Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Dzitetezeni Kuti Asakubereni Galimoto!

Dzitetezeni Kuti Asakubereni Galimoto!

Dzitetezeni Kuti Asakubereni Galimoto!

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU SOUTH AFRICA

VUTO la kuba magalimoto likukula m’mizinda yambiri padziko lapansi, kuyambira ku Karachi mpaka ku Lisbon, ku Nairobi mpaka ku Rio de Janeiro. Kuyambira 1993 mpaka 2002, malinga ndi bungwe la U.S. Bureau of Justice Statistics, magalimoto pafupifupi 38,000 ankabedwa chaka chilichonse m’dziko la United States.

M’dziko la South Africa, lomwe chiwerengero cha anthu ake chimalowa kasikisi mu chiwerengero cha anthu a ku United States, mumabedwa magalimoto ambiri kuposa pamenepa poyerekezera ndi chiwerengero cha anthu, chifukwa mumabedwa magalimoto 14,000 pachaka. Mukaona zitsanzo zomwe zili mu nkhani ino, mumvetsa chifukwa chimene anthu ambiri amaonera kuti kuberedwa galimoto ndiwo umbanda umene amauopa kwambiri. Zinthu zotsatirazi zinachitikadi. Zinachitikira anthu amene amakhala mu mzinda waukulu kwambiri wa ku South Africa, wa Johannesburg. Mukawerenga zomwe zinawachitikirazi, zingakuthandizeni kudziwa zomwe mungachite ngati akufuna kukuberani galimoto, kapenanso, momwe mungapewere kuberedwa galimoto.

Zinthu Zochitikadi

▪ “Ine ndi mnzanga Susan tinkagwirira limodzi ntchito yolalikira kwa chaka chimodzi. Lachitatu linalake, tisanapite ku phunziro lathu la Baibulo lotsatira, tinaimitsa galimoto pansi pa mtengo m’mphepete mwa msewu ku dera lomwe kunali nyumba za anthu, kuti timwe tiyi. Susan anatuluka m’galimoto kuti akatenge basiketi kumbuyo. Akuti azindipatsa kapu yanga, amuna awiri anangotulukira modzidzimutsa, ndipo mmodzi anaika mfuti pakhosi pa Susan. Podzidzimuka, ndinayesera kutuluka m’galimotomo, koma mwamuna winayo anandikankhira m’kati. Choncho tinapezeka kuti akazi awiri takakamizidwa kukhala m’galimoto ndipo amuna awiri akutiyendetsa. Ndinkaganiza kuti atigwiririra kapena kutipha basi.”—Anatero Anika, mtsikana wapabanja.

▪ “Ndinali kuyendetsa galimoto yanga 7 koloko m’mawa, kupita ku ntchito. Ndinaima pa mphambano pamene pamakonda kukhala anthu omwe akusakasaka ntchito. Maganizo anga anali kwina mpaka pamene munthu wina anakankhira mfuti pakhosi panga kudzera pa windo la galimotoyo, lomwe linali lotsegula, n’kunena kuti, ‘Tuluka, apo ayi ndikuwombera.’ Panthawi yomweyo, ndege ya helikopita ya anthu oona zapamsewu inayamba kuuluka pamwamba. Poganiza kuti ndi apolisi, wakubayo anawomba mfutiyo n’kuthawa. Anandiwombera pakhosi, ndipo anadula mtsempha wanga wa mumsana. Zimenezi zinachititsa kuti ziwalo zanga zonse, kuyambira pakhosi kupita pansi, zife. Sindingathe kugwiritsa ntchito manja ndi miyendo yanga, ndipo sindimva chilichonse m’ziwalo zimenezi.”—Anatero Barry, bambo wa mnyamata wa zaka za pakati pa 13 ndi 20.

▪ “Ine ndi mkazi wanga Lindsay tinali titatsala pang’ono kupita kwinakwake kokadya. Ndinali kumudikirira m’galimoto. Makomo a galimotoyo anali okhoma, koma mawindo anali otsegula pang’ono chifukwa cha kutentha. Ndinkayang’ana kutsogolo kwa galimotoyo n’takhala pa mpando wa dalaivala pamene amuna awiri anabwera kuchokera chakuseri, akuoneka ngati akuyendera zawo. Atatsala mayadi pafupifupi eyiti kuti afike kutsogolo kwa galimotoyo, anagawikana, wina kupita kumanzere kwa galimotoyo wina kumanja. Mwadzidzidzi, anafika pa zitseko za galimotoyo akundilozetsa mfuti kumbali zonse ziwiri. Ankalankhula mokuwa pondilamula zochita. Nditayamba kuyendetsa galimotoyo pomvera zonena zawo, anakuwa n’kundiuza kuti ndituluke ndikakhale pampando wakumbuyo. Mmodzi ankayendetsa galimotoyo pamene wina anandikakamiza kuti ndiweramire pansi. Anandifunsa kuti, ‘Ungandipatse chifukwa chotani choti ndisakuphere?’ Ndinayankha kuti, ‘Ndine wa Mboni za Yehova.’ Anapitiriza kunena zoti andipha, ndipo ine ndinapitiriza kupemphera ndi kuganizira za mkazi wanga wokondedwa, n’kumaganiza kuti kodi adzachita chiyani akazindikira kuti mwamuna wake wasowa limodzi ndi galimoto.”—Anatero Alan, woyang’anira woyendayenda amenenso ndi kholo.

Zochitika zimenezi zikusonyeza momwe anthu amabera magalimoto modzidzimutsa ndi mwachangu. Zikusonyezanso mipata imene anthu oba magalimoto amakonda kugwiritsa ntchito. M’madera ambiri masiku ano, n’zoopsa ngakhale kudikirira kapena kupumula m’galimoto yomwe yaimikidwa pa msewu wa m’dera lomwe kuli nyumba za anthu. Malo ena oopsa ndi pa mphambano ndi pa kanjira kopita ku nyumba kwanu.

Pambuyo Poberedwa Galimoto

N’zosangalatsa kuti zomwe Susan ndi Anika anakumana nazo zinatha bwino. Atatengedwa m’galimoto ndi akubawo, azimayi awiriwo anayamba kufotokoza za ntchito yophunzitsa anthu Baibulo yomwe anali kuchita. Zimenezi zikuoneka kuti zinakhudza chikumbumtima cha amunawo. Anika anafotokoza kuti: “Anapepesa chifukwa cha zomwe anali kuchitazo, koma anati chifukwa cha nthawi zomwe tikukhalamozi, amakakamizika kuba magalimoto ndi zinthu zina kuti azipeza zosowa za pamoyo wawo. Tinawafotokozera chifukwa chimene Mulungu amalolera kuti pakhale umphawi ndi kuvutika.” Uthenga wa m’Baibulo unawakhudza mtima akubawo, ndipo anabweza ndalama ndi mawotchi omwe anatenga, ndiponso anatsimikizira Susan ndi Anika kuti sawavulaza m’njira iliyonse. Susan akukumbukira kuti: “Kenaka winayo anayamba kutipatsa malangizo a mmene tingapewere kuberedwa galimoto m’tsogolo.” Anika akuwonjezera kuti: “Anatiuza kuti tiwalonjeze kuti sitidzaimanso m’mphepete mwa msewu n’kumamwa tiyi.” Kenaka, monga momwe anawauzira, akubawo anaimitsa galimotoyo, anatuluka, analandira mosangalala mabuku ofotokoza za m’Baibulo, kenaka analola Susan ndi Anika kuyendetsa galimoto yawoyo bwinobwino.

Alan, woyang’anira woyendayenda uja, analamulidwa kutuluka m’galimoto yake akubawo atafika pa malo opanda anthu. Ngakhale kuti anataya zinthu zamtengo wapatali, anali woyamikira kuti sanamuvulaze. Alan akukumbukira kuti: “Ndikuganiza kuti zinthu zinandiyendera bwino chifukwa choti ndinkachita zomwe ankandiuza kuti ndichite ndiponso sindinkachita zachiwawa, komanso sindinachite zinthu mwaphuma. Koma zimenezi sizikanachitika n’komwe ndikanakhala tcheru. Ndaphunzira kuchokera pa zimene zinandichitikirazi kuti sitiyenera kutayirira ngakhale pang’ono popeza tsopano tikukhala kumapeto kwambiri kwa masiku otsiriza a dongosolo loipa la Satana.” Tsiku lotsatira, Alan ndi Lindsay anabwerera ku gawo lawo kukapitiriza kulalikira limodzi ndi mpingo umene anali kutumikira. Alan anafotokoza kuti: “Tinapemphera, ndipo maso athu anali kuunguzaunguza tsiku lonse lathunthu. Zinali zovuta, koma Yehova anatipatsa ‘mphamvu yoposa yachibadwa.’”—2 Akorinto 4:1, 7, NW.

Barry, amene anakumana ndi zoopsa kwambiri pa onsewa, wakhala akugwiritsa ntchito njinga ya olumala kwa zaka 11 tsopano. Koma n’zolimbikitsa kuti Barry wakhalabe ndi maganizo abwino ndipo sanalole kuti zimene zinamuchitikirazi zimuchititse kutaya mtima. Chikhulupiriro chake mu lonjezo la Yehova Mulungu loti adzabweretsa dziko latsopano lachilungamo sichinasinthe. (2 Petro 3:13) Barry akupitirizabe kupita ku misonkhano yachikristu nthawi zonse ndipo amagwiritsa ntchito mpata uliwonse kuuza ena za chikhulupiriro chake. Iye anati: “Kutumikira Yehova kumandisangalatsa nthawi zonse. Ngakhale kuti ndimagwiritsa ntchito njinga ya olumala ndipo sindingathe kudzichitira ndekha zinthu zambiri, nthawi zambiri ndimaganizira zinthu zimene Yehova wandichitira, ndipo kuchita zimenezi kumandithandiza kupirira. Posachedwapa dongosolo loipali lidzatha, ndipo tsiku limene ndidzathenso kuyenda lidzakhala losangalatsa kwambiri!”—Yesaya 35:6; 2 Timoteo 3:1-5.

Zimene boma la South Africa lachita zathandiza kuti kuba magalimoto kuchepeko. Komabe, magalimoto akubedwabe, ndipo m’madera ena padzikoli magalimoto amene akubedwa akuchuluka. Akristu oona akudziwa kuti Ufumu wa Mulungu ndiwo boma lokhalo lomwe lidzathetse umbanda ndi chiwawa chonse choterechi.—Salmo 37:9-11; Mateyu 6:10.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 14]

MFUNDO ZOTHANDIZA KUTI ASAKUBERENI GALIMOTO

▪ Ngati mukuyendetsa galimoto kumalo kumene kunabedwapo magalimoto, khomani zitseko ndi kutseka mawindo a galimoto yanu.

▪ Mukamachepetsa liwiro kuti muime pa mphambano, khalani tcheru kuti muone anthu okayikitsa amene angakhale atangoimaima kumbali zonse ziwiri za msewuwo.

▪ Ngati musiya mpata wokwanira bwino pakati pa galimoto yanu ndi galimoto yapatsogolo panu, zingakuthandizeni kuti muthe kutembenuka mosavuta n’kuthawa ngati zinthu zitavuta.

▪ Ngati galimoto ina yakugundani kumbuyo, samalani musanatuluke kuti mukaone chomwe chawonongeka, chifukwa umenewu ukhoza kukhala msampha. Ngati zinthu ngati zimenezi zichitika pamalo pomwe pamabedwa magalimoto ambiri, mungachite bwino kupitiriza kuyendetsa galimoto yanu mpaka kukafika ku polisi yomwe muli nayo pafupi.

▪ Khalani tcheru ngati mwaona anthu achilendo atangoimaima pafupi ndi kanjira kolowera kunyumba kwanu. Ngati mutaona zotero, mungachite bwino kungopitirira n’kukabweranso nthawi ina, kapena mukhoza kupita ku polisi yomwe muli nayo pafupi.

▪ Ngati mukufunika kudikirira m’galimoto yomwe yaimikidwa pamalo omwe pamabedwa kwambiri magalimoto kapena pamalo pamene pali anthu ochepa, khalani tcheru n’kumaona zomwe zikuchitika kutsogolo ndi kumbuyo kwanu. Ngati mukuona kuti pali zokayikitsa, yambani kuyendetsa galimotoyo kulowera ku msewu wina.

[Chithunzi patsamba 14]

Barry sanataye mtima ngakhale kuti amagwiritsa ntchito njinga ya olumala