Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo la M’chinenero Chamakono

Baibulo la M’chinenero Chamakono

Baibulo la M’chinenero Chamakono

“NGATI mumakhulupirira kuti Baibulo ndi mawu a Mulungu kwa anthu, ndiye kuti Mulungu akulankhula nafe. . . . Ngati chipembedzo chanu chimakhudza mbali zonse za moyo wanu, ndiye kuti chinenero [cha Baibulo] chiyenera kukhala chamakono.” Analemba choncho katswiri wina wa Baibulo dzina lake Alan Duthie m’buku lake lakuti Bible Translations: And How to Choose Between Them.

Anthu okonda Mawu a Mulungu amavomereza mfundo imeneyi ndi mtima wonse. Iwo sakayikira m’pang’ono pomwe kuti “Malemba onse anawauzira ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu, kulangiza m’chilungamo.” (2 Timoteyo 3:16) Baibulo sikuti ndi buku wamba la mfundo zachipembedzo zachikalekale. Baibulo ndi buku ‘lamoyo, ndi lamphamvu,’ ndipo lili ndi njira zothetsera mavuto omwe anthufe timakumana nawo tsiku ndi tsiku. (Aheberi 4:12) Komabe, kuti anthu owerenga buku lopatulikali alimvetse ndi kuchita zimene limanena, m’pofunika kuti likhale m’chinenero chamakono. Ndipotu, mabuku amene anthu amati Chipangano Chatsopano, analembedwa m’Chigiriki wamba chotchedwa Koine chimene anthu ambiri anali kulankhula, osati m’Chigiriki chapamwamba chimene ankalankhula anthu ofufuza nzeru zapamwamba monga Plato. Inde, Baibulo linalembedwa n’cholinga choti anthu wamba aziliwerenga ndi kulimvetsa.

Kuti izi zitheke, pa zaka zapitazi pakhala pakutulutsidwa Mabaibulo ambiri amakono m’zinenero zosiyanasiyana. Ku mbali yaikulu, zotsatira zake zakhala zopindulitsa kwambiri. Anthu ambiri akhala ndi mwayi wopeza Malemba mosavuta. Komabe, n’zomvetsa chisoni kuti ambiri mwa Mabaibulo atsopanowa sanamasuliridwe molondola, ndipo nthawi zambiri amatengera zikhulupiriro za omasulira ake, ndiponso amasinthasintha mawu. Mwachitsanzo, Mabaibulo ena safotokoza bwino mfundo zosavuta kumva zimene Baibulo limaphunzitsa pankhani ya zimene zimachitikira munthu akafa, kuti mzimu wa munthu n’chiyani, ndiponso dzina la Mulungu woona.

Choncho anthu okonda Mawu a Mulungu akusangalala ndi kutuluka kwa Malemba Achigiriki Achikhristu a Baibulo la New World Translation m’Chichewa. Dzina lake pa Chichewa ndi lakuti Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu. Mboni za Yehova zinalengeza kutulutsidwa kwa Baibulo lamakonoli pa Msonkhano Wachigawo wa 2006 wakuti “Chipulumutso Chayandikira.” Popeza n’losasokonezedwa ndi zikhulupiriro zazipembedzo, Baibuloli n’lomasuliridwa molondola kwambiri kuposa Baibulo lina lililonse la m’mbuyomu, ndipo izi zithandiza kuti anthu amvetse Baibulo mozama, zomwe poyamba sizikanatheka kwa anthu amene sakudziwa zinenero zoyambirira. Koma mwina mungadzifunse kuti, kodi Baibulo lapaderali lamasuliridwa ndi ndani?

Omasulira Amene Analemekeza Mulungu

Ngakhale kuti Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu n’latsopano kwa anthu olankhula Chichewa, lakhalapo kuyambira mu 1950. Panthawi imeneyo, linatulutsidwa m’Chingelezi ndi bungwe la Watch Tower Bible and Tract Society. Bungwe limeneli ndi bungwe lapadziko lonse lomwe linayamba kalekale kufalitsa Mabaibulo. Dzina la Baibulo latsopanoli, lomwe silinatsatire chizolowezi chofala chogawa Baibulo kukhala chipangano “chakale” ndi “chatsopano,” linali njira imodzi chabe mwa njira zambiri zimene zinasonyeza kuti ndi lapadera. Nsanja ya Olonda ya Chingelezi ya September 15, 1950 inati: “Amuna amene akupanga komiti yomasulira Baibuloli anena kuti . . . akufuna asadziwike, ndipo sakufuna kuti mayina awo aululidwe, kaya ali moyo kapena akadzamwalira. Cholinga cha Baibulo limeneli n’kukweza dzina la Mulungu wamoyo ndi woona.”

Baibulo lonse lathunthu la New World Translation of the Holy Scriptures la Chingelezi linatuluka mu 1961. Ndipo ngakhale kuti mayina a anthu amene anamasulira Baibuloli sanaululidwe mpaka pano, zolinga zawo pomasulira Baibuloli kapena kudzipereka kwawo n’zodziwika bwino. Mawu oyamba a m’Baibulo la New World Translation of the Holy Scriptures lomwe linakonzedwanso mu 1984, amati: “Kumasulira Malemba Oyera kumatanthauza kutembenuzira m’chinenero china maganizo ndi mawu a Yehova Mulungu. . . . Anthu amene anamasulira Baibuloli, omwe amaopa ndiponso amakonda Mulungu yemwe analemba Malemba Oyera, akuona kuti Iye anawapatsa udindo wapadera womasulira maganizo ake ndi mawu ake molondola zedi.”

Kupatulapo mfundo yoti anthu a m’komiti yomasulira Baibuloli anali ndi zolinga zabwino, kodi anthuwa anali oyenerera kugwira ntchito imeneyi? Akatswiri ena osakhutira ndi ntchitoyi ananena kuti popeza mayina a omasulira Baibulolo ndiponso maphunziro awo sizinaululidwe, ndiye kuti Baibulolo linamasuliridwa ndi anthu osadziwa ntchito imeneyi. Koma si akatswiri onse amene ali ndi maganizo osathandiza ngati amenewa. Alan S. Duthie analemba kuti: “Tikadziwa amene anamasulira kapena kufalitsa Baibulo linalake, kodi zimenezo zimatithandiza kudziwa ngati Baibulolo analimasulira bwino kapena ayi? Osati kwenikweni. Palibe njira ina yodziwira zimenezi kusiyapo kuwerenga Baibulolo.” *

Izi n’zimene anthu ambiri achita. Tikunena pano, Mabaibulo a Dziko Latsopano athunthu kapena mbali yake chabe oposa 120,000,000, asindikizidwa m’zinenero 53 padziko lonse. Kodi anthu ochuluka amene awerenga Baibuloli apeza zotani?

Baibulo Limene Limayeretsa Dzina la Mulungu

Pa Mateyo 6:9, Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kupemphera kuti: “Atate wathu wa kumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.” Komatu, m’Mabaibulo ambiri sanatchule dzina la Mulungu, m’malo mwake amangodziwika ndi dzina laulemu lakuti “Mulungu” kapena “Ambuye.” Koma umu si mmene zinalili poyambirira. M’Malemba oyambirira a Chiheberi, Mulungu anali kudziwika ndi dzina lakelake lakuti “Yehova,” ndipo limapezekamo nthawi pafupifupi 7,000. (Eksodo 3:15; Salmo 83:18) Patapita zaka, zikhulupiriro zopanda maziko zinachititsa Ayuda kusiya kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu. Atumwi a Yesu atafa, mantha omwewa anafalikiranso mu mpingo wachikhristu. (Yerekezerani ndi Machitidwe 20:29, 30; 1 Timoteyo 4:1) Okopera Malemba Achigiriki anayamba kuchotsa dzina la Mulungu, lakuti Yehova, n’kuyamba kugwiritsa ntchito mawu a Chigiriki akuti Kyʹri·os kutanthauza kuti “Ambuye,” ndi mawu akuti The·osʹ kutanthauza kuti “Mulungu.”

N’zosangalatsa kuti Baibulo la Dziko Latsopano labwezeretsa dzina la Yehova m’Malemba Achigiriki Achikhristu (amene amatchedwanso “Chipangano Chatsopano”), ndipo dzinali limapezekamo nthawi 237. Kubwezeretsa kumeneku kwachitika chifukwa cha kufufuza mosamalitsa ndiponso molondola, osati chifukwa chakuti omasulirawo anangofuna kuchita zimenezi popanda zifukwa zenizeni. Mwachitsanzo, lemba la Luka 4:18 limagwira mawu a pa Yesaya 61:1. M’Malemba oyambirira a Chiheberi, m’vesi la Yesayali muli dzina lakuti Yehova. * N’chifukwa chake mu Baibulo la Dziko Latsopano, lemba la Luka 4:18 linamasuliridwa moyenerera kuti: “Mzimu wa Yehova uli pa ine, chifukwa iye anandidzoza kuti ndilengeze uthenga wabwino kwa osauka.”

Kumasulira kotereku kumathandizanso owerenga kusiyanitsa Yehova Mulungu ndi Mwana wake wobadwa yekha, Yesu Khristu. Mwachitsanzo, Mabaibulo ambiri amamasulira Mateyo 22:44 kuti: “Ambuye ananena kwa Ambuye wanga.” Koma kodi ndani amene akulankhula pamenepa ndipo akulankhula kwa ndani? Vesi limeneli linagwira mawu Salmo 110:1 limene m’malemba a Chiheberi oyambirira lili ndi dzina la Mulungu. N’chifukwa chake, Baibulo la Dziko Latsopano limamasulira vesi limeneli kuti: “Yehova anati kwa Mbuye wanga: ‘Khala kudzanja langa lamanja kufikira nditaika adani ako kunsi kwa mapazi ako.’” Kuzindikira mmene Malemba amasiyanitsira Yehova Mulungu ndi Mwana wake sikuti kumangokhutiritsa nzeru zathu basi. (Maliko 13:32; Yohane 8:17, 18; 14:28) Kudziwa zimenezi n’kofunika kwambiri kuti munthu apulumuke. Lemba la Machitidwe 2:21, limati: “Aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.”

N’londola ndi Lomveka Bwino

Baibulo la Dziko Latsopano lilinso ndi zinthu zina zabwino kwambiri. Baibulo la Chigiriki lokonzedwa bwino kwambiri la Westcott ndi Hort ndi limene analigwiritsa ntchito kwambiri pomasulira Baibulo la Chingelezi. Ndiyeno anasamala kwambiri kuti amasulire Chigiriki choyambiriracho molondola ndiponso motsatira tanthauzo lake lenileni m’chinenero chamakono chosavuta kumva. Kuchita zimenezi kunathandiza kuti Baibuloli limveke monga mmene malemba oyambirira a Baibulo analili komanso kuti anthu alimvetse bwino.

Mwachitsanzo, talingalirani mawu amene ali pa Aroma 13:1, pamene mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu kuti “azimvera olamulira aakulu,” kapena kuti maboma. Mabaibulo ambiri popitiriza lembali amati maboma amenewa “anaikidwa ndi Mulungu” kapena “anasankhidwa ndi Mulungu.” (King James Version; Jerusalem Bible) Olamulira ena agwiritsa ntchito kamasuliridwe kameneka posonyeza kuti sakulakwa kuchita nkhanza. Koma potsatira tanthauzo lake lenileni ndiponso kumasulira molondola, Baibulo la Dziko Latsopano pa vesi limeneli limati, “olamulira amene alipowa ali m’malo awo osiyanasiyana mololedwa ndi Mulungu.” * Tsopano munthu akhoza kuzindikira kuti ngakhale kuti Mulungu sasankha yekha olamulira a dziko, iye amalola anthu amenewa kukhala pamalo aulamuliro, ena okulirapo powayerekeza ndi anzawo, koma nthawi zonse n’ngaang’ono kwa iye.

Baibulo la Dziko Latsopano limayesetsanso kusonyeza kusiyanasiyana kochepa kwa aneni kapena kuti mawu osonyeza ntchito, a Chigiriki. M’zinenero zambiri zamakono, aneni amasiyanitsidwa pang’ono kuti asonyeze nthawi yochitikira chinthu, kaya kale, tsopano, kapena m’tsogolo. M’Chigiriki, aneni amasonyezanso kuti zochitikazo n’zotani, kaya n’zakanthawi kochepa, zachitika ndipo zatha, kapena zikupitirira. Taonani mawu a Yesu pa Mateyo 6:33. Mneni wa Chigiriki wotanthauza “kufuna” amasonyeza kuti kufunako kuyenera kupitiriza. Motero, tanthauzo lonse la mawu a Yesu limaoneka mwa kumasulira vesili motere: “Chotero pitirizani kufuna ufumu choyamba ndi chilungamo chake, ndipo zina zonsezi zidzawonjezedwa kwa inu.” N’chimodzimodzinso ndi lemba la Mateyo 7:7, lomwe lamasuliridwa kuti: “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani; funafunanibe, ndipo mudzapeza, gogodanibe, ndipo adzakutsegulirani.”—Onaninso Aroma 1:32; 6:2; Agalatiya 5:15.

Baibulo la Dziko Latsopano n’lapaderanso chifukwa layesetsa zedi kumasulira mawu ofunika kwambiri mosasinthasintha. Mwachitsanzo, mawu a Chigiriki akuti pa·rou·siʹa, amasuliridwa kuti “kukhalapo” m’malo ambiri omwe mawu amenewa akupezekamo. Motero, owerenga angazindikire mwamsanga kuti, mosiyana ndi ziphunzitso za zipembedzo, kubweranso kwa Yesu sikuti ndi kwa kanthawi kochepa chabe ayi, koma kwa nthawi yaitali.—Mateyo 24:3, 27, 37, 39; 1 Atesalonika 2:19; 3:13; 2 Atesalonika 2:1.

Kuchititsa Kuti Mawu a Mulungu Azipezeka Padziko Lonse Lapansi

Kutulutsidwa kwa Malemba Achigiriki Achikhristu m’Chichewa n’chiyambi chabe. Pakonzedwa zoti Baibulo lonse lathunthu limasuliridwe m’kupita kwa nthawi. Koma kodi owerenga angatsimikizedi kuti Baibulo la Dziko Latsopano la Chichewa lidzakhala lolondola ndi losasinthasintha mawu ngati mmene lilili la Chingelezi?

Indedi angatero. Izi zili choncho chifukwa chakuti ntchito yomasulirayi yakhala ikuyang’aniridwa mosamala ndi Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. Anaganiza mwanzeru kuti pomasulira Baibulo m’zinenero zina, anthu angapo ayenera kugwirira ntchito limodzi. Motero, anakhazikitsa magulu omasulira Baibulo m’mayiko angapo padziko lonse. Ku New York anakhazikitsa Dipatimenti Yothandiza Omasulira, kuti izithandiza magulu amenewo, kuyankha mafunso, ndi kuonetsetsa kuti Baibulo la New World Translation n’logwirizana m’zinenero zosiyanasiyana. Anakonzanso njira yothandiza kwambiri ya pa kompyuta, kuti ithandize omasulira Baibulo. Koma musaiwale: Mbali yaikulu pa ntchito yomasulirayi imagwiridwabe ndi anthu. Komabe pulogalamu ya pa kompyuta imeneyi yathandiza kwambiri kufewetsa cholinga chachikulu cha magulu omasulira Baibulo, chomwe ndi kumasulira Baibulo la New World Translation molondola ndiponso mosasinthasintha mawu monga mmenenso zilili m’Baibulo la Chingelezi. Mwa zina, pulogalamu ya pa kompyutayi imasonyeza mmene liwu lililonse la Chiheberi ndi Chigiriki analimasulira m’Baibulo la Chingelezi. Zimenezi zimathandiza kwambiri omasulirawo kusankha mawu oyenerera a chinenero chawo.

Kuyenda bwino kwa dongosolo limeneli kungaoneke mosavuta mwa kuona zotsatira zake. Tikukupemphani kuwerenga mosamala Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu. Mukhoza kuitanitsa Baibulo limeneli kwa ofalitsa a magazini ino. Musangalalanso ndi mbali zambiri zapadera za Baibuloli monga: zilembo zooneka bwino zosavuta kuwerenga; mitu ya nkhani pamwamba pa tsamba lililonse, imene ingakuthandizeni kupeza mwamsanga mavesi amene mukuwadziwa bwino; mapu amene awafotokoza mwatsatanetsatane; ndiponso mfundo za kumapeto zochititsa chidwi. Koposa zonsezi, mungawerenge Baibulo limeneli muli ndi chikhulupiriro chonse kuti lamasulira mawu a Mulungu molondola m’chinenero chamakono.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 N’zochititsa chidwi kuti pa chikuto cha Baibulo lokhala ndi malifalensi la New American Standard Bible lofalitsidwa mu 1971 panalembedwanso mawu ofanana ndi amenewa, akuti: “Sitinayamikire kapena kugwiritsira ntchito dzina la katswiri aliyense chifukwa tikukhulupirira kuti Mawu a Mulungu ayenera kusonyeza okha kuti ndi olembedwa bwino kapena ayi.”

^ ndime 13 N’zoona kuti Baibulo la Chigiriki la Septuagint n’limene ankaligwiritsa ntchito pogwira mawu a m’Malemba Achiheberi m’mbali ya Baibulo imene imatchedwa Chipangano Chatsopano. Popeza Mabaibulo a Septuagint olembedwa chaposachedwa alibe dzina la Mulungu, akatswiri ambiri amanena kuti dzinali liyeneranso kuchotsedwa m’Malemba Achigiriki Achikhristu. Komabe, Mabaibulo akale kwambiri a Septuagint amene alipobe ali ndi dzina lakuti Yehova, lolembedwa mmene ankalilembera kale m’Chiheberi. Zimenezi zikutipatsa mphamvu yobwezeretsa dzina la Yehova m’Malemba Achigiriki.

^ ndime 17 Onani buku lotanthauzira mawu lakuti A Manual Greek Lexicon of the New Testament, lolembedwa ndi G. Abbott-Smith, ndi lakuti A Greek-English Lexicon lolembedwa ndi Liddell ndi Scott. Malinga ndi mabuku amenewa, ndi mabuku enanso odalirika, mawu a Chigiriki amene ali pamenepa amatanthauza “kuika mwadongosolo, kuika pamalo pake.”

[Zithunzi pamasamba 16, 17]

Mbali za Baibulo la Dziko Latsopano:

Anayesetsa kwambiri kuti amasulire mawu oyambirira a Chigiriki molondola kwambiri ndiponso mosasintha tanthauzo lake, m’chinenero chamakono, chosavuta kumva

Zilembo zosavuta kuwerenga zimachititsa kuti munthu azisangalala poliwerenga

Mitu ya nkhani pamwamba pa tsamba lililonse imathandiza munthu kupeza mosavuta mavesi a m’Baibulo amene akuwadziwa bwino

Mapu amene awafotokoza mwatsatanetsatane amathandiza owerenga kudziwa bwino malo a m’Baibulo

[Chithunzi patsamba 15]

Olemba Baibulo ngati mtumwi Paulo analemba m’chinenero chimene chinali chamakono panthawi imeneyo

[Chithunzi patsamba 18]

Popeza “Baibulo la Dziko Latsopano” n’lomveka bwino, limathandiza kwambiri mu utumiki wachikhristu