zakale zomwe zapezedwa, katswiri wina wa sayansi ya zamoyo dzina lake Jonathan Wells analemba kuti: “Tikaona magulu, magulu okulirapo, ndi magulu aakulu kwambiri a zamoyo, sitikuonapo kusintha kwapang’onopang’ono kuchokera kwa makolo ochepa akale. Tikaona umboni wa zinthu zakufa zakale zomwe zapezedwa, ndi tinthu ting’onoting’ono tomwe timapanga zamoyo, palibe umboni wokwanira wotsimikizira mfundo imeneyi.”

Kodi Chisinthiko Chinachitikadi Kapena Ndi Nkhani Yongopeka?

N’chifukwa chiyani anthu ambiri otchuka okhulupirira chisinthiko amalimbikira kunena kuti kusintha kochoka ku mtundu wina wa chamoyo kupita ku mtundu wina kunachitikadi? Atatsutsana ndi mfundo zina za Richard Dawkins, munthu wina wotchuka wokhulupirira chisinthiko dzina lake Richard Lewontin analemba kuti asayansi ambiri amakhala okonzeka kukhulupirira mfundo zasayansi zosemphana ndi zinthu zochita kuonekeratu “chifukwa choti tinavomereza kale kuti zinthu zinangopangika zokha popanda winawake amene anazipanga.” Asayansi ambiri amakaniratu kuganizira n’komwe zoti mwina kunja kuno kungakhale winawake wanzeru amene anapanga zinthu chifukwa choti, monga momwe Lewontin analembera, “sitifuna kuvomereza zoti Mulungu alipo.”

Pa nkhani imeneyi, katswiri wina wa chikhalidwe cha anthu dzina lake Rodney Stark anagwidwa mawu m’magazini ya Scientific American akunena kuti: “Papita zaka 200 zomwe takhala tikuuzidwa kuti ngati ukufuna kukhala munthu wasayansi uyenera kuchotsa m’maganizo mwako mfundo zilizonse zachipembedzo chifukwa zimalepheretsa munthu kuganiza momasuka.” Iye anapitiriza kunena kuti m’mayunivesite ochitira kafukufuku, “anthu opembedza amatseka pakamwa pawo,” pamene “anthu osapembedza amapondereza anzawowo.” Malinga ndi zomwe ananena Stark “m’maudindo akuluakulu [a sayansi], munthu amapatsidwa ulemu akakhala wosapembedza.”

Kuti muthe kukhulupirira chiphunzitso cha kusintha kochoka ku mtundu wina wa chamoyo kupita ku mtundu wina pali zinthu zingapo zimene muyenera kukhulupirira. Muyenera kukhulupirira kuti asayansi okhulupirira kuti kulibe Mulungu kapena okhulupirira kuti Mulungu alipo koma salowerera pa zochitika za anthu, sadzalola kuti zikhulupiriro zawozo zikhudze kaonedwe kawo ka umboni wasayansi womwe apeza. Muyeneranso kukhulupirira kuti kusintha kwa maselo a zamoyo ndi kupulumuka kwa zamoyo zamphamvu zokhazokha kunayambitsa mitundu yosiyanasiyana ya zamoyo, ngakhale kuti patatha zaka zoposa 100 akuchita kafukufuku wa kusintha kwa maselo, apeza kuti kusintha kwa maselo sikunasinthe ngakhale mtundu umodzi wokha wa chamoyo kuti ukhale mtundu wina watsopano. Ndipo muyenera kukhulupirira kuti zamoyo zonse zinasintha pang’onopang’ono kuchokera ku kholo limodzi, ngakhale kuti zinthu zakufa zakale zomwe apeza zimasonyeza moonekeratu kuti mitundu ikuluikulu ya zomera ndi zinyama inakhalapo mwadzidzidzi ndipo sinasinthe n’kusanduka zinthu zina, ngakhale patapita zaka zambiri. Kodi chikhulupiriro choterocho chagona pa zinthu zochitikadi kapena pa nkhani yongopeka?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Anthu oweta agalu akhoza kusankha galu wamwamuna ndi wamkazi oti abereke ana n’cholinga choti anawo adzakhale ndi miyendo ifupiifupi kapena tsitsi lalitali kusiyana ndi makolo awo. Komabe, kusintha kumene kumabwera chifukwa chobereketsa agalu nthawi zambiri kumachitika chifukwa chakuti maselo ena a agaluwo sanagwire ntchito yake. Mwachitsanzo, pali agalu enaake amene amakhala aang’ono kwambiri chifukwa choti minofu yawo yokhala pakati pa mafupa sikula bwinobwino, ndipo mapeto ake agaluwa amakhala ngati abathwa.

^ ndime 4 Ngakhale kuti mawu akuti “mtundu” agwiritsidwa ntchito kwambiri mu nkhani ino, tiyenera kutchulapo kuti mawu amenewa si ofanana tanthauzo lake ndi mawu akuti “mtundu” amene ali m’buku la m’Baibulo la Genesis. M’Baibulo mawu akuti “mtundu” amatanthauza zinthu za m’gulu limodzi zomwe zikhoza kukhala zosiyanasiyana. Nthawi zambiri, zimene asayansi amati ndi kusintha kwa mtundu wa chamoyo n’kupanga chamoyo china, kwenikweni kumangokhala kusiyanasiyana kwa zamoyo za mtundu umodzi, monga momwe mawuwa akugwiritsidwira ntchito mu nkhani ya mu Genesis.

^ ndime 6 Onani bokosi lakuti “Mmene Zinthu Zamoyo Zimagawidwira M’magulu.”

^ ndime 11 Kafukufuku wasonyeza kuti mbali yamadzimadzi ya selo, zikopa zake, ndi mbali zake zina nazonso zimathandizira kupanga chibadwa cha chamoyo.

^ ndime 13 Ndemanga za Lönnig mu nkhani ino ndi zakezake ndipo sizikuimira maganizo a bungwe la Max Planck Institute for Plant Breeding Research.

^ ndime 14 Kafukufuku wasonyeza kuti kusintha kumene kumachitika m’zamoyo za mtundu umodzi kumakhala kofananafanana ndipo zimati zikasinthasintha n’kufika nambala inayake, sizisinthanso ndipo nambala ya zamoyo zimene zikusintha imayamba kuchepa. Kuchokera ku zochitika zimenezi, Lönnig anakhazikitsa lamulo latsopano la sayansi lonena kuti “zamoyo zimene zimabadwa zitasintha zimakhala zofanana ndi zina zimene zinabadwa zitasinthapo kale.” Kuwonjezera apo, zomera zosinthika maselo zosakwana wani peresenti n’zimene anazisankha kuti achite nazo kafukufuku wowonjezera, ndipo pa gulu limeneli zomera zosakwana wani peresenti n’zomwe anazipeza kuti angazigwiritsedi ntchito pa ulimi weniweni. Zotsatirapo za kusintha maselo a zinyama zinali zoipa kwambiri kusiyananso ndi zomera, ndipo njirayi kenaka anangosiyiratu.

[Mawu Otsindika patsamba 15]

“Zamoyo zosinthidwa maselo sizingasinthe mtundu woyambirira [wa chomera kapena wa nyama] kuti ukhale mtundu wina”

[Mawu Otsindika patsamba 16]

Zimene tingaphunzire kuchokera ku mbalame za Darwin n’zakuti zamoyo zimatha kusintha pang’ono kuti zigwirizane ndi kusintha kwa nyengo

[Mawu Otsindika patsamba 17]

Zinthu zakufa zakale zikusonyeza kuti mitundu yonse ikuluikulu ya zinyama inakhalapo mwadzidzidzi ndipo sinasinthe kwambiri m’kupita kwa nthawi

[Tchati patsamba 14]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

MMENE ZINTHU ZAMOYO ZIMAGAWIDWIRA M’MAGULU

Zamoyo akamazigawa m’magulu, amayambira ku magulu okhala ndi zamoyo zochepa kumapita ku magulu okhala ndi zamoyo zamitundu yambiri. * Mwachitsanzo, tayerekezerani magulu a anthu ndi ntchentche omwe alembedwa pansipa.

ANTHU NTCHENTCHE

Mtundu anthu amakono ntchentche zodya zipatso

Mtundu Wokulirapo Anthu ntchetche zing’onozing’ono

Banja Anthu ndi anyani ntchentche

Banja Lokulirapo Nyama zoyamwitsa zoyenda Tizilombo touluka

ndi miyendo iwiri

Gulu Nyama zonse zoyamwitsa Tizilombo tonse

Gulu Lokulirapo Nyama zoyamwitsa Tizilimbo ndi nyama zina

ndi nyama zina

Gulu Lalikulu Nyama zonse nyama zonse

Kwambiri

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 48 Dziwani izi: Genesis chaputala 1 chimati zomera ndi zinyama zizidzaberekana “monga mwa mitundu yawo.” (Genesis 1:12, 21, 24, 25) Komabe, mawu a m’Baibulo akuti “mtundu” si mawu asayansi ndipo sayenera kusokonezedwa ndi mawu akuti “mtundu” amene asayansi amagwiritsa ntchito.

[Mawu a Chithunzi]

Tchatichi chatengedwa m’buku lotchedwa Icons of Evolution—Science or Myth? Why Much of What We Teach About Evolution Is Wrong, lolembedwa ndi Jonathan Wells

[Zithunzi patsamba 15]

Ntchentche yosinthika maselo (pamwambapo), ngakhale kuti ndi yopunduka, ndi ntchentchebe basi

[Mawu a Chithunzi]

© Dr. Jeremy Burgess/​Photo Researchers, Inc.

[Zithunzi patsamba 15]

Kafukufuku wasonyeza kuti kusintha kumene kumachitika m’zomera za mtundu umodzi kumakhala kofananafanana ndipo zimati zikasinthasintha n’kufika nambala inayake, sizisinthanso ndipo nambala ya zomera zimene zikusintha imayamba kuchepa (Chomera chimene chasintha n’chimene chili ndi maluwa okulirapo)

[Mawu a Chithunzi patsamba 13]

From a Photograph by Mrs. J. M. Cameron/​U.S. National Archives photo

[Mawu a Chithunzi patsamba 16]

Finch heads: © Dr. Jeremy Burgess/​Photo Researchers, Inc.

[Mawu a Chithunzi patsamba 17]

Dinosaur: © Pat Canova/​Index Stock Imagery; fossils: GOH CHAI HIN/​AFP/​Getty Images