Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndinapulumutsidwa ku Masautso Anga Onse

Ndinapulumutsidwa ku Masautso Anga Onse

Ndinapulumutsidwa ku Masautso Anga Onse

Yosimbidwa ndi Jean-Claude François

Chifukwa chotsatira chikumbumtima changa chophunzitsidwa baibulo, ndinazunzika kwa zaka 7 m’ndende zosiyanasiyana zopitirira 12. ngakhale ndinavutika choncho, ndimaona kuti ndine wodala. dikirani ndifotokoze.

NDINABADWIRA ku Algiers, m’dziko la Algeria, pa January 9, 1937. Panthawi imeneyo, dziko la Algeria linkalamulidwa ndi dziko la France, ndipo bambo anga anali ndi udindo m’gulu la asilikali a dziko la France. Chifukwa cha ntchito yawo, ankayendayenda ndipo ankapita ku mayiko ngati Egypt, Iraq, Lebanon, ndi Syria. Nthawi zina ankakhalako kwa miyezi ingapo, choncho sankakhala ndi nthawi yambiri yocheza ndi ana awo asanu.

Ndinkakonda kwambiri sukulu ndipo ndinkakhoza bwino. Koma ndinkalephera kupeza mayankho okhutiritsa a mafunso ngati akuti, N’chifukwa chiyani timafa, ndipo n’chifukwa chiyani pali zoipa ngati Mulungu ali wamphamvu zonse ndi wabwino? Ndinkafunanso kudziwa mmene moyo unayambira. Chiphunzitso cha Darwin choti tinachita kusanduka kuchokera ku zinthu zopanda moyo n’chimene chinkaoneka chomveka, choncho, m’kupita kwa nthawi, ndinayamba kukhulupirira kuti kulibe Mulungu.

Potsirizira Pake, Ndinapeza Mayankho

Mu 1954, mnzanga wina dzina lake Georges, amene anali atakhala wa Mboni za Yehova, anandipatsa kabuku kotchedwa Evolution Versus the New World. * Ndinakawerenga mwachidwi. Kuwonjezera pa kusonyeza kuti chiphunzitso choti zamoyo zinachita kusanduka kuchokera ku zinthu zina n’chosamveka, kabukuka kanasonyezanso kuti zamoyo zakufa zakale zimagwirizana ndi nkhani ya mu Genesis, imene imati Mulungu analenga chamoyo chilichonse “monga mwa mtundu wake.” (Genesis 1:12, 25) Koma ndinali ndisanapezebe yankho la funso loti n’chifukwa chiyani padziko pamachitika zinthu zoipa.

Georges anali mpainiya, kapena kuti mtumiki wa nthawi zonse, ndipo ankathera nthawi yake yambiri akuphunzitsa anthu Baibulo, buku lomwe ndinali ndisanaliwerengepo. Koma kodi akanatha kuyankha mafunso anga? Ndinapita ku nyumba kwake, kumene ankakhala ndi apainiya ena, ndipo anandipatsa mayankho ochokera m’Malemba a mafunso anga ambiri. Kenaka ndinayamba kuphunzira Baibulo mwadongosolo, ndipo ndinasangalala kwambiri kuchita zimenezi. Kuyambira nthawi imeneyo, sindinatopepo n’kufufuza mosamala m’Mawu a Mulungu kuti ndipezemo chuma chake cholimbitsa chikhulupiriro.—Miyambo 2:1-5.

Ndinayamba kupita ku misonkhano yachikhristu, yomwe inkachitikira m’chipinda chapansi pa lesitilanti inayake pakatikati pa mzinda wa Algiers. A Mboniwo anandilandira ndi manja awiri, ndipo m’kupita kwa nthawi ndinayamba kupita ku misonkhano yonse. Atalengeza kuti pa msewu winawake padzakhala msonkhano wina, ndinapita pa msewupo. Nditafika, ndinauzidwa kuti Mbonizo zakumana kuti zipite ku ulaliki wa ku nyumba ndi nyumba. (Machitidwe 20:20) Komabe, sindinabwerere, ndipo mmenemo ndi mmene ndinayambira kulalikira kwa anthu onse.

Ulendo wachitatu umene ndinapita kolalikira, ndinalankhula ndi anthu ndekhandekha. Pa khomo linalake, ndinalephera kupeza lemba la m’Baibulo lomwe ndinaligwira mawu. Mwininyumbayo anati: “Bwanawe, udzayambe kuphunzitsa anthu ukadzadziwa kuphunzitsa.” Kenaka anatseka chitseko. N’takhumudwa, ndinakhala pa benchi n’kufufuza lemba lomwe linandivuta kupeza lija. N’talipeza patatha mphindi zingapo, ndinabwerera n’kukamusonyeza mwamuna uja.

Ndinabatizidwa pa March 4, 1956, posonyeza kudzipereka kwanga kwa Mulungu. Patatha miyezi sikisi, ndinafunika kusankha chochita pa nkhani yaikulu. Kodi nditumikire monga mpainiya wokhazikika, kapena ndivomere kukakhala mphunzitsi wa sukulu m’katikati mwa dziko la Algeria n’kumathera nthawi yochepa mu utumiki? Ndinasankha kuchita upainiya.

Bambo anga anakwiya koopsa n’zimene ndinasankhazi ndipo anandiika mpeni pakhosi, n’kundiuza kuti ndizibwera kunyumba madzulo alionse. Anandiuzanso kuti asiya kundidyetsa, ngakhale kuti ndinali wokonzeka kudzipezera ndekha zosowa. Choncho ndinkachoka ndi njala kunyumba m’mawa, ndinkadya chakudya chamasana ndi apainiya, n’kudya sangweji madzulo ndisanabwerere kunyumba.

Kupewa Mabomba ndi Kuzinda Zipolopolo

Panthawi imeneyi, dziko la Algeria linali pa nkhondo yomenyera ufulu wawo kuchokera ku dziko la France, ndipo mu mzinda wa Algiers munkangokhalira kuphulika mabomba ndiponso munkangochitika zipolowe. M’mwezi winawake munaphulitsidwa mabomba 100. Mabomba ankatcheredwa m’mabasi, m’malo ogulitsira mowa, ndi m’mabwalo a masewero. Zinali zovuta kuchita utumiki. Anthu ankaopa kutsegula zitseko zawo, ndipo nthawi zambiri pankakhala malamulo oti munthu asayende ikakwana nthawi yakutiyakuti. Komanso, anthu ankafunsidwa kuti asonyeze ziphaso zawo ndi kuchitidwa chipikisheni.

Lamlungu pa September 30, 1956, ine ndi apainiya ena angapo tikukonza malo athu osonkhanira, bomba linaphulika mu lesitilanti yomwe inali pamwamba pathu, ndipo anthu ambiri anaphedwa ndi kuvulala. Mwamwayi, palibe aliyense wa ife pansipo amene anavulala. Mu December, ine ndi mlongo wina tinkalalikira pamsewu pomwe panali anthu ambiri. Kenaka, galimoto inatidutsa mothamanga ndipo anthu amene anali m’galimotoyo anawombera zipolopolo kudzera pa mawindo ake otsegula, kuwombera khamu la anthu amene anali pamsewupo. Tinathawira pakhomo la nyumba inayake, pamene ndinakankhira mlongoyo pansi, nanenso n’kugwera pansi. Zipolopolo zomwe zinanjanja pansi zinkadutsa pamwamba pathu. Zitachitika zimenezi, tonsefe tinkachita zinthu mosamala kwambiri tikamalalikira.

Ndinakana Kumenya Nawo Nkhondo

Pa March 1, 1957, ndinaitanidwa kuti ndikalembedwe usilikali. Popeza chikumbumtima changa monga Mkhristu sichikanandilola kumenya nawo nkhondo, ndinapemphera kuti ndikhale ndi mphamvu zotha kufotokozera zimenezi kwa akuluakulu a boma. Ndinapempheranso kuti ndisakangane ndi bambo anga. Mtima wanga unakhala m’malo pamene ndinauzidwa kuti ndipite ku mzinda wa Lille, ku France, kutali ndi kwathu.

Patatha masiku 6 ndinafika pa nyumba inayake yotchedwa Linga la Lille, lomwe linamangidwa kalekale pa nthawi imene Mfumu Louis XIV ankalamulira m’ma 1600. Pogwiritsa ntchito Baibulo, ndinafotokozera akuluakulu a asilikaliwo chifukwa chimene sindinkafunira kumenya nawo nkhondo, ndipo anandiponya m’ndende. M’mawa wina, asilikali anandikokera kunja kwa chipinda changa, anafufuzafufuza m’zovala zanga, ndipo anapeza Baibulo laling’ono. Kenaka anandiuza kuti ndigone chafufumimba pachipale chofewa, anaponyera Baibulolo pafupi nane, n’kuyamba kuthinikiza chigwiriro cha mfuti pankhongo panga, ndipo anandigoneka pamenepo pafupifupi kwa mphindi 30. Kenaka, ndinasangalala kwambiri kuti asilikaliwo anandilola kusunga Baibulo langalo, ndipo likadali pa shelefu yanga ya mabuku mpaka pano. Komabe, chifukwa cha mmene anandizunzira tsiku limenelo, ndinkamva kupotokola m’mimba kwa zaka zambiri.

Patapita masiku ochepa, msilikali wamkulu anandiwerengera mawu amene anali m’kalata imene analandira kuchokera kwa bambo anga. Kalatayo inati: “Mum’kakamize kuti agonjere. Asweke mtima ngati pangafunike kutero.” Popeza sindinagonjere, msilikaliyo anandiponyera m’chipinda cha mdima, mmene ndinkagona pa katoni ndipo ndinkafunda kabulangete kakang’ono. Popeza munalibe chimbudzi, ndinkadzithandizira pakona ya chipindacho. Sindinkasamba, kutsuka m’kamwa, kapena kutsuka mbale yanga yodyera. Patatha milungu iwiri, ananditumiza ku ndende ya Fresnes ku Paris.

Pa zaka 6 zotsatira, ndinalamulidwa kanayi konse kuti ndikhale m’ndende, ndipo ndinakhala m’ndende zosiyanasiyana zokwana 14. Panyengo ina yozizira, ndinali ku Fontevrault, yomwe inali nyumba ya masisitere yomangidwa m’zaka za m’ma 1100 ku Loire Valley, imene inkagwiritsidwa ntchito ngati ndende. Anandilanda katundu wanga yense n’tangofika. Chifukwa ndinkangokhalira kuwapempha kuti andipatse Baibulo langa, alonda anandiika m’chipinda chandekha kwa mwezi umodzi. M’chipinda chimenecho, mdani wanga wina uja, kuzizira, anabwereranso ndipo anandizunza kwambiri, moti ndinayamba kutsokomola magazi.

Kenaka anandisamutsira ku ndende ina yabwinoko, yotchedwa Château de Turquant, kufupi ndi tawuni ya Saumur, kumene akaidi ankagwira ntchito ku nyumba za oweruza opuma pantchito. Mmodzi wa akaidiwo anali Ahmed Ben Bella, amene kenaka anadzakhala pulezidenti wa dziko la Algeria. Kwa miyezi ingapo, ndinkamulalikira. Panthawi ina anandiuzapo kuti: “Ndiwe mbadwa ya ku Algiers, ndipo uli kuno chifukwa unakana kutenga zida n’kupha anthu a ku Algeria.” Ankandilemekeza chifukwa chochita zimenezi.

Ndinalimbikitsidwa Kupirira Ziyeso Zina

Thanzi langa linafookerafookera, ndipo anandipeza ndi TB n’kunditumiza ku chipatala chaching’ono kum’mwera kwa France, kumene ndinakhala chigonere kwa miyezi ingapo. Dokotala wanga anandiuza kuti ndikufunika kuchitidwa opaleshoni kuti achotse mapapo amodzi amene anawonongeka, ndipo ndinavomera kuchitidwa opaleshoniyo, bola ngati akanandilola ‘kusala mwazi.’ (Machitidwe 15:29) Dokotalayo anakwiya ndipo anakana kundichita opaleshoni. Pamenepa n’kuti nditakhala zaka 6 kundende.

Ndinachoka ku chipatala chaching’ono chija pakatikati pa nyengo yozizira, ndipo zovala zomwe ndinali nazo zinali zomwe ndinavalazo basi. Koma monga momwe Yehova anatumizira Onesiforo kukathandiza mtumwi Paulo, tsopano ananditumizira wondithandiza, Mbale Adolphe Garatoni, amene anandisunga n’kukhaladi ‘wondithandiza ndi wondilimbikitsa.’ (Akolose 4:11; 2 Timoteyo 1:16-18) Ndi thandizo lake, ndiponso la dokotala wina kum’mwera kwa France, ndinayamba kuchira.

Panthawi imeneyi, panali zinthu zambiri zoti ndilipire, zofuna ndalama zambiri. Sindinkadziwa kuti ndalama zake ndizitenga kuti. Kenaka tsiku linalake kunabwera mlendo. Mlendoyo anati: “Ndine loya. Pulezidenti wa dziko la Algeria, Bambo Ben Bella, andituma kuti ndidzakupatseni izi.” Anandipatsa envulopu imene inali ndi ndalama zambiri kuposa zimene ndimafuna zija. Ndinathokoza Yehova, “Wakumva pemphero,” ndi mtima wanga wonse.—Salmo 65:2.

Utumiki Wosangalatsa ndi Mkazi Wokongola

Popeza tsopano ndinali n’tatuluka m’ndende, ndinayambiranso utumiki wa nthawi zonse. Mu mpingo wa Melun, kufupi ndi mzinda wa Paris, ndinakumana ndi mkazi wina wamasiye wa zaka 35, dzina lake Andrée Morel. Mwamuna wake woyamba, yemwenso anali Mboni, anamwalira pangozi ya galimoto. Tinakwatirana pa September 26, 1964. Pa August 1, 1965, tinaikidwa kukhala apainiya apadera. Ngakhale kuti Andrée analibe thanzi labwino, anachita utumiki wa nthawi zonse kwa zaka 28!

Mu 1967 ndinaikidwa kukhala woyang’anira dera, kapena kuti mtumiki amene amayendera ndi kulimbikitsa mipingo ya Mboni za Yehova. Tinatumikira kum’mwera kwa France kuchokera ku Bordeaux mpaka ku Monaco, ndipo kwa chaka chimodzi tinatumikira ku Paris. Chifukwa cha kufooka kwa thanzi lathu, ntchito yoyendayenda inali yovuta, koma ndi thandizo la Yehova, tinatumikira abale athu kwa zaka 20, mpaka mu 1986, pamene tinakhalanso apainiya apadera.

Moyo Wanga Panopa

Tsopano ndili ndi zaka pafupifupi 70 ndipo ndaphunzira nthawi ndi nthawi kuti Yehova nthawi zonse amapatsa atumiki ake mphamvu zimene akufunikira kuti apirire. Ndipo zina mwa mphamvu zimenezo munthu amazipeza pophunzira Mawu a Mulungu ouziridwa, amene ndimayesetsa kuwerenga kuyambira koyambirira mpaka kumapeto chaka chilichonse.—Yesaya 40:28-31; Aroma 15:4; 2 Timoteyo 3:16.

Ine ndi Andrée timalimbikitsidwa tikaona anthu akumvera uthenga wabwino ndi kupereka moyo wawo kwa Yehova. Ndipo pa zaka zapitazi, taona anthu 70 mwa ophunzira Baibulo athu akuchita zimenezo, zimene zatibweretsera chimwemwe chosaneneka ndi chosatha. Poganizira za moyo wathu, timamva ngati mmene anamvera wamasalmo, amene analemba kuti: “Munthu uyu wozunzika anafuula, ndipo Yehova anamumva, nam’pulumutsa m’masautso ake onse.”—Salmo 34:6.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova koma tsopano anasiya kukasindikiza.

[Chithunzi patsamba 27]

Ndili m’ndende ku Château de Turquant, kufupi ndi tawuni ya Saumur

[Zithunzi patsamba 29]

Ndili ndi mkazi wanga mu 1967, ndi panopa