Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi TV Imakuberani Nthawi?

Kodi TV Imakuberani Nthawi?

Kodi TV Imakuberani Nthawi?

MUNTHU wina atakuuzani kuti akupatsani ndalama zokwana madola wani miliyoni kuti musadzaonerenso TV kwa moyo wanu wonse, kodi mungalole? Zaka zingapo zapitazo, munthu mmodzi mwa anthu anayi alionse a ku United States amene anafunsidwapo funso limenelo anayankha kuti sangalole. Kafukufuku winanso anafunsa azibambo kuti atchule chinthu chimene amachifuna kwambiri. Ambiri mwa iwo anati amafuna mtendere ndi chimwemwe. Komabe zimenezi zinabwera pamalo achiwiri. Chinthu chimene chinali pamalo oyamba chinali TV yaikulu.

Anthu ambiri amakonda kuonera TV padziko lonse. Mu 1931, ma TV asanachuluke kwambiri, mkulu wa bungwe la Radio Corporation of America anati: “Ma TV akadzachuluka kwambiri, amene azidzatha kuionera adzakhala anthu ambiri, pafupifupi kufanana ndi anthu a padziko lonse lapansi.” Mawu amenewo ankamveka ngati nthano chabe m’nthawi imeneyo, koma sizili choncho panopa. Masiku ano, akuti mwina pali ma TV okwana 1.5 biliyoni padziko lonse, ndipo anthu amene amaonerera ndi ochuluka kwambiri kuposa nambala imeneyi. Kaya inu mumaikonda kapena ayi, TV imakhudza moyo wa anthu ambiri.

Nthawi imene anthu amathera akuonera TV ndi yochuluka modabwitsa. Posachedwapa, kafukufuku wapadziko lonse wasonyeza kuti anthu ambiri amaonera TV kwa nthawi yopitirira maola atatu tsiku lililonse. Anthu a ku North America amaonera TV kwa maola anayi ndi theka tsiku lililonse, ndipo a ku Japan ndiwo ali patsogolo chifukwa amaonera kwa maola asanu tsiku lililonse. M’kupita kwa nthawi, maola amenewa amachulukana. Ngati titamaonera TV kwa maola anayi tsiku lililonse, ndiye kuti tikamadzafika msinkhu wa zaka 60, tidzakhala titawononga zaka 10 tikuonera TV. Koma palibe wina aliyense wa ife amene angakonde kuti pachiliza chake padzalembedwe mawu akuti: “Mbale wathu wokondedwa wagona apayu anathera nthawi yambiri ya moyo wake akuonera TV.”

Kodi anthu amaonera TV kwa maola ambiri chifukwa choti amasangalala nayo? Osati kwenikweni. Anthu ambiri amadziwa zoti amathera nthawi yochuluka akuonera TV, ndipo pambuyo pake amadziimba mlandu kuti akanatha kugwiritsa ntchito bwino nthawi yawoyo mwakuchita zinthu zina zothandiza. Ena amanena okha kuti “anakodwa mumsampha woonera kwambiri TV.” N’zoona kuti simungakodwe mumsampha woonera kwambiri TV mofanana ndi mmene mungakodwere mumsampha wogwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, ngakhale kuti pali mbali zina zofanana. Anthu amene akodwa mumsampha wogwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo amathera nthawi yaitali akugwiritsa ntchito mankhwalawa. Ngakhale kuti amafuna atachepetsako kapena kusiya kumene khalidwe lawolo, amalephera. M’malo mochita zinthu zina zofunika pamodzi ndi anzawo ndiponso anthu apabanja pawo, iwo amathera nthawi yaitali akugwiritsa ntchito mankhwalawa, ndipo akapanda kutero amavutika. Zizindikiro zonsezi zingaonekenso mwa anthu amene amaonera kwambiri TV.

“Kudya uchi wambiri sikuli kwabwino,” analemba motero Mfumu yanzeru Solomo. (Miyambo 25:27) Mfundo imeneyi imagwiranso ntchito pa nkhani yoonera TV. Ngakhale kuti pa TV pali mapulogalamu ambiri othandiza, kuthera nthawi yaitali tikuonerera kungachepetse nthawi yocheza ndi anthu a m’banja lathu, kungachititse ana kuti asamawerenge kwambiri ndiponso asamakhonze bwino kusukulu, ndiponso kungakulitse vuto la kunenepa. Ngati mumathera nthawi yaitali mukuonera TV, mungachite bwino kuganizira mwakuya za zomwe mukupindulapo. Nthawi yathu ndi yamtengo wapatali yosafunika kuiwononga. Ndi bwinonso kuganizira za mapulogalamu amene timaonera. Tikambirana mfundo imeneyi m’nkhani yotsatira.