Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Sayansi Imatsutsana ndi Nkhani ya mu Genesis?

Kodi Sayansi Imatsutsana ndi Nkhani ya mu Genesis?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Sayansi Imatsutsana ndi Nkhani ya mu Genesis?

ANTHU ambiri amati sayansi imatsutsana ndi nkhani ya m’Baibulo ya momwe zinthu zinalengedwera. Koma kutsutsana kwenikweni kuli pakati pa sayansi ndi maganizo a magulu a Akristu oumirira zinthu pa nkhani zachipembedzo, osati ndi Baibulo. Ena mwa magulu amenewa amanena zinthu zomwe si zoona, zoti malinga ndi Baibulo, zinthu zonse m’chilengedwe zinalengedwa m’masiku sikisi a maola 24 tsiku lililonse, zaka pafupifupi 10,000 zapitazo.

Koma Baibulo siligwirizana ndi maganizo amenewo. Likanakhala kuti limagwirizana nawo, ndiye kuti zinthu zambiri zimene asayansi atulukira pa zaka mahandiredi angapo zapitazi bwenzi zikutsutsanadi ndi Baibulo. Kuwerenga bwino zimene Baibulo limanena kumasonyeza kuti palibe kutsutsana kulikonse ndi mfundo zimene asayansi atulukira. Pa chifukwa chimenechi, Mboni za Yehova zimatsutsana ndi Akristu oumirira pa nkhani zachipembedzo ndi anthu ambiri amene amati dziko lapansi linalengedwa m’masiku sikisi enieni. Mfundo zotsatirazi zikusonyeza zimene Baibulo limaphunzitsa kwenikweni.

Kodi Mawu Akuti “Pachiyambi” Amatanthauza Chiyani?

Nkhani ya mu Genesis imayamba ndi mawu osavuta kumvetsa koma amphamvu akuti: “Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.” (Genesis 1:1) Akatswiri a Baibulo amagwirizana pa mfundo yakuti vesi limeneli likunena za chochitika chosiyana ndi masiku a kulenga ofotokozedwa kuyambira pa vesi 3 kupita m’tsogolo. Zimenezi zili ndi tanthauzo lalikulu. Malinga ndi mawu oyambirira a m’Baibulo, chilengedwe chonse, kuphatikizapo dziko lapansi, zinakhalapo kwa nthawi yosadziwika, masiku a kulenga asanayambe.

Akatswiri a sayansi ya nthaka amati dziko lapansi mwina lakhalapo kwa zaka pafupifupi 4 biliyoni, ndipo akatswiri a sayansi ya zakuthambo amawerengetsera kuti chilengedwe chonse mwina chakhalapo kwa zaka pafupifupi 15 biliyoni. Kodi zimene asayansiwa apeza, kapena zina zogwirizana ndi zimenezi zomwe angadzapeze m’tsogolomu, zikutsutsana ndi lemba la Genesis 1:1? Ayi. Baibulo silitchula kuti “kumwamba ndi dziko lapansi” zakhalapo kwa zaka zingati. Sayansi sitsutsana ndi zimene Baibulo limanena.

Kodi Masiku a Kulenga Anali Aatali Bwanji?

Bwanji za kutalika kwa masiku a kulenga? Kodi anali a maola 24 enieni? Ena amati tsiku lililonse la masiku a kulenga liyenera kukhala la maola 24 enieni chifukwa choti Mose, amene analemba Genesis, kenaka anadzatchula za tsiku limene linatsatira masiku sikisi a kulenga monga chitsanzo cha Sabata la mlungu ndi mlungu. (Eksodo 20:11) Kodi mawu a mu Genesis akugwirizana ndi mfundo imeneyo?

Ayi, sakugwirizana nayo. Zoona zake n’zoti mawu a Chihebri amene anawamasulira kuti “tsiku” akhoza kutanthauza nthawi yotalika mosiyanasiyana, osati yotalika maola 24 okha basi. Mwachitsanzo, pofotokoza ntchito yonse yolenga zinthu imene Mulungu anachita, Mose anatchula masiku onse sikisi ngati kuti anali tsiku limodzi. (Genesis 2:4) Choncho Malemba sapereka chifukwa chilichonse chonenera kuti tsiku lililonse la kulenga linali la maola 24.

Choncho, kodi masiku a kulenga anali aatali bwanji? Mmene Genesis chaputala 1 ndi 2 chimafotokozera nkhaniyi zimasonyeza kuti masikuwa anatenga nthawi yaitali.

Zinthu Zinkalengedwa Pang’onopang’ono

Mose analemba nkhani yake m’Chihebri, ndipo anailemba ngati mmene munthu amene ali padziko lapansi akanaonera zinthu. Mfundo ziwiri zimenezi, tikaziphatikiza ndi mfundo yakuti chilengedwe chonse chinalipo masiku a kulenga asanayambe, zimatithandiza kuthetsa kusamvana kwakukulu kumene kumakhalapo ponena za nkhani ya kulenga zinthu. Kodi zimatithandiza bwanji?

Tikaona bwinobwino nkhani ya mu Genesis, timaona kuti zinthu zimene zinayamba tsiku limodzi la kulenga zinkapitirirabe mpaka tsiku limodzi kapena masiku angapo otsatira. Mwachitsanzo, tsiku loyamba la kulenga lisanayambe, kuwala kochokera ku dzuwa, lomwe linalipo kale, kunalephera kufika padziko, mwina chifukwa cha mitambo yambiri. (Yobu 38:9) Pa tsiku loyamba la kulenga, chophimba chimenechi chinayamba kuchoka, zomwe zinachititsa kuti kuwala kuyambe kudutsa m’mlengalenga mpaka kufika padziko. *

Pa tsiku lachiwiri la kulenga, zikuoneka kuti m’mlengalenga munapitiriza kuyera, zomwe zinachititsa kuti pakhale mpata pakati pa mitambo yambiri yomwe inali pamwamba, ndi nyanja yomwe inali pansi. Pa tsiku lachinayi la kulenga, m’mlengalenga munali mutayera mokwanira moti dzuwa ndi mwezi zinaoneka “m’thambo la kumwamba.” (Genesis 1:14-16) Kunena kwina tingati, potengera mmene munthu yemwe ali padziko lapansi akanaonera, dzuwa ndi mwezi zinayamba kuoneka. Zinthu zimenezi zinachitika pang’onopang’ono.

Nkhani ya mu Genesis imanenanso kuti pamene m’mlengalenga munapitiriza kuyera, zouluka, kuphatikizapo tizilombo ndi nyama zokhala ndi mapiko, zinayamba kuoneka pa tsiku lachisanu la kulenga. Komabe, Baibulo limasonyeza kuti pa tsiku la sikisi la kulenga, Mulungu anali akadali m’kati ‘moumba ndi nthaka zamoyo zonse za m’thengo, ndi mbalame zonse za m’mlengalenga.’—Genesis 2:19.

N’zachionekere kuti kafotokozedwe ka zinthu ka Baibulo kamasonyeza kuti n’kutheka kuti zochitika zina zikuluzikulu mu tsiku lililonse la kulenga, zinkatha kuchitika pang’onopang’ono m’malo mongochitika nthawi imodzi, ndipo mwina zina mwa izo zinkapitirirabe mpaka kufika ku masiku otsatira a kulenga.

Mwa Mitundu Yawo

Kodi kuonekera pang’onopang’ono kwa zomera ndi zinyama kumeneku kukutanthauza kuti Mulungu anagwiritsa ntchito chisinthiko kuti apange zinthu zosiyanasiyana zamoyo? Ayi. Nkhaniyo imanena momveka bwino kuti Mulungu analenga “mitundu” yonse ya zomera ndi zinyama. (Genesis 1:11, 12, 20-25) Kodi “mitundu” yoyambirira imeneyi ya zomera ndi zinyama inalengedwa m’njira yoti ikhoza kusintha mogwirizana ndi kusintha kwa malo awo okhala? Kodi malire amene amasiyanitsa “mtundu” umodzi wa chamoyo ndi wina amathera pati? Apanso Baibulo silinena chilichonse. Komabe, limanena kuti zamoyo ‘zinachuluka mwa mitundu yawo.’ (Genesis 1:21) Mawu amenewa akusonyeza kuti pali malire a kusintha kumene kungachitike m’kati mwa “mtundu” wa chamoyo. Umboni wa zakufa zakale ndi kafukufuku wamakono, umagwirizana ndi mfundo yoti mitundu ikuluikulu ya zomera ndi zinyama sinasinthe kwambiri pa nthawi yaitali.

Mosiyana ndi zimene anthu ena oumirira pa nkhani zachipembedzo amanena, nkhani ya mu Genesis siphunzitsa kuti chilengedwe chonse, kuphatikizapo dziko lapansi ndi zamoyo zonse zomwe zili pamenepo, zinalengedwa mu nthawi yaifupi zaka zochepa chabe zapitazo. M’malo mwake, mmene buku la Genesis limafotokozera kulengedwa kwa chilengedwe chonse ndi kuonekera kwa zinthu zamoyo padziko lapansi, zimagwirizana ndi zinthu zambiri zimene asayansi atulukira posachedwapa.

Chifukwa cha zikhulupiriro zawo, asayansi ambiri savomereza zimene Baibulo limanena zoti zinthu zonse zinalengedwa ndi Mulungu. Koma n’zochititsa chidwi kuti m’buku lakale la m’Baibulo la Genesis, Mose analemba kuti chilengedwe chonse chinali ndi chiyambi ndi kuti zamoyo zinaonekera pang’onopang’ono kwa nthawi yaitali. Kodi Mose akanadziwa bwanji zinthu zogwirizana ndi sayansizi zaka pafupifupi 3,500 zapitazo? Pali yankho limodzi lokha lomveka. Amene ali ndi mphamvu ndi nzeru zotha kulenga kumwamba ndi dziko lapansi akanatha kuuza Mose zinthu zogwirizana ndi sayansi zimenezo. Zimenezi zikutsimikizira zimene Baibulo limanena zoti ilo “adaliuzira Mulungu.”—2 Timoteo 3:16.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Pofotokoza zomwe zinachitika pa tsiku loyamba la kulenga, mawu a Chihebri a kuwala amene anagwiritsidwa ntchito ndi akuti ʼohr, kutanthauza kuwala basi; koma ponena za tsiku lachinayi la kulenga, mawu amene anagwiritsidwa ntchito ndi akuti ma·ʼohrʹ, amene amatanthauza gwero la kuwalako.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ Kodi Mulungu analenga liti chilengedwe chonse?—Genesis 1:1.

▪ Kodi dziko lapansi linalengedwa m’masiku sikisi a maola 24 tsiku lililonse?—Genesis 2:4.

▪ Kodi zinatheka bwanji kuti zolemba za Mose zonena za chiyambi cha dziko lapansi zikhale zogwirizana ndi sayansi?—2 Timoteo 3:16.

[Mawu Otsindika patsamba 19]

Nkhani ya mu Genesis siphunzitsa kuti chilengedwe chonse, kuphatikizapo dziko lapansi ndi zamoyo zonse zomwe zili pamenepo, zinalengedwa mu nthawi yaifupi zaka zochepa chabe zapitazo

[Mawu Otsindika patsamba 20]

“Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.”—Genesis 1:1

[Mawu a Chithunzi patsamba 18]

Universe: IAC/​RGO/​David Malin Images

[Mawu a Chithunzi patsamba 20]

NASA photo