Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Funso Lovuta Kwambiri

Funso Lovuta Kwambiri

Funso Lovuta Kwambiri

“CHIFUKWA chiyani?” Zimakhala zomvetsa chisoni kuona ululu ndi kusweka mtima zimene zimakhala m’mawu osavuta kutchula amenewa. Nthawi zambiri anthu amafunsa funso limeneli kukachitika tsoka kapena ngozi, monga: mphepo ya mkuntho ikasakaza malo, n’kupha anthu komanso kuwononga katundu. Chivomerezi chikafafaniza mzinda. Zigawenga zikasokoneza tsiku labwinobwino n’kukhala lochititsa mantha ndi lachiwawa. Kapena munthu amene timamukonda akavulala kwambiri kapena kufa pangozi.

N’zomvetsa chisoni kuti nthawi zambiri anthu amene amakhudzidwa ndi masoka ndi ngozi zotere, amakhala anthu omwe ndi osalakwa komanso sangathe kudziteteza. Posachedwapa kwachitika ngozi ndi masoka ambiri otere, amene achititsa anthu ambiri kufunsa Mulungu akulira kuti, “Chifukwa chiyani?” Taganizirani zitsanzo zina izi:

▪ “N’chifukwa chiyani mwatichitira zimenezi, Mulungu? Takulakwirani chiyani?” Nyuzipepala ya Reuters News, inati mayi wina ku India anafunsa mafunso amenewa tsunami atawononga mudzi wawo.

▪ “Mulungu anali kuti? Ngatidi Mulungu ndi wamphamvu zonse, n’chifukwa chiyani analola zimenezi kuchitika?” Mawu amenewa anafunsidwa m’nyuzipepala ina ya ku Texas, ku United States, mwamuna wina atavulaza ndi kupha anthu ambirimbiri m’tchalitchi powawombera ndi mfuti.

▪ “N’chifukwa chiyani Mulungu analola kuti afe?” Mayi wina anafunsa zimenezi mnzake wina atafa ndi khansa, kusiya mwamuna wake akusamalira ana awo asanu.

Si anthu okhawa amene amaganiza kuti Mulungu ndiye amachititsa mavuto awo. Mwachitsanzo, ponena za masoka achilengedwe, anthu opitirira theka amene anapereka maganizo awo pa Intaneti ananena kuti masoka monga mphepo za mkuntho amachokera kwa Mulungu. N’chifukwa chiyani anthu ambiri amaganiza choncho?

Zipembedzo Zikusokoneza Anthu

M’malo mophunzitsa anthu zinthu zomveka, nthawi zambiri atsogoleri a chipembedzo ndiwo akuthandizira kusokoneza anthu. Tiyeni tikambirane mayankho atatu chabe amene kawirikawiri atsogoleri achipembedzo amapereka pankhani imeneyi.

Yankho loyamba: Atsogoleri ambiri azipembedzo amalalikira kuti Mulungu amabweretsa masoka n’cholinga cholanga anthu ochimwa. Mwachitsanzo, mphepo ya mkuntho yotchedwa Katrina itawononga mzinda wa New Orleans ku Louisiana, ku United States, abusa ena ankati Mulungu wachita zimenezi pofuna kulanga anthu a mu mzindawu chifukwa cha kuchuluka kwa chinyengo, njuga, ndi chiwerewere. Ena anafika mpaka popereka umboni wa m’Baibulo woti Mulungu anawonongapo anthu oipa ndi chigumula kapena moto. Koma mfundo ngati zimenezi, si za m’Baibulo.—Onani bokosi lakuti “Kodi Mulungu Ndiye Amachititsa Masoka?”

Yankho lachiwiri: Atsogoleri ena achipembedzo amati Mulungu ali ndi zifukwa zabwino zochititsira masoka amene amavutitsa anthu koma n’zoti anthufe sitingathe kuzimvetsa. Anthu ambiri samvetsa mfundo imeneyi. Amafunsa kuti: ‘Kodi zingathekedi kuti Mulungu achititse zinthu zoipa zimenezi ndiyeno n’kukana kufotokoza chifukwa chake kwa anthu amene akufunikira chitonthozo ndiponso amene amafunsa mochonderera kuti, “Chifukwa chiyani?”’ Koma zoona zake n’zakuti, Baibulo limati: “Mulungu ndiye Chikondi.”—1 Yohane 4:8.

Yankho lachitatu: Atsogoleri ena achipembedzo amaganiza kuti mwina Mulungu alibe mphamvu kwenikweni ndipo alibe chikondi. Onaninso kuti maganizo otere kamabutsa mafunso ena ofunika kuwaganizira kwambiri. Kodi zingatheke bwanji kuti amene ‘analenga zinthu zonse’ kuphatikizapo chilengedwe chonse chomwe anthu amalephera kuchimvetsachi, alephere kuteteza anthu padziko lapansi lokhali? (Chivumbulutso 4:11) Kodi zingatheke bwanji kuti Mulungu amene anatilenga kuti tizitha kukonda anzathu, amenenso Mawu ake amati ndi chikondi, akhale wopandiratu chisoni akaona anthu akuvutika?—Genesis 1:27; 1 Yohane 4:8.

Komatu mfundo zitatu zatchulidwazi ndi zina chabe za mfundo zimene anthu amagwiritsa ntchito pofotokoza chifukwa chake Mulungu walola kuti tizivutika, funso limene lakhala likuzunguza anthu kwa zaka zambiri. Nkhani yotsatira ifotokoza zimene Baibulo limanena pa nkhani yofunika kwambiri ndi ya panthawi yake imeneyi. Muona kuti Baibulo limayankha funso limeneli momveka ndi motsatirika bwino, ndipo mukadziwa zifukwa zake simungasokonezekenso. Kuwonjezera apo, Baibulo limapereka mawu otonthoza kwa onse amene akumana ndi mavuto osiyanasiyana pa moyo wawo.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 4]

Kodi Mulungu Ndiye Amachititsa Masoka?

Kodi Baibulo limaphunzitsa kuti Mulungu ndiye amachititsa masoka achilengedwe amene akuchitika masiku anowa? Ayi, silitero ngakhale pang’ono! Ziweruzo za Mulungu monga mmene zafotokozedwera m’Baibulo ndi zosiyana kwambiri ndi masoka achilengedwe. Mwachitsanzo, Mulungu akamawononga sapha aliyense, koma amaunika m’mitima ya anthu n’kuwononga okhawo amene ali oipa. (Genesis 18:23-32) Kuwonjezera apo, Mulungu amayamba wachenjeza kaye asanawononge, choncho amapereka mwayi kwa anthu olungama kuti athawe.

Mosiyana ndi zimenezo, masoka achilengedwe amabwera mwina ndi chenjezo lochepa chabe kapena popanda chenjezo lililonse, ndipo amapha ndi kuvulaza anthu popanda kusankha. Komanso, mwa njira zina anthu ndiwo akuchititsa kuti masoka otere awonjezeke mwa kuwononga chilengedwe komanso pokhala kumadera kumene kumachitika zivomerezi, kumene kumasefukira madzi ndi kumalo kumene nyengo yake ili yoipa kwambiri.

[Mawu a Chithunzi]

SENA VIDANAGAMA/​AFP/​Getty Images

[Chithunzi patsamba 4]

Atsogoleri achipembedzo akusokoneza anthu ndi mayankho awo osiyanasiyana