Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Anagwiritsa Ntchito Chisinthiko Polenga Zamoyo?

Kodi Mulungu Anagwiritsa Ntchito Chisinthiko Polenga Zamoyo?

Kodi Mulungu Anagwiritsa Ntchito Chisinthiko Polenga Zamoyo?

“Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, nizinalengedwa.”—CHIVUMBULUTSO 4:11.

PATANGODUTSA nthawi yochepa Charles Darwin atafalitsa chiphunzitso chake cha chisinthiko, matchalitchi ambiri amene amati ndi achikristu anayamba kufunafuna njira zoti agwirizanitse chikhulupiriro chawo mwa Mulungu ndi chiphunzitso cha chisinthiko.

Masiku ano, magulu ambiri azipembedzo zachikristu akuoneka kuti akuvomereza zoti Mulungu anagwiritsa ntchito chisinthiko mwanjira inayake kuti alenge zamoyo. Ena amaphunzitsa kuti Mulungu anakonzeratu chilengedwe chonse kuti tinthu topanda moyo tidzasinthe n’kusanduka zinthu zamoyo, zomwe zinapitiriza kusintha mpaka kukhala anthu. Anthu amene amakhulupirira chiphunzitso chimenechi amati Mulungu sanalowerereponso chisinthiko chitayamba. Ena amaganiza kuti Mulungu analola chisinthiko kuyambitsa chokha mitundu yambiri ya zomera ndi zinyama, ndipo nthawi ndi nthawi ankalowererapo kuti zinthu zipitirizebe kusinthika.

Kodi N’zotheka Kuphatikiza Ziphunzitso za M’Baibulo ndi Chisinthiko?

Kodi chiphunzitso cha chisinthiko n’chogwirizanadi ndi zimene Baibulo limaphunzitsa? Chisinthiko chikanakhala chiphunzitso choona, nkhani ya m’Baibulo yonena za kulengedwa kwa munthu woyamba, Adamu, ikanangokhala nkhani yophunzitsa makhalidwe abwino basi, osati yeniyeni. (Genesis 1:26, 27; 2:18-24) Kodi mmenemo ndi mmene Yesu ankaionera nkhani ya m’Baibulo imeneyi? Yesu anati: “Kodi simunawerenga kuti iye amene adalenga anthu pachiyambi, anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi, nati, Chifukwa cha ichi mwamuna adzasiya atate wake ndi amake, nadzaphatikizana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi? Chotero kuti salinso awiri koma thupi limodzi. Chifukwa chake ichi chimene Mulungu anachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.”—Mateyu 19:4-6.

Pano Yesu ankakamba nkhani yonena za kulengedwa kwa anthu yofotokozedwa mu chaputala chachiwiri cha Genesis. Ngati Yesu ankaona kuti nkhani ya ukwati woyambirira inali yongopeka, kodi akanaitchula kuti atsimikizire zimene ankaphunzitsa zokhudza kupatulika kwa ukwati? Ayi. Yesu anatchula nkhaniyi chifukwa ankadziwa kuti inachitikadi.—Yohane 17:17.

Ophunzira a Yesu nawonso ankakhulupirira nkhani yonena za kulengedwa kwa zinthu ya mu Genesis. Mwachitsanzo, Uthenga Wabwino wa Luka umalondoloza mibadwo ya Yesu ndi makolo ake mpaka kukafika pa Adamu. (Luka 3:23-38) Ngati Adamu ndi munthu wongopeka chabe, kodi m’ndandanda wa mibadwo ya anthu umenewu unayambira pati kunena za anthu enieni? Ngati anthu a koyambirira kwa m’ndandanda wa mibadwo ya anthuwu anali ongopeka, kodi zimenezi zikanatsimikizira bwanji zimene Yesu ankanena zoti iye ndi Mesiya, wobadwira m’banja la Davide? (Mateyu 1:1) Luka, amene analemba nawo Uthenga Wabwino, anati ‘analondalonda mosamalitsa zinthu zonse kuyambira pachiyambi.’ N’zachionekere kuti iye ankakhulupirira nkhani ya mu Genesis yonena za kulengedwa kwa zinthu.—Luka 1:3.

Chikhulupiriro cha mtumwi Paulo mwa Yesu chinali chogwirizana ndi kukhulupirira kwake nkhani ya mu Genesis. Iye analemba kuti: “Pakuti monga imfa inadza mwa munthu, kuuka kwa akufa kunadzanso mwa munthu. Pakuti monga mwa Adamu onse amwalira, choteronso mwa Kristu onse akhalitsidwa ndi moyo.” (1 Akorinto 15:21, 22) Ngati Adamu sanalidi tate wa anthu onse, amene kudzera mwa iye “uchimo unalowa m’dziko lapansi . . . ndi imfa mwa uchimo,” kodi Yesu akanafunikira kufa kuti afafanize zotsatirapo za uchimo wotengera kwa Adamu?—Aroma 5:12; 6:23.

Kutsutsa chikhulupiriro cha nkhani ya kulengedwa kwa zinthu ya mu Genesis n’chimodzimodzi n’kutsutsa maziko enieni a Chikristu. Chiphunzitso cha chisinthiko n’chosemphana ndi ziphunzitso za Kristu. Kuyesayesa kulikonse kophatikiza ziphunzitso ziwirizi kumabweretsa chikhulupiriro chofooka chomwe chimakhala ‘chogwedezekagwedezeka, chotengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso.’—Aefeso 4:14.

Chikhulupiriro Chokhala ndi Maziko Olimba

Kwa zaka zambiri, Baibulo lakhala likutsutsidwa ndi kuukiridwa, koma nthawi zonse lapezeka kuti ndi loona. Paliponse pomwe Baibulo latchulapo nkhani zokhudza mbiri yakale, thanzi la anthu, ndi sayansi, nkhani zake zimakhala zodalirika. Malangizo ake onena za momwe tingakhalire ndi anthu ena n’ngodalirika ndiponso amagwira ntchito nthawi ina iliyonse. Nzeru ndi ziphunzitso za anthu, mofanana ndi udzu wobiriwira, zimakula kenaka n’kufota pakapita nthawi, koma Mawu a Mulungu “adzakhala nthawi zachikhalire.”—Yesaya 40:8.

Chiphunzitso cha chisinthiko chimakhudza zambiri, osati sayansi yokha. Chiphunzitsochi chinayambira ku maganizo a anthu omwe anayamba pang’onopang’ono, n’kukhazikika patapita zaka zambiri. Koma m’zaka zaposachedwapa, ngakhale chiphunzitso chofala cha Darwin nachonso chakhala chikusintha kwambiri, makamaka chifukwa chakuti akhala akumachiyerekezera ndi umboni womwe ukuchulukirachulukira wosonyeza kuti zinthu zamoyo zinapangidwa mwaluso. Tikukupemphani kuti muonenso mfundo zina zokhudzana ndi nkhani imeneyi. Mungatero mwa kuwerenga nkhani zina zomwe zili m’magazini ino. Mukhozanso kuwerenga mabuku amene asonyezedwa pa tsamba lino ndi pa tsamba 32.

Sitikukayikira kuti mukaifufuza bwinobwino nkhaniyi, chikhulupiriro chanu cha zimene Baibulo limanena zokhudza zomwe zinachitika kale chidzalimba. Ndipo chikhulupiriro chanu cha malonjezo a m’Baibulo onena za m’tsogolo chidzakula. (Ahebri 11:1) Mungafikenso mpaka pofuna kulemekeza Yehova, “amene analenga zakumwamba ndi dziko lapansi.”—Sal. 146:6.

ZOWERENGA ZINA

Buku la Anthu Onse Zitsanzo zosonyeza kuti Baibulo ndi lodalirika zafotokozedwa m’kabuku kameneka

Is There a Creator Who Cares About You? Onaninso umboni wina wasayansi ndi kudziwa chifukwa chomwe Mulungu wachikondi angalolere kuti anthu azivutika ngati momwe akuvutikira masiku ano

Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Funso lakuti, Kodi Mulungu Ali Nalo Cholinga Chotani Dziko Lapansili? layankhidwa m’mutu wachitatu wa buku limeneli

[Mawu Otsindika patsamba 10]

Yesu ankakhulupirira nkhani ya mu Genesis yonena za kulengedwa kwa zinthu. Kodi analakwitsa?

[Bokosi patsamba 9]

KODI CHISINTHIKO N’CHIYANI?

Tanthauzo limodzi la “chisinthiko” ndi: “Kusintha kwa zinthu mwanjira inayake.” Komabe, mawuwa amagwiritsidwa ntchito m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, amagwiritsidwanso ntchito kutanthauza kusintha kwakukulu kwa zinthu zopanda moyo, kapena kuti kupangika kwa chilengedwe chonse. Komanso, mawuwa amagwiritsidwa ntchito kutanthauza kusintha kwakung’ono kwa zinthu zamoyo, kapena kuti njira imene zomera ndi zinyama zimasinthira, malo amene zikukhala akamasinthanso. Koma mawuwa amagwiritsidwa ntchito kwambiri kutanthauza chiphunzitso chimene chimati moyo unachokera ku tinthu ting’onoting’ono topanda moyo, timene tinasintha n’kukhala maselo otha kuchulukana, ndipo pang’ono ndi pang’ono maselowa anasanduka zinthu zamoyo zochititsa kaso. Potsirizira pake anthu ndi amene anakhala anzeru kwambiri pa zamoyo zonse. Tanthauzo lachitatuli n’limene mawu oti “chisinthiko” akuimira mu nkhani ino.

[Mawu a Chithunzi patsamba 10]

Space photo: J. Hester and P. Scowen (AZ State Univ.), NASA