Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mulungu Amatiganizira!

Mulungu Amatiganizira!

Mulungu Amatiganizira!

MMENE Mulungu wachitira ndi nkhani ya kupanduka kwa anthu mu Edene, zikungosonyeza kuti amakonda aliyense wa ife ndipo amaganizira kwambiri za tsogolo lathu. Tikukupemphani kuganizira bwino umboni wotsatirawu wakuti Mulungu amatiganizira, ndipo werengani m’Baibulo lanu malemba amene asonyezedwa.

● Watipatsa dziko lapansi lokongola kwambiri, limene lili ndi zamoyo zosangalatsa, komanso n’lachonde.—Machitidwe 14:17; Aroma 1:20.

● Anapanga thupi lathu modabwitsa kuti tizisangalala ndi moyo m’njira zosiyanasiyana tsiku ndi tsiku, monga kumva kukoma tikamadya chakudya chabwino, kusangalala ndi kulowa kwa dzuwa, kusangalala ndi mwana akamaseka, ndi kumva bwino tikakhala ndi wokondedwa wathu.—Salmo 139:14.

● Watipatsa malangizo anzeru otithandiza kulimbana ndi mavuto osiyanasiyana.—Salmo 19:7, 8; 119:105; Yesaya 48:17, 18.

● Watipatsa chiyembekezo chabwino kwambiri, monga chodzakhala ndi moyo padziko lapansi la paradaiso ndi chodzaona okondedwa athu amene anafa akuukitsidwa.—Luka 23:43; Yohane 5:28, 29.

● Anatumiza Mwana wake wobadwa yekha kudzatifera kuti tikhale ndi chiyembekezo chokhala ndi moyo kosatha.—Yohane 3:16.

● Wakhazikitsa Ufumu wa Mesiya kumwamba n’kutipatsa umboni wokwanira wakuti Ufumu umenewu udzalamulira dziko lapansi posachedwapa.—Yesaya 9:6, 7; Mateyo 24:3, 4, 7; Chivumbulutso 11:15; 12:10.

● Akutipempha kuti tizilankhula naye mwa kupemphera, kumukhuthulira nkhawa zonse za kumtima kwathu, ndipo amatimvetseradi tikamachita zimenezi.—Salmo 62:8; 1 Yohane 5:14, 15.

● Nthawi zonse amatitsimikizira kuti amatikonda ndipo amatidera nkhawa.—1 Yohane 4:9, 10, 19.