Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Muyenera Kukhulupirira Ndani?

Kodi Muyenera Kukhulupirira Ndani?

Kodi Muyenera Kukhulupirira Ndani?

“Pakuti nyumba ili yonse ili naye wina woimanga; koma wozimanga zonse ndiye Mulungu.”—AHEBRI 3:4.

KODI mukugwirizana ndi zomwe ananena wolemba Baibulo ameneyu? Patha zaka pafupifupi 2,000 kuchokera pamene vesi limenelo linalembedwa ndipo anthu apita patsogolo kwambiri mwasayansi. Kodi alipo anthu amene akukhulupirirabe kuti kupangidwa mwaluso kwa zinthu zamoyo kumasonyeza kuti pali Mlengi amene anazipanga, kapena kuti Mulungu?

Ngakhale m’mayiko otukuka anthu ambiri angayankhe kuti inde. Mwachitsanzo, ku United States, pa kafukufuku amene a magazini ya Newsweek anachita mu 2005, anapeza kuti anthu 80 pa anthu 100 alionse “amakhulupirira kuti Mulungu analenga chilengedwe chonse.” Kodi anthuwa amakhulupirira zimenezi chifukwa choti ndi osaphunzira? Mwachitsanzo, kodi pali asayansi alionse amene amakhulupirira kuti kuli Mulungu? Magazini yotchedwa Nature inanenapo mu 1997 kuti pafupifupi akatswiri 40 pa akatswiri 100 alionse a sayansi ya zinthu zamoyo, sayansi ya kapangidwe ka zinthu, ndi masamu, amene anafunsidwa mafunso pa kafukufuku wina, amakhulupirira kuti Mulungu alipo komanso amamvetsera ndi kuyankha mapemphero.

Komabe, asayansi ena amatsutsa kwambiri zimenezi. Dr. Herbert A. Hauptman, amene anapatsidwapo mphoto yapamwamba ya Nobel, posachedwapa anauza asayansi pa msonkhano kuti kukhulupirira zinthu zauzimu, makamaka kukhulupirira kuti kuli Mulungu, n’kosemphana ndi sayansi yabwino. Iye anati “chikhulupiriro choterechi chimasokoneza anthu.” Ngakhale asayansi amene amakhulupirira kuti kuli Mulungu sakonda kuphunzitsa kuti kupangidwa mwaluso kwa zomera ndi zinyama kumasonyeza kuti pali winawake amene anazipanga. Chifukwa chiyani? Pofotokoza chifukwa chimodzi, Douglas H. Erwin, katswiri wa sayansi ya zinthu zakufa zakale wogwira ntchito pa bungwe lasayansi lotchedwa Smithsonian Institute, anati: “Lamulo limodzi pa sayansi n’loti sitivomereza zozizwitsa.”

Mukhoza kulola kuti anthu ena azikuuzani zinthu zoti muganize ndi kukhulupirira. Kapena mungafufuze nokha umboni womwe ulipo kuti mudziwe zoona zake zenizeni. Pamene mukuwerenga za zinthu zatsopano zomwe asayansi atulukira m’masamba otsatirawa, dzifunseni kuti, ‘Kodi n’chinthu chanzeru kukhulupirira kuti Mlengi alipo?’

[Mawu Otsindika patsamba 3]

Fufuzani nokha umboni umene ulipo

[Bokosi patsamba 3]

KODI MBONI ZA YEHOVA ZIMAKHULUPIRIRA KUTI DZIKO LINALENGEDWA M’MASIKU SIKISI ENIENI?

Mboni za Yehova zimakhulupirira nkhani yonena za kulengedwa kwa zinthu monga mmene yalembedwera m’buku la m’Baibulo la Genesis. Komabe, Mboni za Yehova sizili m’gulu la anthu amene amakhulupirira kuti dziko linalengedwa m’masiku sikisi enieni. Chifukwa chiyani? Choyamba, anthu ambiri amene amakhulupirira zimenezi amati chilengedwe chonse ndi dziko lapansi ndi zamoyo zonse zinalengedwa m’masiku sikisi a maola 24, zaka pafupifupi 10,000 zapitazo. Koma zimenezi si zimene Baibulo limaphunzitsa. * Komanso, anthu okhulupirira kuti dziko linalengedwa m’masiku sikisi enieni amakhulupirira zinthu zinanso zambiri zimene sizigwirizana ndi zimene Baibulo limanena. Ziphunzitso zonse za Mboni za Yehova zimachokera m’Mawu a Mulungu basi.

Komanso, m’mayiko ena, anthu amene amakhulupirira kuti dziko lapansi linalengedwa m’masiku sikisi enieni amakhala m’magulu a anthu oumirira pa nkhani zachipembedzo, amene amatenga nawo mbali pa ndale. Magulu amenewa amafuna kukakamiza andale, oweruza, ndi aphunzitsi kuti akhazikitse malamulo ndi ziphunzitso zimene zimagwirizana ndi ziphunzitso zawo zachipembedzo.

Mboni za Yehova sizilowerera pa nkhani za ndale. Zimalemekeza ufulu wa maboma wopanga malamulo ndi kuonetsetsa kuti malamulowo akutsatiridwa. (Aroma 13:1-7) Komabe, izo zimamvera mawu a Yesu oti “siali a dziko lapansi.” (Yohane 17:14-16) Zikamagwira ntchito yawo yolalikira, zimapatsa anthu mwayi wophunzira za ubwino wotsatira mfundo za Mulungu pa moyo wawo. Koma siziphwanya mfundo zachikristu zoletsa kulowa ndale, mwa kuthandiza nawo magulu oumirira pa nkhani zachipembedzo. Magulu amenewa amayesetsa kukhazikitsa malamulo amene angakakamize anthu ena kuyamba kutsatira mfundo za m’Baibulo.—Yohane 18:36.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Onani nkhani yakuti, “Zimene Baibulo Limanena: Kodi Sayansi Imatsutsana ndi Nkhani ya mu Genesis?” imene ili pa tsamba 18 m’magazini ino