Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chifukwa Chimene Sindikondwerera Halowini

Chifukwa Chimene Sindikondwerera Halowini

Chifukwa Chimene Sindikondwerera Halowini

CHAKA chatha, anthu oyandikana nawo nyumba anali m’kati mokonzekera Halowini, lomwe ndi tsiku latchuthi lotchuka m’mayiko ena lomwe zochitika zake n’zogwirizana kwambiri ndi zamizimu. Koma Michael wa zaka 14 wa ku Canada anali kuganizira zina. M’chimangirizo cha ku sukulu chomwe analemba, Michael anati:

‘Panopa kwada, ndipo mawa ndi tsiku la Halowini. Ndikayang’ana panja, ndikuona kuti mabwalo onse a anthu oyandikana nawo nyumba akongoletsedwa ndi zinthu zokhala ngati ziliza ndi mafupa a anthu ndipo m’mawindo awo aikamo nyali zapadera. * Makolo akumalizitsa kukonza zovala zapadera za ana awo, ananso akuganizira za kuchuluka kwa maswiti amene alandire mawa.

‘Banja lathu ndi losiyana ndi mabanja ena. Pabwalo pa nyumba yathu sitinapakongoletse, ndipo m’mawindo athu mulibe nyali. Anthu amandifunsa kuti n’chifukwa chiyani sindikondwerera Halowini. Mwachidule, Mboni za Yehova sizikondwerera Halowini chifukwa cha chiyambi chake. *

‘Koma kudabwitsa kwake n’koti ndimakonda nthawi ya Halowini. Mwina mungafunse kuti, “Chifukwa chiyani?” Chifukwa choti imandichititsa kuganizira zinthu mozama. Imandichititsa kuganiza za chifukwa chimene ndinasankhira kusachita zinthu zinazake. Munthu aliyense amafuna kudziyankhira yekha funso loti kodi chiyambi cha mwambo wina uliwonse chili ndi ntchito. Ine ndikuganiza kuti chili ndi ntchito. Mwachitsanzo, ambiri angakwiye anthu oyandikana nawo nyumba atavala zovala ngati za chipani cha Anazi. Chifukwa chiyani? Chifukwa cha chiyambi cha zovala za Anazi ndi mfundo zimene zimaimira, zimene anthu ambiri amanyansidwa nazo. Ndimanyansidwa ndi mfundo zimene Mdyerekezi, mizimu yoipa, ndi afiti amaimira, ndipo sindifuna kugwirizana nazo m’njira ili yonse. Ndi bwino kuganizira zinthu zimene timasankha ndi zifukwa zathu zosankhira zimenezo, ndiponso kusankha zinthu potsatira mfundo zoyenera, osati chifukwa choti anthu ambiri akuchita zimenezo. N’chifukwa chake ndimakonda nthawi ino yapachaka. Ndimanyadira kukhala wosiyana ndi anthu ena ndi kutsatira mfundo zimene ndimakhulupirira.’

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Nyali zapadera zimenezi zimakhala dzungu lomwe alidula m’njira yoti lizioneka ngati nkhope ya munthu, lokhala ndi mphuno, pakamwa, ndi maso. Kandulo kapena nyali ya mtundu wina imaikidwa m’kati mwake.