Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingathetse Bwanji Chizolowezi Chimenechi?

Kodi Ndingathetse Bwanji Chizolowezi Chimenechi?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndingathetse Bwanji Chizolowezi Chimenechi?

“Ndinayamba kudziseweretsa maliseche ndili ndi zaka eyiti. Kenaka ndinaphunzira mmene Mulungu amaonera zimenezi. Ndinkakhumudwa kwambiri nthawi iliyonse yomwe ndinachita zimenezi. Ndinkadzifunsa kuti, ‘Kodi Mulungu angakonde bwanji munthu ngati ine?’ Ndinkaona kuti sindidzalowa m’dziko latsopano la Mulungu.”—Anatero Luiz. *

MWINA nanunso, ngati Luiz, muli ndi chizolowezi chodziseweretsa maliseche. Mukudziwa kuti Yehova angasangalale nanu mutalimbana ndi chizolowezi chimenechi n’kumatha kudziletsa, popeza kudziletsa ndi chipatso cha mzimu woyera wa Mulungu. (Agalatiya 5:22, 23; 2 Petulo 1:5, 6) Koma nthawi zina mumalephera kudziletsa. Nthawi iliyonse imene mwalephera kudziletsa, mumaona kuti simungathenso kusintha, kuti simungakwanitse kutsatira miyezo yolungama ya Mulungu.

Mmenemo ndi mmene mnyamata wina dzina lake Pedro ankadzionera. Iye anati: “Ndikadziseweretsa maliseche, ndinkakhumudwa kwambiri. Ndinkaona kuti palibenso chimene ndikanachita kuti ndikonze zinthu. Zinkandivuta kupemphera. Ndinkayamba n’kunena kuti: ‘Yehova, sindikudziwa ngati mumve pemphero ili kapena ayi, koma . . . ’” Mnyamata wina dzina lake André ankamvanso chimodzimodzi. Iye anati: “Ndinkadziona ngati munthu wachinyengo. Zinkandivuta kwambiri kudzuka pa bedi m’mawa n’kuyamba kuchita zinthu za tsiku limenelo. Ndinkalephera kukhala pa misonkhano yachikhristu kapena kuchita nawo utumiki.”

Ngati mumamva ngati mmene anamvera Luiz, Pedro, kapena André, musataye mtima. Si inu nokha amene muli ndi vuto limeneli, ndipo si zoona kuti simungathe kusintha! Achinyamata ambiri, ndi akuluakulunso, alimbana ndi vuto lodziseweretsa maliseche, ndipo aligonjetsa. Inunso mukhoza kutero. *

Kulimbana ndi Kudziimba Mlandu

Monga tanenera kale, anthu amene ali ndi chizolowezi chodziseweretsa maliseche nthawi zambiri amadziimba mlandu. N’zosakayikitsa kuti kumva “chisoni chaumulungu” kukhoza kukuthandizani kuthetsa chizolowezi chimenechi. (2 Akorinto 7:11) Koma kudziimba mlandu kwambiri kukhoza kukupweteketsani. Kukhoza kukugwetsani ulesi kwambiri moti mungafune kungosiya, osayeseranso kuthetsa chizolowezichi.—Miyambo 24:10.

Choncho yesetsani kuona nkhaniyi moyenera. Kudziseweretsa maliseche ndi mtundu umodzi wa chidetso. Kukhoza kukupangitsani kukhala ‘kapolo wa zilakolako ndi zosangalatsa zosiyanasiyana’ ndipo kumalimbikitsa maganizo amene angawononge kaganizidwe kanu. (Tito 3:3) Komabe, kudziseweretsa maliseche si mtundu wa chisembwere chonyansa, ngati mmene lilili dama. (Aefeso 4:19) Choncho ngati muli ndi vuto lodziseweretsa maliseche, musaganize kuti mwachita tchimo losakhululukidwa. Chimene chingakuthandizeni ndicho kulimbana ndi chilakolako chofuna kuchita zimenezi ndiponso kuyesayesabe kuthetsa vutoli!

Nthawi zina n’zosavuta kugwa mphwayi mukayambiranso kudziseweretsa maliseche pambuyo posiya. Zimenezi zikachitika, kumbukirani mawu a pa Miyambo 24:16, akuti: “Wolungama amagwa kasanu ndi kawiri, nanyamukanso; koma oipa akhumudwa pom’fikira tsoka.” Mukabwerera m’mbuyo pang’ono sizitanthauza kuti ndinu munthu woipa. Choncho musatope. M’malo mwake, ganizirani zimene zinakuchititsani kuti muyambirenso, ndipo yesetsani kupewa zimenezo.

M’malo momangokhalira kudziimba mlandu chifukwa cha vuto lanulo, khalani ndi nthawi yosinkhasinkha za chikondi ndi chifundo cha Mulungu. Wamasalmo Davide, amene analinso ndi zofooka, anati: “Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuopa Iye. Popeza adziwa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.” (Salmo 103:13, 14) Indedi, Yehova amadziwa kuti ndife opanda ungwiro ndipo tikalakwa, iye “ndi wokhululukira.” (Salmo 86:5) Komabe, iye amafuna kuti tiziyesetsa kusintha.

Kodi mungatani kuti mugonjetse chizolowezi chanucho n’kupewa kuyambiranso?

Ubwino Wouza Munthu Wina

Ngakhale kuti nkhani ya kugonana imatchulidwatchulidwa m’mayiko ambiri, anthu ambiri zimawavuta kuti alankhule nkhani zokhudza kugonana mwaulemu. Inuyo mwina mungamachite manyazi kulankhula za nkhani imeneyi, ngakhale kwa munthu amene mumauzana naye zakukhosi. Mkhristu wina amene analimbana ndi vuto lodziseweretsa maliseche kwa zaka zambiri anati: “Ndimalakalaka n’kadalimba mtima n’kuuza munthu wina za vuto langalo pamene ndinali mnyamata! Ndinakhala ndikudziimba mlandu kwa zaka zambiri, ndipo zinandiwonongera ubwenzi wanga ndi ena, ndipo koposa zonse, ndi Yehova.”

Kodi muyenera kulankhula ndi ndani? Munthu wabwino kulankhula naye angakhale munthu amene ali wokhwima mwauzimu, makamaka kholo lanu. Mukhoza kuyamba n’kunena kuti: “Ndikufuna ndikuuzeni za vuto linalake limene likundisowetsa mtendere kwambiri.”

Mário anaganiza zolankhula ndi bambo ake, omwe anali omvetsa ndiponso anamumvera chisoni. Mpaka anamuuza Mário kuti nawonso anali ndi chizolowezi chimenechi ali achinyamata. Mário anati: “Kuona mtima ndi kulankhula mwachilungamo kwa bambo anga kunandilimbikitsa kwambiri. Ndinazindikira kuti ngati iwowo anatha kuthetsa vutoli, nanenso ndikhoza kutero. Zinandikhudza kwambiri kuona momwe bambo anakhudzidwira moti ndinayamba kulira.”

André analimba mtima n’kulankhula ndi mkulu wachikhristu, ndipo ndi wosangalala kuti anachita zimenezi. * André anati: “Pamene mkuluyo ankandimvetsera, misozi inalengeza m’maso mwake. N’tamaliza kulankhula, ananditsimikizira kuti Yehova amandikonda. Anandiuza kuti anthu ambiri amakhala ndi vuto limeneli. Anandilonjeza kuti azindifunsa mmene zinthu zikuyendera ndipo andibweretsera mfundo zina zoti ndiwerenge zochokera m’mabuku ofotokoza za m’Baibulo. N’talankhula naye, ndinatsimikiza kuti ndipitiriza kuyesetsa kuthetsa vutoli, ngakhale ngati nditayambiranso nthawi zina.”

Mofanana ndi Mário ndi André, mukhoza kupeza thandizo pamene mukuyesayesa kuthana ndi chizolowezi chodziseweretsa maliseche. Tsatirani malangizo amene ali m’bokosi lakuti, “Gonjetsani Chizolowezichi!” Inde, dziwani kuti mukhoza kuthetsa vuto limeneli!

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Tasintha mayina mu nkhani ino.

^ ndime 6 Ngakhale kuti anthu amene tawatchula mu nkhani ino ndi amuna, akazi ambiri amavutikanso ndi chizolowezi chodziseweretsa maliseche. Choncho malangizo amene aperekedwawa akukhudza amuna ndi akazi omwe. Onaninso kuti nkhani ino ikunena za kudziseweretsa wekha maliseche. Kuseweretsa maliseche a munthu amene simuli naye pabanja ndi mbali imodzi ya zimene Baibulo limatcha dama, lomwe ndi tchimo lalikulu kwambiri pamaso pa Mulungu.—Onani nkhani yakuti “Achinyamata Akufunsa Kuti . . . Kodi Pali Cholakwika Kugonana Tisanakwatirane?” mu Galamukani! ya August 8, 2004, tsamba 12 mpaka 14.

^ ndime 17 Mtsikana mwina angalankhule ndi mayi ake kapena mlongo wokhwima mwauzimu wa mumpingo mwawo.

ZOTI MUGANIZIRE

▪ Kodi n’chifukwa chiyani m’pofunika kukumbukira kuti Yehova “ndi wokhululukira”?—Salmo 86:5.

▪ Kodi muchita chiyani kuti muthetse chizolowezi chodziseweretsa maliseche?

▪ N’chifukwa chiyani simuyenera kuchita manyazi kupempha thandizo?

▪ Kodi njira yabwino yoikira maganizo anu pa zinthu zoyera ndi yotani?

[Bokosi/Chithunzi patsamba 11]

Kuyambiranso Si Kulephera!

N’zosavuta kuganiza kuti: ‘Ndalephera, choncho ndingosiya zolimbana ndi vutoli basi.’ Musalole kuganiza choncho. Musalole kuti kubwerera m’mbuyo kamodzi, ngakhale kangapo, kukusiyitseni kulimbana ndi vutoli.

Taganizirani chitsanzo ichi: Ngati mukukwera masitepe n’kupunthwa, kenaka n’kubwerera m’mbuyo sitepe imodzi kapena awiri, kodi munganene kuti, ‘Basi, zateremu ndingotsika n’kukayambiranso poyambirira’? Ayi! Nangano n’chifukwa chiyani muyenera kuganiza molakwika chonchi mukamalimbana ndi zizolowezi zoipa?

Nthawi zambiri mukayambiranso, mumadziimba mlandu. Mukhoza kudziimba mlandu mopitirira muyeso poganiza kuti ndinu munthu wopanda pake, wofooka, ndi wachabechabe. Musalole kuti muzidziimba mlandu mopitirira muyeso choncho. Kuchita zimenezo kumakutherani mphamvu zimene mukanagwiritsa ntchito kuti muyambirenso kulimbana ndi vutoli. Ndipo kumbukirani izi: Munthu wamkulu koposa onse amene anakhalapo pa dziko lapansi, Yesu Khristu, anabwera kudzawombola ochimwa, osati anthu angwiro. Choncho palibe aliyense wa ife amene angachite zinthu mwangwiro panthawi ino.—Zachokera mu Galamukani! ya April 8, 1991, tsamba 30.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 12]

Gonjetsani Chizolowezichi!

▪ Dzikakamizeni kuti muyambe kuganiza zina.—Afilipi 4:8.

▪ Pewani kuyang’ana zinthu zimene zingakudzutsireni zilakolako zoipa.—Salmo 119:37.

▪ Pempherani kuti mukhale ndi “mphamvu yoposa yachibadwa.”—2 Akorinto 4:7.

▪ Khalani otanganidwa ndi ntchito zachikhristu.—1 Akorinto 15:58.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 12]

Thandizo Lina

Kuti mumve zambiri za mmene mungathetsere chizolowezi chodziseweretsa maliseche, onani mutu 25 ndi 26 m’buku la Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.