Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

“Pansi pa nyanja ndiwo malo aakulu kwambiri pa onse amene ali ndi zamoyo padziko lonse lapansi. Ndipo ndi malonso amene ali ovuta kwambiri kuti zamoyo zikhalepo . . . Komabe, kulikonse kumene tingayang’ane, tikupeza zamoyo, nthawi zina zochuluka kwambiri kuposa momwe tinali kuyembekezera.”—NEW SCIENTIST, BRITAIN.

Pa mlandu waposachedwapa umene anafuna kuti ukhale chitsanzo, woweruza wa khoti lina laboma ku Harrisburg, ku Pennsylvania, m’dziko la United States, analamula kuti “n’zosemphana ndi malamulo a dziko kuphunzitsa [kuti pali winawake wanzeru amene anapanga zinthu zamoyo] m’malo mophunzitsa chisinthiko, pophunzitsa sayansi m’masukulu a boma.”—NEW YORK TIMES, U.S.A.

Malinga ndi kafukufuku amene anafalitsidwa m’nyuzipepala ina mu 2005, “anthu 51 pa anthu 100 alionse a ku America savomereza chiphunzitso cha chisinthiko.”—NEW YORK TIMES, U.S.A.

Pa chilumba cha Galápagos, pali kamba wina wamkulu dzina lake Harriet, yemwe ali ndi zaka 175 ndipo amalemera makilogalamu 150. Kambayu amakhala kumalo osungira zinyama ku Brisbane, m’dziko la Australia, ndipo ndi amene ali “nyama yakale kwambiri yodziwika imene ikadali ndi moyo padziko lonse.”—AUSTRALIAN BROADCASTING CORPORATION.

Ochita kafukufuku ena a ku Switzerland apeza njira imene mitundu ina ya chimanga imagwiritsa ntchito kuti idziteteze ku mbozi zodya mizu ya chimanga. Chimangachi chimatulutsa fungo lomwe limapita mu dothi. Fungoli limaitana nyongolotsi zinazake zomwe zimapha tiana ta mbozi zodya mizu ya chimangazo.—DIE WELT, GERMANY.

Nyama Yaikulu ya M’madzi Inajambulidwa

Kufupi ndi zilumba za Bonin kum’mwera kwa dziko la Japan, asayansi kwa nthawi yoyamba ajambula nyama yaikulu yamoyo ya m’gulu la nkhanu ili kumalo ake okhala achilengedwe. Iwo anaika ku mbedza tinsomba ting’onoting’ono ndi tinsomba tina togayagaya kuti tikhale nyambo, n’kuika makamera pamwamba pa mbedzazo. Nyama yaikulu ya m’gulu la nkhanu yomwe inaonekera, pamalo pokuya mamita 900, akuti inali yaitali pafupifupi mamita 8.

‘Zinyama Zakale Zikuluzikulu Zinkadya Udzu’

“N’zodabwitsa kwa asayansi” kutulukira kuti “zinyama zakale zikuluzikulu zotchedwa ma dinosaur zinkadya udzu,” linatero lipoti lina lofalitsidwa ndi bungwe lotchedwa Associated Press. Anatulukira zimenezi ataunika bwinobwino ndowe za nyama zina za m’gulu limeneli zomwe anazipeza ku India. N’chifukwa chiyani asayansiwa anadabwa? Poyamba anthu ankaganiza kuti “kalelo kunalibe udzu ndipo unadzakhalapo patapita nthawi yaitali zinyamazi zitafa,” linafotokoza choncho lipotilo. Ankaganizanso kuti zinyama zimenezi “zinalibe mano apadera amene amafunika kuti nyama ithe kutafuna udzu wokhakhala.” Katswiri wina wa zomera zakale zakufa, dzina lake Caroline Stromberg, amene anatsogolera gulu limene linatulukira zimenezi, anati: “Anthu ambiri sakanaganiza zoti zinyamazi zinkadya udzu.”

Kodi Njuchi Zimauluka Bwanji?

Anthu ena anenapo mwanthabwala kuti mainjiniya asonyeza kuti njuchi sizingauluke. Zinkaoneka kuti njuchi, zomwe zimaoneka ngati zolemera ndipo zili ndi mapiko amene amayenda pang’onopang’ono, sizingathe kupanga mphamvu zokwanira kuti zinyamuke n’kuyamba kuuluka. Kuti adziwe chinsinsi cha njuchizi, mainjiniya “anajambula njuchi zikuuluka pamalo amodzimodzi, ndipo ankajambula zithunzi 6000 pa sekondi imodzi,” inatero magazini ya New Scientist. Njira imene njuchi zimagwiritsa ntchito akuti ndi “yodabwitsa.” “Phikolo limakupizira chakumbuyo ndipo pokupizapo limapanga kona ya madigiri 90, kenaka likamabwerera kutsogolo limatembenuka, ndipo limachita zimenezi nthawi 230 pa sekondi imodzi. . . . Zili ngati mmene chimakhalira chinthu chozungulira chokhala ndi zitsulo zingapo chimene chimakhala pamwamba pa ndege za helikopita, zitsulozo zitakhala kuti nazonso zikuzungulira pazokha,” anatero mmodzi mwa anthu amene anachita kafukufukuyo. Zimene anapezazi zingathandize mainjiniya kupanga zitsulo zozungulira zokhala pamwamba pa helikopita zabwino kwambiri ndi kupanga ndege zotha kuuluka m’njira zosiyanasiyana.

Mbewa Zimaimba Nyimbo

“Mbewa zimatha kuimba nyimbo, ndipo . . . nyimbo zimene zimaimbira mbewa zomwe zikufuna kuti zikhale akazi kapena amuna awo, zimakhala zovuta kuimba, pafupifupi kufanana ndi nyimbo za mbalame,” inatero magazini ya New Scientist. Nyimbo za mbewa zimakhala zokwera kwambiri kupitirira pa mlingo umene makutu a anthu amatha kumva, ndipo mwina chimenechi n’chifukwa chake anthu anali asanamvepo mbewa zikuimba. Ochita kafukufuku pa yunivesite ya St. Louis, ku Missouri, m’dziko la United States anapeza kuti mawu amene mbewa zazimuna zimatulutsa “anali okonzedwa m’magulu a mawu okhala ndi chuni chinachake, zomwe ndi zinthu zomwe zimafunika kuti mawu atchedwe ‘nyimbo.’” Zimenezi zikuika mbewa m’gulu la nyama zapadera. Nyama zina zoyamwitsa zimene zikudziwika kuti zimaimba nyimbo ndi anamgumi, ma dolphins mitundu ina ya mileme, ndi anthu.