Njira Zothandiza Kuti Musamaonere TV Kwambiri
Njira Zothandiza Kuti Musamaonere TV Kwambiri
“TIKANGOYATSA TV, tinkaonera chilichonse ndiponso pulogalamu iliyonse yomwe inkaonetsedwa pa nthawiyo. Sitinkaithimitsa mpaka panthawi yoti tigone,” anatero Claudine. Anthu ena amati: “Ndimalephera kudziletsa kuti n’saonere TV,” ndipo enanso amati, “Sindimafuna kuti ndizionera TV kwambiri monga mmene ndimachitiramu, koma sindingathe kusiya.” Kodi inu mumaonera kwambiri TV? Kapena mukuda nkhawa ndi mmene TV ikukhudzira banja lanu? Nazi njira zina zimene zingakuthandizeni kuti musamaonere kwambiri TV.
1. DZIWANI KUCHULUKA KWA NTHAWI IMENE MUMAONERA TV. “Wochenjera asamalira mayendedwe ake,” limatero lemba la Miyambo 14:15. Mungachite bwino kufufuza kuti mudziwe kuchuluka kwa nthawi imene mumaonera TV, ndi kuona ngati mungafunikire kusintha. Muzilemba kuchuluka kwa nthawi imene mwaonera TV kwa mlungu wonse kapena kuposerapo. Mungalembenso mapulogalamu amene mwaonera, zimene mwaphunzirapo, ndiponso ngati mapulogalamuwo anakusangalatsani. Komabe, mfundo yaikulu ndi yoti muwerengere kuchuluka kwa nthawi imene mumathera poonera TV. Mungadabwe kwambiri mutaona kuchuluka kwa nthawi imene mumawononga. Kungodziwa kuchuluka kwa nthawi imene mumathera pa TV kungakuchititseni kuti musinthe.
2. CHEPETSANI NTHAWI YOONERA TV. Yesani kukhala osaonera TV kwa tsiku limodzi, mlungu umodzi, ngakhale kwa mwezi. Kapena, mungaike malire a nthawi imene mukufuna kuti muzionerera tsiku lililonse. Ngati mutachotsa mphindi 30 za nthawi imene mumaonera TV tsiku lililonse, ndiye kuti mungapeze nthawi yowonjezera yokwana maola 15 pamwezi uliwonse. Gwiritsani ntchito nthawi imeneyi pa zinthu zina zofunika, monga kuchita zinthu zauzimu, kuwerenga buku labwino, kapena kucheza ndi banja lanu ndiponso anzanu. Kafukufuku wasonyeza kuti anthu amene saonera kwambiri TV ndi amenenso amasangalala nayo kwambiri kuposa anthu amene amaonera kwa nthawi yaitali.
Kuchotsa TV kuchipinda chogona ndi njira imodzi imene mungachepetsere nthawi yoonerera. Ana amene ali ndi TV kuchipinda kwawo amaonerera kwambiri TV pafupifupi ndi ola limodzi ndi theka kuposa ana amene alibe TV kuchipinda kwawo. Kuwonjezera apo, TV ikakhala kuchipinda kwa mwana, makolo sadziwa zimene mwanayo akuonera. Makolo ndiponso anthu okwatirana adzapeza nthawi yochuluka yocheza ngati atachotsanso TV kuzipinda zawo zogona. Anthu ena asankha kusakhala n’komwe ndi TV.
3. KONZANI NDANDANDA YA ZINTHU ZOTI MUONERE. N’zoona kuti pali mapulogalamu ambiri osangalatsa kuonerera. M’malo momangofufuza m’matchanelo osiyanasiyana kapena kuonera pulogalamu iliyonse yomwe ikuonetsedwa, mungachite bwino kuoneratu ndandanda ya mapulogalamu kuti musankhe zoti muonere. Yatsani TV panthawi imene pulogalamu imene mwasankhayo ikuyamba, ndipo ithimitseni pulogalamuyo ikatha. Kapenanso m’malo moonera TV panthawi imene pulogalamuyo ikuulutsidwa, mukhoza kungoijambula kuti mudzaonere panthawi ina. Zimenezi zingakuthandizeni kuti muonerere pa nthawi imene ili yabwino kwa inuyo ndipo mungadumphe mbali zimene zili ndi malonda.
4. MUZISANKHA ZOONERA. Baibulo linaneneratu kuti anthu a m’nthawi yathu adzakhala “odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, [ndi] okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu.” Mosakayikira mungavomereze kuti anthu ambiri amene amaonetsedwa pa TV ali ndi makhalidwe amenewa. Baibulo limachenjeza kuti, “kwa iwonso udzipatule.” (2 Timoteo 3:1-5) “Musanyengedwe,” tikuchenjezedwa choncho, chifukwa “mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma”—1 Akorinto 15:33.
M’pofunika kudziletsa kuti muzisankha zoonera. Kodi munayamba mwaonererapo sewero kapena filimu yomwe kwa mphindi zingapo zoyambirira munazindikira kuti siyoyenera, koma munapitirizabe kuonera filimu yonse kuti mudziwe zomwe zichitike? Ambiri achitapo zimenezi. Komabe, ngati mungakhale otsimikiza mtima kuthimitsa TV yanu kuti mupange zinthu zina, mudzaona kuti pamapeto pake simudzakhalanso ndi chidwi choti mudziwe zomwe zinachitika m’sewerolo kapena filimuyo.
Kale kwambiri ma TV asanayambe, wamasalmo analemba kuti: “Sindidzaika chinthu choipa pamaso panga.” (Salmo 101:3) Imeneyitu ndi mfundo yabwino yoti tiziikumbukira tikamasankha zoti tionere. Anthu ena asankha kuti asakhalenso ndi TV, mofanana ndi mmene wachitira Claudine. Iye anati: “Sindinkadziwa kuti TV inkandichititsa kukhala munthu wouma mtima kwambiri. Ndikakhala ndi mwayi woonera TV masiku ano, ndimakhudzidwa mtima ndiponso kumva chisoni ndi zinthu zomwe poyamba sizinkandikhudza n’komwe. M’masiku amenewo, ndinkaganiza kuti zomwe ndimasankha kuonera zinali zabwino, koma masiku ano ndazindikira kuti sizinali zoyenera. Ndikamaonerera zinthu zabwino, ndimasangalala nazo kwambiri.”
[Chithunzi patsamba 8]
Lembani kuchuluka kwa nthawi yomwe mumathera poonera TV
[Chithunzi patsamba 8]
Chitani zinthu zina zothandiza m’malo moonera TV
[Chithunzi patsamba 9]
Musazengereze kuthimitsa TV