Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuthandiza Mtsikana Wovutika Maganizo

Kuthandiza Mtsikana Wovutika Maganizo

Kuthandiza Mtsikana Wovutika Maganizo

SIBIA, mtsikana wa pa sukulu wazaka 13 ku Mexico, anazindikira kuti mnzake wina wa m’kalasi ankabwera kusukulu akulira nthawi zonse. Iye anayesetsa kum’tonthoza. Tsiku lina mnzakeyo anamuululira kuti bambo ake ndi chidakwa ndipo ankamenya amayi ake.

Sibia akulongosola kuti: “Mnzangayo anandiuza kuti samafunanso kukhala ndi moyo, ndipo mpaka anayesapo kudzipha. Iye anati samakondedwa ndi wina aliyense, komanso amamva kuti ali yekhayekha. Ndiyeno ndinamuuza kuti pali Winawake amene amam’konda kwambiri, yemwe ndi wofunika kuposa wina aliyense m’chilengedwe chonse. Kenako ndinam’fotokozera za cholinga chimene Yehova ali nacho kwa anthu onse.”

Kenako Sibia anam’patsa mnzakeyo buku lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza ndipo anayamba kuphunzira naye bukulo kusukulu komweko pa nthawi yopuma. M’kupita kwa nthawi, mtsikanayo anasiya kudzipatula ndipo anayamba kucheza komanso kuseka ndi anthu ena. M’kalata yopita kwa Sibia, mtsikanayo anati: “Zikomo chifukwa cha mtima wako waubwenzi ndiponso kumvetsetsa kwako. Iweyo uli ngati mchemwali wanga amene ndimalakalaka n’takhala naye. Tsopano ndikudziwa kuti pali winawake amene amandikonda, yemwe ndi Yehova.”

Mwina nanunso mukudziwa wachinyamata amene angapindule ndi buku la Achichepere Akufunsa. Bukuli lili ndi mitu 39, ndipo ina mwa mituyo ndi yoti: “Kodi Ndingapange Motani Mabwenzi Enieni?,” “Bwanji Ponena za Kugonana Ukwati Usanachitike?” ndiponso “Kodi Ndingadziŵe Motani Ngati Chiri Chikondi Chenicheni?” Ngati mukufuna kuitanitsa bukuli, lembani zofunika m’mizere ili pansiyi ndipo tumizani ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ino.

□ Popanda kulonjeza kuti ndidzachita chilichonse, ndikupempha kuti munditumizire buku lomwe lasonyezedwa panoli.

□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo la panyumba laulere.