Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika?

N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika?

N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika?

NTHAWI zina munthu akamafunsa kuti “Chifukwa chiyani?” amakhala akufuna kulimbikitsidwa komanso kuyankhidwa, popeza ngati munthu wafunsa funso limeneli chifukwa chakuti wakumana ndi mavuto aakulu, kwenikweni amakhala kuti akufuna kutonthozedwa. Kodi Baibulo limatonthoza anthu otero? Ganizirani mfundo zitatu za choonadi cha m’Baibulo zokhudza nkhani imeneyi.

Yoyamba, sikulakwa kufunsa kuti n’chifukwa chiyani Mulungu akulola kuti tizivutika. Anthu ena amada nkhawa kuti mwina kufunsa funso lotere n’kupanda chikhulupiriro mwa Mulungu kapena n’kusalemekeza Mulungu. Mosiyana ndi maganizo amenewa, malinga ngati mutafunsa funso lanu moona mtima, simunalakwe chifukwa pali anthu ambiri amene afunsaponso funso limeneli. Mneneri Habakuku anafunsapo Mulungu kuti: “N’chifukwa chiyani mukundionetsa zinthu zosalungama zonsezi? N’chifukwa chiyani mukulekerera chiwawa, kusamvera, umbanda, ndi nkhanza kufalikira paliponse?” (Habakuku 1:3, Contemporary English Version) Yehova Mulungu sanadzudzule Habakuku. M’malo mwake, anachititsa kuti mafunso a munthu wachikhulupiriro ameneyu alembedwe m’Baibulo kuti tonsefe tiwawerenge.—Aroma 15:4.

Yachiwiri, m’pofunika kuzindikira kuti Yehova amakhudzidwa mtima akakuonani mukuvutika. Sikuti kuvutika kwanu alibe nako ntchito. Iye “amakonda chilungamo,” ndipo amada zinthu zoipa ndi mavuto amene zimabweretsa. (Salmo 37:28, NW; Miyambo 6:16-19) Kalelo m’masiku a Nowa, Mulungu “anavutika m’mtima mwake” chifukwa cha chiwawa chimene chinafalikira padziko lapansi. (Genesis 6:5, 6) Mulungu sanasinthe, amamva chimodzimodzi akaona zinthu zimene zikuchitika masiku anozi.—Malaki 3:6.

Yachitatu, Mulungu si amene amachititsa zinthu zoipa. Baibulo limafotokoza mfundo imeneyi momveka bwino. N’kunyoza kwakukulu kunena kuti Mulungu ndiye amachititsa kuphana ndi uchigawenga. Taonani zimene lemba la Yobu 34:10 limanena: “N’kutali ndi Mulungu kuchita choipa, ndi Wamphamvuyonse kuchita chosalungama.” Lemba la Yakobe 1:13 limanenanso chimodzimodzi kuti: “Pokhala pa mayesero, munthu asanene kuti: ‘Mulungu akundiyesa.’ Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa.” Choncho ngati mwakumana ndi zinthu zoipa khalani otsimikiza mtima kuti si Mulungu amene anazichititsa.

Kodi Ndani Akulamulira Dziko Lapansili?

Komabe mfundo zimene takambiranazi zikutisiya ndi funso lakuti, ngati Mulungu ali wachikondi, wachilungamo, ndi wamphamvu, n’chifukwa chiyani zinthu zoipa zachuluka chonchi? Choyamba, tiyenera kufotokoza kaye mfundo imodzi imene anthu saimvetsa bwino. Anthu ambiri amaganiza kuti Mulungu ndiye wolamulira wa dzikoli, amene akuyendetsa zonse. Mkulu wa sukulu ina yophunzitsa abusa anati: “Palibe atomu kapena kanthu kakang’ono kalikonse kamene sikalamulidwa ndi Mulungu.” Kodi Baibulo limaphunzitsadi zimenezi?

Siliphunzitsa zimenezi ngakhale pang’ono. Ambiri amadabwa kudziwa amene Baibulo limanena kwenikweni kuti ndiye akulamulira dziko. Mwachitsanzo, lemba la 1 Yohane 5:19 limati: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” Kodi woipa ameneyu ndi ndani? Yesu Khristu anamutcha Satana Mdyerekezi, “wolamulira wa dziko.” (Yohane 14:30) Kodi simukuona kuti n’zomveka kunena kuti Satana ndiye akulamulira dziko? Satana ndi wankhanza, wabodza, ndi woipa, makhalidwe amene akuchititsa kuti anthu azivutika kwambiri. Komano, n’chifukwa chiyani Mulungu akulola Satana kulamulira?

Nkhani Imene Inayambira mu Edene

Kodi n’chiyani chimene kholo lachikondi ndi labwino kwambiri lingachite ngati litanamiziridwa pamaso pa anthu kuti limanamiza ana ake, limawalamulira mwankhanza, ndi kuti limawabisira zinthu zabwino? Kodi angathetse mabodzawo mwa kumenya munthu amene wawafalitsayo? Mwachidziwikire sangatero! Chifukwa ngati atatero, anthu angaganize kuti zimene amanena munthu uja n’zoona.

Chitsanzo chimenechi chikutithandiza kumvetsa zimene Yehova Mulungu anachita atatsutsidwa kuchiyambiyambi kwa mbiri ya anthu mu Edene. Pa nthawi imeneyo, anthu awiri oyamba, Adamu ndi Hava, anauzidwa za ntchito yosangalatsa kwambiri imene Mulungu anafuna kuchitira ana ake padziko lapansi. Anauzidwa zodzadza dziko lapansi, kuligonjetsa, n’kulisintha kukhala paradaiso. (Genesis 1:28) Kuwonjezera apo, ana auzimu ambirimbiri a Mulungu anali nayo chidwi kwambiri ntchito yosangalatsayi.—Yobu 38:4, 7; Danieli 7:10.

Pokhala Mulungu wowolowa manja, Yehova anapatsa Adamu ndi Hava munda wokongola kwambiri wokhala ndi zipatso zosiyanasiyana zokoma. Koma anawaletsa kudya mtengo umodzi wokha, “mtengo wodziwitsa zabwino ndi zoipa.” Adamu ndi Hava akanasonyeza kuti akukhulupirira Mulungu kotheratu mwa kusadya zipatso za mtengo umenewu, ndipo akuzindikira kuti Atate wawo anali ndi ufulu wowasankhira zabwino ndi zoipa.—Genesis 2:16, 17.

Komano, n’zachisoni kuti mmodzi wa ana auzimu a Mulungu, pofuna kulambiridwa, anauza Hava kuti ngati atadya chipatso choletsedwa, sadzafa. (Genesis 2:17; 3:1-5) Potero, mngelo woipa ameneyu, kapena kuti Satana, anatsutsiratu Mulungu, n’kumuonetsa ngati wabodza! Satana anapitirizanso kutsutsana ndi Mulungu pomunamizira kuti Iye anali kubisira Adamu ndi Hava zinthu zofunika kwambiri kuzidziwa. Satana anakhala ngati wanena kuti anthu afunikira kudzisankhira okha zinthu zabwino ndi zoipa. Mwachidule, Satana ananena kuti Mulungu si Wolamulira kapena Tate wabwino ndi kuti Satanayo atakhala wolamulira, angawalamulire bwino anthu.

Chifukwa chonena mabodza oipa ndi anjiruwa, mngeloyo anadzipanga yekha kukhala Satana Mdyerekezi. Mayina amenewa amatanthauza “Wotsutsa” ndi “Woneneza.” Kodi Adamu ndi Hava anatani? Anamvera Satana, n’kumukana Mulungu.—Genesis 3:6.

Yehova akanatha kuwononga opanduka amenewa nthawi yomweyo. Koma, monga tanenera m’chitsanzo chathu, nkhani ngati zimenezi sizingathetsedwe pobwezera mwachiwawa. Kumbukiraninso kuti mamiliyoni ambiri a angelo ankamvetsera pa nthawi imene Satana amatsutsa Mulungu. Ndipo ngakhale kuti chiwerengero chake chenicheni sitikuchidziwa, angelo ambiri anadzagwirizana ndi Satana kupandukira Mulungu, n’kukhala ziwanda.—Maliko 1:34; 2 Petulo 2:4; Yuda 6.

N’chifukwa Chiyani Mulungu Sanalowererepo?

Mwa kupandutsa Adamu ndi Hava kuti adziimire paokha popanda kudalira Mlengi wawo, mwa njira ina Satana anayambitsa banja lomwe silinali lodziimira palokha kwenikweni, koma lomwe linali kulamulidwa ndi iyeyo. Kaya limadziwa kapena ayi, banja limeneli linayamba kulamulidwa ndi “atate” wawo Mdyerekezi, ndipo linayamba kudzisankhira lokha zolinga ndi kuyendera mfundo zawozawo. (Yohane 8:44) Koma, kodi moyo umenewu ukanawabweretsera ufulu weniweni ndi chimwemwe chosatha? Yehova anadziwiratu kuti moyo umenewu udzawagwiritsa mwala. Komabe analola opandukawo kupitirizabe kudzisankhira okha zochita, chifukwa ndi njira imeneyi yokha imene ikanathetseratu nkhani imene inayambira mu Edene ija.

Kwa zaka zoposa 6,000 tsopano, anthu apanga dongosolo loyendetsera zinthu, uku akuyesera mitundu yosiyanasiyana ya ulamuliro ndi kakhalidwe. Kodi inuyo mukusangalala ndi zotsatirapo zake? Kodi anthu alidi ndi chimwemwe, mtendere ndi mgwirizano? Yankho lake n’lodziwikiratu kuti ayi! M’malo mwake, nkhondo, njala, masoka achilengedwe, matenda, ndi imfa zakhala zikuvutitsa anthu, kuyambitsa “mkhalidwe wopanda pake,” “zopweteka,” ndi ‘kubuula.’—Aroma 8:19-22; Mlaliki 8:9.

Komabe, ena angafune kudziwa kuti, ‘N’chifukwa chiyani Mulungu sateteza anthu kuti asakumane ndi mavuto?’ Kuchita zimenezo kungakhale kupanda chilungamo, ndipo kungasokoneze nkhani ija n’kutichititsa kuganiza kuti kupandukira Mulungu kulibe zotsatirapo zake. Choncho Yehova saletsa mwachindunji kapena mwa njira zina zinthu zoipa ndi masoka zimene zimatsatirapo anthu akapanda kumumvera. * Yehova sangaikire nawo kumbuyo bodza lakuti dongosolo la Satana likhoza kupambana, ndi kuti lapeza chinsinsi cha moyo wachimwemwe. Komabe, sikuti palibe chilichonse chimene Yehova wachita. Monga mmene tionere panopa, wachita zambiri.

“Atate Wanga Akugwirabe Ntchito Mpaka Pano

Mawu a Yesu amenewa akusonyeza kuti si kuti Mulungu wangokhala, n’kumangoonerera zinthu zikuchitika. (Yohane 5:17) Komano, kuyambira pa kupanduka kwa anthu mu Edene, iye wakhala akuchita zambiri. Mwachitsanzo, iye anauzira olemba Baibulo kulemba kuti “mbewu” ya m’tsogolo idzaphwanya Satana ndi onse amene akupitirizabe kumumvera. (Genesis 3:15) Kuwonjezera apo, pogwiritsa ntchito mbewu imeneyi, Mulungu adzapanga boma, lomwe ndi Ufumu wa kumwamba, umene udzadalitsa anthu omvera ndi kuthetseratu mavuto onse, ngakhale imfa imene.—Genesis 22:18; Salmo 46:9; 72:16; Yesaya 25:8; 33:24; Danieli 7:13, 14.

Pofuna kukwaniritsa malonjezo osangalatsa amenewa, Yehova anatumiza ku dziko lapansi Uyo amene anali kudzakhala Wolamulira wamkulu wa Ufumu umenewu. Ameneyu si winanso, koma Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu. (Agalatiya 3:16) Pofuna kukwaniritsa cholinga cha Mulungu, Yesu analimbikira kwambiri kulalikira za Ufumu wa Mulungu. (Luka 4:43) Ndipo kwenikweni, Khristu anasonyeza chitsanzo cha zimene adzakwaniritsa monga Mfumu ya Ufumuwu. Anadyetsa anthu anjala zikwi zambiri, anachiritsa odwala, anaukitsa akufa, ndipo pamene anatontholetsa namondwe anaonetsa kuti ali ndi mphamvu ngakhale zolamulira zinthu zachilengedwe. (Mateyo 14:14-21; Maliko 4:37-39; Yohane 11:43, 44) Ponena za Yesu, Baibulo limati: “Malonjezo a Mulungu, kaya akhale ochuluka chotani, akhala inde kudzera mwa iye.”—2 Akorinto 1:20.

Onse amene amamvera Yesu ‘n’kuchoka m’dziko,’ limene lili dongosolo la zinthu losayanjana ndi Mulungu ndipo lolamulidwa ndi Satana, amalandiridwa m’banja la Yehova. (Yohane 15:19) Banja la padziko lonse limeneli la Akhristu oona limatsatira lamulo la chikondi, n’lokonda mtendere, ndipo limadziwika bwino kuti likuyesetsa kuthetsa tsankho ndi kusankhana mitundu kulikonse pakati pawo.—Malaki 3:17, 18; Yohane 13:34, 35.

M’malo molimbikitsa zinthu za m’dziko lino, Akhristu oona akuchirikiza ndi kulengeza Ufumu wa Mulungu pomvera lamulo la Yesu la pa Mateyo 24:14. Taganizirani izi: Ndani akulalikira “uthenga wabwino uwu wa ufumu” padziko lonse lapansi? Ndi banja liti lauzimu padziko lonse lapansi limene lakana kulowa nkhondo ndi kutenga nawo mbali pa mikangano yogawanitsa anthu amitundu ndi mafuko osiyanasiyana? Ndipo ndi ndani amene alola Mawu a Mulungu kutsogolera khalidwe lawo, ngakhale ngati anthu ambiri sakutsatira mfundo zake zapamwamba? (1 Yohane 5:3) Anthu ambiri aona kuti Mboni za Yehova ndizo zimachita zimenezi. Tikukupemphani kuti mufufuze nokha umboni wake.

Sankhani Ulamuliro wa Mulungu!

Anthu otalikirana ndi Mulungu amenenso akusocheretsedwa ndi Satana, apanga dongosolo la zinthu padzikoli limene likungowonjezera mavuto a anthu n’kuwasiya opanda chiyembekezo. Ngakhalenso zinthu zachilengedwe padziko lapansili zikuwonongedwa. Koma Yehova wakhazikitsa boma lakumwamba limene lasintha moyo wa anthu mamiliyoni ambiri ndipo lapatsa aliyense wa anthu amenewa chiyembekezo chodalirika. (1 Timoteyo 4:10) Kodi inuyo musankha ulamuliro uti?

Inoyi ndiyo nthawi yoti musankhe, chifukwa Mulungu salola kuti Satana ndi dziko lake loipa apitirizebe kukhalapo. Chifuno cha Mulungu choyambirira chopanga dziko lapansili kukhala paradaiso, sichinasinthe. N’chifukwa chake Ufumu wa Mulungu ndi anthu amene amaukonda adzapitirizabe kukulirakulira m’mphamvu, pamene dziko lolamulidwa ndi Satana lidzakumana ndi “masautso” owonjezerekawonjezereka mpaka pamene Mulungu adzaliwononga. (Mateyo 24:3, 7, 8) Choncho ngati munafunsapo kwa Mulungu mukulira kuti, “Chifukwa chiyani?”, mverani zimene akunena m’Baibulo kuti mupeze chitonthozo ndi chiyembekezo chodalirika. Ngakhale tsopano lino, misozi yanu ingasinthe n’kukhala chisangalalo.—Mateyo 5:4; Chivumbulutso 21:3, 4.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 19 Ngakhale kuti nthawi zina Mulungu walowererapo pa zochita za anthu, zochita zake sizikhala zochirikiza dongosolo la zinthu la masiku anoli. M’malo mwake zimakhala zokhudzana ndi kukwaniritsidwa kwa chifuniro chake.—Luka 17:26-30; Aroma 9:17-24.

[Zithunzi patsamba 7]

Kodi mukukondwera ndi zotsatirapo za ulamuliro wa anthu?

[Mawu a Chithunzi]

Baby: © J. B. Russell/​Panos Pictures; crying woman: © Paul Lowe/​Panos Pictures

[Chithunzi pamasamba 8, 9]

Yesu adzabwezeretsa Paradaiso, ndiponso adzaukitsa ngakhale anthu amene anafa