Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingafotokoze Bwanji Zimene Ndimakhulupirira Zokhudza Chilengedwe?

Kodi Ndingafotokoze Bwanji Zimene Ndimakhulupirira Zokhudza Chilengedwe?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndingafotokoze Bwanji Zimene Ndimakhulupirira Zokhudza Chilengedwe?

“Nkhani ya chisinthiko itafotokozedwa m’kalasi, inatsutsana ndi zonse zimene ndinali n’taphunzitsidwa. Inafotokozedwa ngati yoona, ndipo zimenezo zinandisokoneza maganizo.”—Anatero Ryan, wa zaka 18.

“Pamene ndinali ndi zaka pafupifupi 12, aphunzitsi anga ankakhulupirira kwambiri chisinthiko. Mpaka anaika chizindikiro cha Darwin pa galimoto yawo! Zimenezi zinandichititsa kuti ndiziopa kulankhula za chikhulupiriro changa choti zinthu zinachita kulengedwa.”—Anatero Tyler, wa zaka 19.

“Ndinachita mantha kwambiri aphunzitsi athu a sayansi atanena kuti phunziro lathu lotsatira lidzakhala la chisinthiko. Ndinadziwa kuti ndidzafunikira kufotokoza m’kalasi maganizo anga pa nkhani yovutayi.”—Anatero Raquel, wa zaka 14.

MWINA nanunso, mofanana ndi Ryan, Tyler, ndi Raquel, mumasowa mtendere nkhani ya chisinthiko ikayamba kukambidwa m’kalasi. Mumakhulupirira kuti Mulungu ‘adalenga zonse.’ (Chivumbulutso 4:11) Mumaona paliponse umboni woti zinthu zinachita kupangidwa mwanzeru. Koma mabuku a kusukulu amati tinachita kusintha, ndipo aphunzitsi anunso amanena zomwezo. Kodi inu ndinu ndani kuti muzitsutsana ndi anthu amene amati ndi akatswiri? Ndipo kodi anzanu a m’kalasi adzakuonani bwanji mukayamba kulankhula za . . . Mulungu?

Ngati mafunso oterewa akukudetsani nkhawa, khazikani mtima pansi! Si inu nokha amene mumakhulupirira kuti zinthu zinachita kulengedwa. Zoona zake n’zoti, ngakhale asayansi ena savomereza chiphunzitso cha chisinthiko. Aphunzitsi ambiri nawonso savomereza zimenezi. Ku United States, ana asukulu ambiri, okwana anayi pa asanu alionse, amakhulupirira kuti Mlengi alipo, ngakhale kuti mabuku amanena zina!

Komabe, mungafunse kuti, ‘Kodi ndidzanena chiyani pofotokozera ena kuti ndimakhulupirira kuti zinthu zinachita kulengedwa?’ Dziwani kuti ngakhale mutakhala ndi mantha, mukhoza kufotokoza zikhulupiriro zanu bwinobwino. Komabe, mufunikira kukonzekera.

Yesani Chikhulupiriro Chanu!

Ngati mukuleredwa ndi makolo achikristu, mukhoza kukhulupirira kuti zinthu zinachita kulengedwa kokha chifukwa choti zimenezi n’zimene mwaphunzitsidwa. Komabe, panopa pamene mukukula, muyenera kulambira Mulungu ndi “luntha la kulingalira,” n’kukhala ndi maziko olimba a chikhulupiriro chanu. (Aroma 12:1, NW) Paulo analimbikitsa Akristu oyambirira kuti ‘ayese zonse.’ (1 Atesalonika 5:21) Kodi inu mungachite bwanji zimenezi pankhani yoti zinthu zinachita kulengedwa?

Choyamba, taganizirani zimene Paulo analemba zokhudza Mulungu. Iye anati: “Chilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zake . . . popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa.” (Aroma 1:20) Poganizira mawu amenewo, taganizirani za thupi la munthu, dziko lapansi, chilengedwe chonsechi, ndi zinthu za m’nyanja za mchere. Ganizirani zodabwitsa za tizilombo, zomera, ndi zinyama, inde, zilizonse zimene zimakuchititsani chidwi inuyo. Ndiyeno, pogwiritsa ntchito “luntha la kulingalira,” dzifunseni kuti, ‘Kodi n’chiyani chimanditsimikizira kuti Mlengi alipo?’

Kuti ayankhe funso limeneli, Sam, wa zaka 14, amagwiritsa ntchito chitsanzo cha thupi la munthu. Iye anati: “Thupi la munthu lili ndi zigawo zambirimbiri zovuta kuzimvetsa, ndipo mbali zake zonse zimagwira bwino ntchito mogwirizana. Thupi la munthu silikanangosinthika lokha!” Holly, wa zaka 16, akuvomereza zimenezi. Iye anati: “Kuyambira pamene anandipeza ndi matenda a shuga, ndaphunzira zambiri za momwe thupi limagwirira ntchito. Mwachitsanzo, n’zochititsa chidwi kuti kapamba, yemwe ndi kachiwalo kakang’ono komwe kali kuseri kwa chifu, amagwira ntchito yaikulu kwambiri pothandiza magazi ndi ziwalo zina kugwira bwino ntchito.”

Achinyamata ena amaionera mwina nkhaniyi. Jared, wa zaka 19 anati: “Kwa ine, umboni waukulu ndi woti timafuna kulambira, komanso timatha kuzindikira kukongola kwa chinthu ndiponso tili ndi mtima wofuna kuphunzira. Tikatengera pa chiphunzitso cha chisinthiko, makhalidwe amenewa si ofunikira kuti munthu apitirizebe kukhala ndi moyo. Mfundo yokhayo imene ili yomveka kwa ine ndi yoti tinaikidwa pa dziko pano ndi winawake amene ankafuna kuti tisangalale ndi moyo.” Tyler, amene tinamutchula koyambirira kuja, anafikanso pa mfundo yofanana ndi imeneyo. Iye anati: “Ndikaganizira ntchito imene zomera zimagwira kuti moyo uzipitirirabe ndi kapangidwe kake kovuta kumvetsa, zimanditsimikizira kuti Mlengi alipo.”

N’zosavuta kunena za chilengedwe ngati mwaiganizira bwinobwino nkhaniyo ndipo yakufikanidi pamtima. Choncho, mofanana ndi Sam, Holly, Jared, ndi Tyler, patulani nthawi yoganizira zodabwitsa za chilengedwe cha Mulungu. Mukhale ngati mukumva zimene chilengedwechi chikukuuzani. Mosakayikira, mudzafika pa mfundo yofanana ndi imene mtumwi Paulo anafikapo, yoti, ‘zinthu zolengedwa zatithandiza kuzindikira bwino’ osati kokha zoti Mulungu alipo, komanso makhalidwe ake. *

Dziwani Zimene Baibulo Limaphunzitsa Kwenikweni

Kuwonjezera pa kuganizira mozama zinthu zimene Mulungu wapanga, kuti muthe kufotokoza bwino zifukwa zimene mumakhulupirira kuti zinthu zinachita kulengedwa muyeneranso kudziwa zimene Baibulo limaphunzitsa kwenikweni pa nkhaniyi. Palibe chifukwa chotsutsirana ndi munthu wina pa zinthu zimene Baibulo silizitchula mwachindunji. Taganizirani zitsanzo zingapo.

Buku langa la sayansi limati dziko lapansi, mapulaneti ena, ndi dzuwa zakhalako kwa zaka mabiliyoni angapo. Baibulo silinenapo zoti dziko lapansi, mapulaneti ena, ndi dzuwa zakhalapo kwa nthawi yaitali bwanji. Ndipotu, zimene Baibulo limanena n’zogwirizana ndi mfundo yoti chilengedwe chonse chinakhalapo kwa zaka mabiliyoni angapo, tsiku loyamba la kulenga lisanayambe.—Genesis 1:1, 2.

Aphunzitsi anga akuti dziko silikanatheka kulengedwa m’masiku sikisi okha. Baibulo silinena kuti tsiku lililonse la masiku sikisi a kulenga linali la maola 24 enieni. Kuti mumve zambiri, onani masamba 18-20 a magazini ino.

M’kalasi mwathu tinakambirana zitsanzo zingapo za mmene zinyama ndi anthu asinthira m’kupita kwa nthawi. Baibulo limati Mulungu analenga zamoyo “mwa mitundu yawo.” (Genesis 1:20, 21) Siligwirizana ndi mfundo yoti moyo unachokera ku zinthu zopanda moyo kapena kuti Mulungu anayambitsa chisinthiko ndi selo limodzi lokha. Komabe, zinthu za mu “mtundu” uliwonse zikhoza kusintha kwambiri. Choncho zimene Baibulo limanena zikugwirizana ndi mfundo yoti kusintha kukhoza kuchitika pakati pa zinthu za “mtundu” uliwonse.

Khalani Otsimikiza za Zimene Mumakhulupirira!

Palibe chifukwa chosowera mtendere kapena kuchita manyazi chifukwa choti mumakhulupirira kuti zinthu zinachita kulengedwa. Poona umboni umene ulipo, n’zanzeru, inde, zogwirizana ndi sayansi, kukhulupirira kuti tinachita kupangidwa ndi winawake wanzeru. Tikaganizira mfundo zonse, chisinthiko, osati chilengedwe, n’chimene chimafuna kuti mukhale ndi chikhulupiriro chachikulu popanda umboni ndiponso muzikhulupirira zozizwitsa zochitika popanda wozichititsa. Ndipotu, mukawerenga nkhani zina za m’magazini ino ya Galamukani! mosakayikira muona kuti umboni umene ulipo ukugwirizana ndi mfundo yoti zinthu zinachita kulengedwa. Ndipo mukaganizira mozama nkhaniyo pogwiritsa ntchito luntha lanu la kulingalira, mudzakhala otsimikiza kwambiri pofotokozera ena m’kalasi mwanu kuti mumakhulupirira kuti zinthu zinachita kulengedwa.

Zimenezi n’zimene Raquel, amene tinamutchula kale uja, anapeza. Iye anati: “Zinanditengera masiku angapo kuti ndizindikire kuti sindiyenera kubisa zikhulupiriro zanga. Ndinapatsa aphunzitsi anga buku lakuti Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? nditalemba mizere kunsi kwa mbali zina zimene ndinkafuna kuti aziwerenge. Kenaka, anadzandiuza kuti bukulo linawachititsa kuganiziranso nkhani ya chisinthiko mwa njira ina yatsopano ndi kuti m’tsogolo, adzagwiritsira ntchito mfundo zimene zili m’bukulo akamadzaphunzitsa nkhani imeneyi!”

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Achinyamata ambiri apindula atawerenga mfundo zomwe zafotokozedwa m’mabuku achingelezi akuti, Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? ndi Is There a Creator Who Cares About You? Mabuku awiri onsewa ndi ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

ZOTI MUGANIZIRE

▪ Kodi ndi njira zina ziti zimene mungafotokozere momasuka kusukulu chikhulupiriro chanu choti zinthu zinachita kulengedwa?

▪ Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumathokoza amene analenga zinthu zonse?—Machitidwe 17:26, 27.

[Bokosi patsamba 27]

“PALI UMBONI WOCHULUKA”

“Kodi munganene chiyani kwa wachinyamata amene anakula akuphunzitsidwa kukhulupirira kuti kuli Mlengi koma tsopano akuphunzitsidwa chisinthiko ku sukulu?” Funso limeneli linafunsidwa kwa katswiri wina wa sayansi ya zinthu zamoyo yemwe ndi wa Mboni za Yehova. Kodi anayankha bwanji? Anati: “Muziona umenewu ngati mwayi woti mudzitsimikizire kuti Mulungu alipo, osati chifukwa choti zimenezo n’zimene munaphunzitsidwa ndi makolo anu, koma chifukwa choti inuyo mwafufuza umboni umene ulipo ndipo mwafika potsimikizira mfundo imeneyo. Nthawi zina aphunzitsi akafunsidwa kuti ‘asonyeze’ kuti chisinthiko chinachitikadi, amaona kuti sangathe kutero, ndipo amazindikira kuti amavomereza chiphunzitsocho chifukwa choti n’chimene anaphunzitsidwa basi. Inunso mukhoza kugwa mu msampha womwewo pankhani yokhulupirira kuti Mlengi alipo. N’chifukwa chake m’pofunika kwambiri kuti mudzitsimikizire nokha kuti Mulungu alipodi. Pali umboni wochuluka wosonyeza zimenezi. Si wovuta kupeza.”

[Bokosi/Chithunzi patsamba 28]

KODI N’CHIYANI CHIMAKUTSIMIKIZIRANI INUYO?

Pansipa, lembani zinthu zitatu zimene zimakutsimikizirani inuyo kuti kuli Mlengi:

1. ․․․․․

2. ․․․․․

3. ․․․․․