Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuchokera kwa Owerenga

Kuchokera kwa Owerenga

Kuchokera kwa Owerenga

Kaonekedwe Katsopano ka Galamukani! Dzulo madzulo ndinamaliza kuwerenga Galamukani! ya January 2006. Kaonekedwe kake katsopanoka ndakakonda kwambiri. Galamukani! tsopano ndi magazini yothandiza kwambiri pophunzira, ndipo kalembedwe kake n’kolimbikitsa wowerengayo kuganiza. Kuyambira koyambirira mpaka kumapeto, ndikutha kuona kuti Yehova akutsogolera zinthu kuti atithandize kupita patsogolo mwauzimu.

B. N., Canada

Ndili ndi zaka 16. Mbali zatsopano za Galamukani! zitithandiza kwambiri pophunzira Baibulo. Nkhani zina zili ndi mafunso othandiza wowerenga kuganizira zimene akuwerengazo. Ndimakonda kugwiritsa ntchito Galamukani! polemba zinthu zomwe timapatsidwa kusukulu. Ndikufuna kuti mupitirize kutikonzera nkhani zochititsa chidwi ndi zothandiza ngati zimenezi.

S. N., Namibia

Chikhulupiriro Chandithandiza Kupirira Matenda Oopsa(January 2006) Nditawerenga nkhani ya Jason Stuart, mavuto anga onse anaoneka kuti ndi aang’ono kwambiri. Ndinazindikira kuti Yehova amayamikira utumiki umene timamuchitira malinga ndi mmene zinthu zilili pamoyo wathu. Ndikuthokoza mkazi wa Jason chifukwa cha kudzipereka kwake ndi chikhulupiriro chake mwa Yehova. Nkhani imeneyi idzakhala mumtima mwanga nthawi zonse ndipo indithandiza kuthana ndi zovuta zomwe ndingakumane nazo m’tsogolo.

C.R.S., Peru

Ndinalira n’tawerenga nkhani ya Jason, osati kokha chifukwa choti ndinakhudzidwa mtima n’tawerenga za mavuto ake, komanso chifukwa choti monga wa Mboni za Yehova, ndine wonyadira kwambiri kukhala ndi mbale wauzimu ngati ameneyu. Kuchokera mu nkhani imeneyi, ndaona ubwino wokonzekera mayesero, chifukwa aliyense wa ife akhoza kukumana ndi zinthu “zom’gwera m’nthawi mwake.”—Mlaliki 9:11.

T. A., Hungary

Amayi anga anamwalira ndi matenda a ALS. Choncho nkhani ya Jason inandikhudza mtima. Chitsanzo chake chinandilimbikitsa kupitiriza kuchita zonse zomwe ndingathe mu utumiki wanga. Ndikupemphera kuti Yehova apitirize kulimbikitsa mbale ameneyu ndi mkazi wake.

L.Z.G., Paraguay

Mfundo yoti Jason anathera nthawi yambiri akuchita phunziro laumwini pamene anali bwino, choncho anali ndi mfundo zambiri zauzimu zoti azigwiritse ntchito pamene anafunikira kutero, inandichititsa kuganiza. Inandilimbikitsa kuchita khama kwambiri pophunzira Baibulo pandekha.

Y. M., Japan

Zimene Achinyamata Amadzifunsa—N’chifukwa Chiyani Ndimadzivulaza? (January 2006) Ndili wachinyamata, ndinavutika ndi kumwa mankhwala osokoneza bongo ndi mowa, koma vuto lomwe ndavutika nalo kwambiri ndilo kudzivulaza. Kulimbana ndi vuto limeneli ndi ntchito yosatherapo, koma nkhani ngati zimenezi zandipatsa mphamvu zomwe ndimafunikira kuti ndithe kupirira vuto limeneli. Ndikusowa mawu okwanira okuthokozerani.

E. C., United States

Ndakhala ndikudzivulaza kuyambira ndili mtsikana. Panopa ndili ndi zaka 56. Ndinasiya chizolowezi chodzivulaza zaka zinayi zapitazo, koma nthawi zina mavuto anga amakhala aakulu kwambiri moti ndimafuna n’tadzivulazanso. Nkhani imeneyi yandifika pamtima kwambiri. Ithandiza anthu ngati ine kupeza nyonga zolimbanirana ndi moyo wa tsiku ndi tsiku.

Dzina labisidwa, Netherlands

Ndili ndi zaka 17 ndipo ndikufuna ndikuthokozeni chifukwa cha nkhani imeneyi. Ndili ndi vuto lodzivulaza. Posachedwapa, ndinadzichekanso. Kenaka ndinapita kwa mayi anga n’kuwapempha kuti apemphere nane. Ngakhale ndili ndi vuto limeneli, ndikudziwa kuti Yehova amandikonda. Nkhani yanuyi yandithandiza kwambiri, ndipo ndikuthokoza Mulungu chifukwa cha nkhani imeneyi!

N. M., Czech Republic

“Sindikukhulupirira zimenezi!” Zimenezo n’zimene ndinanena n’taona nkhani imeneyi. Ndili ndi zaka 18, ndipo ndimakonda kudzivulaza. Ululu umandithandiza kuiwalako nkhawa zanga. Nthawi zambiri ndimafuna kudzizunza mwanjira inayake, ndipo sindidziwa momwe ndingalimbanirane ndi maganizo amenewa. Sindinakhulupirire n’taona nkhani imeneyi. Misozi inalengeza m’maso mwanga, ndipo ndinathokoza Yehova m’pemphero. Ndi m’gulu la Yehova mokha momwe tingapeze chitonthozo ngati chimenechi!

A. P., Russia

N’takwanitsa zaka 14, ndinayamba kuthetsa ululu wanga wa m’maganizo mwa kudzivulaza. Ulendo wina mpaka ndinafunika kupita kuchipatala. Kulemba zochitika za tsiku ndi tsiku kwandithandiza kudziletsa. Komanso, ndikakhala kuti ndikufuna kudzivulaza, ndimaimbira foni mnzanga winawake womvetsa. Pemphero landithandiza kwambiri. Ndipo ndikamadzimva kuti ndine wopanda pake woti sindingathe kupemphera, anzanga ndi akulu achikristu andipemphererapo. Limeneli ndi vuto lovuta kuthana nalo, koma ndaphunzira zomwe ndiyenera kuchita ndipo ndimalandira chithandizo chonse chomwe chilipo kuti ndisamadzivulaze.

N. W., Germany

Chithunzi cha patsamba loyamba la nkhani imeneyi chikusonyeza mtsikana akudzizula tsitsi, ndipo nkhaniyo inatchula za “Sara,” amene amadzizula tsitsi kuti adzilange. Mwana wanga wamkazi ali ndi matenda otchedwa trichotillomania, amene chizindikiro chake ndi kudzizula tsitsi. Matenda amenewa ndi ogwirizana ndi matenda olephera kudziletsa kuti asachite zinthu zinazake. Odwala amachita zimenezi chifukwa choti sangathe kudziletsa, osati chifukwa choti akufuna kudzivulaza. Kuzula tsitsi si chiyambi cha kudzivulaza.

M. H., United States

Yankho la “Galamukani!”: Mawu oti “trichotillomania,” amene anayamba kugwiritsidwa ntchito m’zaka za m’ma 1800, amatanthauza matenda okhudzana ndi khalidwe amene chizindikiro chake chachikulu ndi chilakolako chosaletseka chofuna kudzizula tsitsi. Monga momwe chithunzi chathu chinayesera kuchitira bwino chitsanzo, kuzula tsitsi kwagwiritsidwapo ntchito ndi anthu ena monga njira yodzivulazira. Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti aliyense amene amadzizula tsitsi mosaletseka ndi munthu wodzivulaza amene nkhani yathu inafotokoza. Monga momwe wowerenga wotchulidwa pamwambayu akusonyezera, nthawi zina chizolowezichi chimakhala chogwirizana kwambiri ndi matenda olephera kudziletsa kuchita zinthu zinazake.

Mulimonse mmene zingakhaliremo, akatswiri ena amati tiyenera kuganizira chifukwa chimene chikuyambitsa matenda a “trichotillomania” kuti chithandizo choperekedwa chikhale choyenererana ndi wodwalayo. Choncho anthu amene ali ndi vuto limeneli angachite bwino kukaonana ndi dokotala kuti akawayeze n’kuwauza matenda amene akudwala ndi chithandizo chimene akufunikira.

Kodi Mungayankhe Bwanji? (January 2006) Ndasangalala kwambiri ndi mbali yatsopano imeneyi! Timaphunzitsa zidzukulu zathu sukulu yapakhomo, ndipo imeneyi ikhala mbali yabwino kwambiri yowonjezera pa kuwerenga kwawo kwa Baibulo kwa tsiku ndi tsiku ndi kwa nkhani za mu Galamukani! zimene amawerenga monga mbali ya ntchito zawo za kusukulu. Zikomo kwambiri chifukwa chosamalira kwambiri ana.

B. E., United States

Mbali imeneyi ndi yovuta, koma ndikapeza yankho, ndimasangalala kwambiri! Dzulo ndinatha madzulo onse ndikuwerenga tsamba limeneli, ndipo linali losangalatsa kwambiri! Ndikadzakula, ndikufuna ndidzathandize nawo kupanga magazini imeneyi kuti ena aphunzire za Yehova!

D. H., United States

Ndili ndi zaka eyiti. Banja lathu linagwiritsa ntchito tsamba limeneli pa phunziro lathu labanja. Timasangalala ndi kafukufuku amene timafunikira kuchita. Mbali yakuti “Ndine Ndani?” nthawi zina imakhala yovuta, koma timasangalala kufunafuna mayankho ake. Pitirizani ntchito yabwinoyi.

C. W., United States