Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

“Mgwirizano umene ulipo pakati pa kuona ndi kumva zinthu zachiwawa za pa wailesi, TV, ndi m’nyuzipepala, ndi chiwawa chenicheni [cha achinyamata] ndi wamphamvu kwambiri, pafupifupi kufanana ndi umene ulipo pakati pa kusuta fodya ndi khansa ya m’mapapo.”—THE MEDICAL JOURNAL OF AUSTRALIA.

Papezeka umboni wosonyeza kuti mileme yodya zipatso, imene imadyedwa ndi anthu m’madera ena a ku Africa kuno, “ikuoneka kuti mwachibadwa imasunga kachilombo koyambitsa matenda a Ebola.”—MACLEANS, CANADA.

Umboni womwe wapezeka mu ofesi ya loya wamkulu wa boma ku Mexico ukusonyeza kuti pa zaka eyiti zapitazi, ana osachepera 130,000 m’dziko limenelo anabedwa kuti agulitsidwe, kuti azikachita zachiwerewere kapena azikagwiritsidwa ntchito, kapena kuti azikawachotsa ziwalo n’kuzigulitsa.—MILENIO, MEXICO.

N’chifukwa Chiyani Atha Zaka 12 M’ndende?

Anthu atatu a Mboni za Yehova akhala ali m’ndende ku Sawa, ku Eritrea, kum’mawa kwa Africa kwa zaka 12 tsopano. Sanauzidwebe chimene analakwa ndipo mlandu wawo sunayambe wapitako ku khoti. Palibe amaloledwa kukawaona, ngakhale achibale awo. N’chifukwa chiyani akuchitiridwa zonsezi? Chifukwa chokana kuchita nawo zausilikali. Malamulo a dziko la Eritrea salola munthu kukana kuchita nawo zausilikali chifukwa cha chikumbumtima chake. Anyamata akagwidwa, amatsekeredwa ku ndende ya asilikali, kumene nthawi zambiri amamenyedwa kwambiri ndi kuzunzidwa m’njira zina zosiyanasiyana.

Kodi Intaneti Ikuwonongetsa Zinyama?

“Kodi N’zoona Kuti Intaneti Ikuthandiza Kuti Njovu za ku Africa Zithe Mwamsanga?,” inafunsa choncho nyuzipepala ya The New York Times. Anthu ena ogwira ntchito yoteteza zinyama akukhulupirira kuti ikuchitadi zimenezi, ndi kuti mitundu ina yambiri ya zinyama zina nayonso ili pangozi. Kugulitsa pa Intaneti zinthu zosalolezedwa ndi boma akuti kwawonjezeka pamene zinthu zopezeka pa Intanetiyo zakhala zikuchuluka. Atafufuza zinthu zolembedwa m’chingelezi pa Intaneti kwa miyezi itatu anapeza “zinthu zoposa 6,000 zosaloledwa ndi boma kapena zimene zikhoza kukhala zosaloledwa ndi boma zochokera ku zinyama zikugulitsidwa,” kuphatikizapo ziganamba za akamba a m’madzi, ziboliboli zopangidwa ndi mafupa a njovu, ngakhalenso akambuku amoyo.

Njira Yotenthetsera M’nyumba Yosawononga Chilengedwe

“Kutenthetsa m’nyumba ndi nthanga za maolivi kwayambika tsopano,” inatero nyuzipepala ya ku Spain ya El País. Njira imeneyi imatenthetsa madzi ndi nyumba za anthu zoposa 300 ku Madrid. Monga njira yotenthetsera zinthu, nthanga za maolivi ndi zotsika mtengo, ndipo mtengo wake akauyerekezera ndi mtengo wa mafuta ndi wochepa ndi 60 peresenti, ndipo ndi wochepa ndi 20 peresenti poyerekezera ndi mtengo wa malasha. Siziwononga chilengedwe, chifukwa mpweya woipa umene zimatulutsa zikamayaka ndi wofanana ndi umene zimatulutsa zikamawola mwachilengedwe. Ubwino wina ndi woti n’zosasowa. Nthanga za maolivi ndi zimene zimatsala akayenga mafuta ku maolivi, ndipo dziko la Spain akuti n’limene limapanga mafuta ambiri ochokera ku maolivi padziko lonse lapansi.

Apeza Zakudya Zopangidwa Zaka 4,000 Zapitazo

Nyuzipepala ya The New York Times inati asayansi akumba zimene akuzitcha “zakudya zopangidwa ndi ufa zakale kwambiri.” Zakudyazi ndi zopyapyala, zachikasu, zotalika masentimita 50, ndipo n’zopangidwa kuchokera ku mapira a ku China. Anazipeza mu mphika wovindikiridwa, pansi pa matope okhuthala mamita atatu pafupi ndi mtsinje wa Huang kumpoto chakumadzulo kwa China. Malinga ndi magazini ya Nature, akuti mwina malowo anawonongedwa ndi chivomerezi ndi “chigumula chachikulu” zaka pafupifupi 4,000 zapitazo. Pa mtsutsano womwe ulipo wonena za komwe zakudya zopangidwa ndi ufa zinachokera, kuti kaya ndi ku Italy, ku Middle East, kapena ku Asia, nyuzipepala ya Times inati mmodzi mwa anthu amene anapeza zakudyazi, dzina lake Houyuan Lu wa pa sukulu ya Chinese Academy of Sciences, anati: “Kafukufuku ameneyu wasonyeza kuti ku China n’kumene anayamba kupanga zakudya zochokera ku ufa.”