Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

ZINACHITIKIRA KUTI?

1. Kodi zochitika izi zinachitikira pa phiri liti?

Lembani mzere kuzunguliza yankho lanu pa mapupa.

Phiri la Herimoni

Phiri la Karimeli

Phiri la Gerizimu

Phiri la Moriya

◆ Kodi pa phiri limeneli kenaka anadzamangapo chiyani?

․․․․․

◆ N’chifukwa chiyani Abulahamu ankafuna kumupereka nsembe Isake?

․․․․․

◆ Kodi Isake anali mwana wamng’ono panthawi imeneyi?

․․․․․

Kambiranani: Kodi mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani Isake sanavutevute bambo ake akufuna kumupereka nsembe? Kodi Yesu anali ngati Isake m’njira zotani?

ZINACHITIKA LITI?

Lembani mzere kulumikiza mfumu ndi chaka chimene inayamba kulamulira.

1037 B.C.E. 977 936 716 659 607

2. 1 Mafumu 1:38, 39

3. 2 Mafumu 21:24

4. 1 Mafumu 22:42

NDINE NDANI?

5. Ndinatengedwa ukapolo ku Babulo, koma ndinabwerera ku Yerusalemu, kumene ndinamalizitsa ufumu wanga.

NDINE NDANI?

6. Ndinalemba mbali ina ya Baibulo ndili ku Babulo panthawi imene Aroma ankalamulira Yerusalemu.

KUCHOKERA M’MAGAZINI INO

Yankhani mafunso awa, ndipo lembani vesi kapena mavesi a m’Baibulo omwe akusowapo.

Tsamba 4 Kodi kusiyana kumodzi pakati pa maweruzo a Mulungu ofotokozedwa m’Baibulo ndi masoka achilengedwe n’kotani? (Genesis 18:․․․)

Tsamba 5 Kodi n’kulakwa kufunsa chifukwa chimene Mulungu amalolera anthu kuvutika? (Habakuku 1:․․․)

Tsamba 11 Ngati mukulimbana ndi chizolowezi chodziseweretsa maliseche, n’chifukwa chiyani simuyenera kudziimba mlandu kwambiri mukayambiranso? (Salmo 103:․․․)

Masamba 13-14 Kodi chifukwa chimodzi chothawira dama n’chiyani? (1 Akorinto 6:․․․)

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Kodi mungathe kupeza zithunzi izi m’magazini ino? M’mawu anuanu, fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

(Mayankho ali pa tsamba 22)

MAYANKHO A MAFUNSO A PA TSAMBA 31

1. Phiri la Moriya.

◆ Kachisi wa Solomo.

◆ Anamvera lamulo la Yehova.

◆ Ayi.

2. 1037 B.C.E.

3. 659 B.C.E.

4. 936 B.C.E.

5. Manase.

6. Petulo.