Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

KODI CHOLAKWIKA N’CHIYANI NDI CHITHUNZI ICHI?

Pezani zinthu zitatu zimene sizikugwirizana ndi nkhani ya m’Baibulo ya pa Genesis 3:1-5.

1. ․․․․․

2. ․․․․․

3. ․․․․․

Kambiranani: Kodi n’chifukwa chiyani Yehova anauza Adamu ndi Hava kuti asadye za mumtengo wodziwitsa zabwino ndi zoipa? N’chifukwa chiyani mukuganiza kuti kumvera malamulo a Yehova n’kofunika?

ZINACHITIKA LITI?

Lembani mzere kulumikiza zinthu zolengedwa ndi tsiku limene zinayamba kulengedwa.

Tsiku loyamba Tsiku lachiwiri Tsiku lachitatu Tsiku lachinayi Tsiku lachisanu Tsiku la sikisi Tsiku la seveni

4. Genesis 1:14-16

5. Genesis 1:24

6. Genesis 1:20, 21

NDINE NDANI?

7. Ndimadziwika kuti ndine munthu woyamba kumanga mzinda.

NDINE NDANI?

8. Ndine mkazi woyamba kutchulidwa dzina m’Baibulo pambuyo pa Hava.

KUCHOKERA M’MAGAZINI INO

Yankhani mafunso awa, ndipo lembani lemba kapena malemba a m’Baibulo omwe akusowapo.

Tsamba 9 N’chifukwa chiyani Yehova ali woyenera kumupatsa ulemu? (Chivumbulutso 4:․․․)

Tsamba 20 Nzeru zotsogola zomwe zimaonekera mu Genesis ndi umboni wa chiyani? (2 Timoteo 3:․․․)

Tsamba 25 Kodi zinthu zonse anazitani “pa mphindi yake”? (Mlaliki 3:․․․)

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Kodi mungathe kupeza zithunzi izi m’magazini ino? M’mawu anuanu, fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

(Mayankho ali pa tsamba 12)

MAYANKHO A MAFUNSO A PA TSAMBA 31

1. Njoka inalankhula ndi Hava, osati Adamu.—Genesis 3:1.

2. Adamu ndi Hava asanathamangitsidwe m’munda wa Edene analibe ana.—Genesis 4:1.

3. Adamu ndi Hava ankakhala maliseche nthawi imene anali m’mundamo.—Genesis 2:25.

4. Tsiku lachinayi.—Genesis 1:14-16, 19.

5. Tsiku la sikisi.—Genesis 1:24, 31.

6. Tsiku lachisanu.—Genesis 1:20, 21, 23.

7. Kaini.—Genesis 4:17.

8. Ada.—Genesis 4:19.

[Mawu a Chithunzi patsamba 31]

First circle: Breck P. Kent; second circle: © Pat Canova/​Index Stock Imagery