Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zimene Mumakhulupirira Zili ndi Ntchito?

Kodi Zimene Mumakhulupirira Zili ndi Ntchito?

Kodi Zimene Mumakhulupirira Zili ndi Ntchito?

KODI mukuganiza kuti moyo uli ndi cholinga? Chisinthiko chikanakhala choona, ndiye kuti mawu amene analembedwa m’magazini ya Scientific American akanakhala oona, akuti: “Mmene timachimvera chisinthiko masiku ano zikutanthauza . . . kuti moyo kwenikweni ulibe cholinga.”

Taganizirani zimene mawu amenewo akutanthauza. Ngati moyo kwenikweni ulibe cholinga, ndiye kuti simukanakhala ndi cholinga chilichonse m’moyo kupatulapo kuyesetsa kuchita zinthu zabwino, ndiponso mwina kusiyirako mbadwo wotsatira ena mwa makhalidwe anu achibadwa. Mukafa, moyo wanu bwenzi ukuthera pomwepo. Ubongo wanu, umene umatha kuganiza ndi kusinkhasinkha za tanthauzo la moyo, ukanangokhala chinthu chimene chinakhalako mwangozi padziko pano.

Koma si zokhazo. Anthu ambiri amene amakhulupirira chisinthiko amati Mulungu mwina kulibeko kapena sadzalowerera pa zochitika za anthu. Mulimonsemo, tsogolo lathu ndiye kuti likanakhala m’manja mwa atsogoleri a ndale, a zamaphunziro, ndi a zipembedzo. Poona zinthu zomwe anthu amenewa akhala akuchita, ndiye kuti chipwirikiti, makangano, ndi katangale amene wafala pakati pa anthu akhoza kumangopitirirabe. Chisinthiko chikanakhaladi choona, tikanakhala ndi zifukwa zambiri zokhalira ndi moyo wogwirizana ndi maganizo opanda chiyembekezo akuti: “Tidye timwe pakuti mawa timwalira.”—1 Akorinto 15:32.

Koma dziwani kuti Mboni za Yehova sizivomereza mfundo zimenezi. Ndiponso Mboni sizivomereza chisinthiko, chomwe ndi maziko a mfundo zimenezo. Mosiyana ndi zimenezo, a Mboni amakhulupirira kuti Baibulo ndi loona. (Yohane 17:17) Choncho amakhulupirira zomwe limanena zokhudza chiyambi cha anthufe, zoti: “Chitsime cha moyo chili ndi Inu [Mulungu].” (Salmo 36:9) Mawu amenewa ali ndi tanthauzo lalikulu.

Moyo uli ndi cholinga. Mlengi wathu, chifukwa cha chikondi chake, ali ndi cholinga chabwino chomwe chikukhudza anthu onse amene amasankha kukhala moyo wawo mogwirizana ndi chifuniro chake. (Mlaliki 12:13) Cholinga chimenecho chikuphatikizapo lonjezo loti anthu adzakhala ndi moyo m’dziko lopanda chipwirikiti, mikangano, ndi katangale, ngakhale imfa imene. (Yesaya 2:4; 25:6-8) Mboni za Yehova mamiliyoni ambiri pa dziko lonse lapansi zingakutsimikizireni kuti kuphunzira za Mulungu ndi kuchita chifuniro chake n’kumene kumachititsa moyo kukhala ndi cholinga kuposa chinthu china chilichonse!—Yohane 17:3.

Zimene mumakhulupirira zilidi ndi ntchito, chifukwa zingakhudze osati kokha chimwemwe chanu panopa komanso moyo wanu wa m’tsogolo. Zili kwa inu kusankha. Kodi mukhulupirira chiphunzitso chimene chalephera kufotokoza tanthauzo la umboni umene ukungochulukirachulukira woti zinthu zamoyo zinapangidwa ndi winawake waluso? Kapena kodi muvomereza zimene Baibulo limanena, zoti dziko lapansi ndi zamoyo zimene zili pamenepo zinachita kupangidwa ndi wopanga zinthu waluso kwambiri, Yehova, Mulungu amene ‘adalenga zonse’?—Chivumbulutso 4:11.