Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“N’labwino Kwambiri”

“N’labwino Kwambiri”

“N’labwino Kwambiri”

Zimenezo n’zimene mwamuna wina ndi mkazi wake, ku Georgia m’dziko la United States, ananena atawerenga buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Buku la masamba 224 limeneli lili ndi zithunzi zokongola, ndipo linatulutsidwa mu 2005. Iwo anafotokoza kuti: “N’losavuta kumva moti pafupifupi aliyense akhoza kuligwiritsa ntchito. Komabe, lili ndi mfundo zakuya mokwanira kukhutiritsa njala yauzimu ngakhale ya anthu ophunzira kwambiri.”

Mutu wa bukuli pawokha wakopa kale chidwi cha anthu ena, monga momwe zomwe zinachitikira mwamuna wina ndi mkazi wake, a ku New Jersey, m’dziko la United States, zikusonyezera. Atalandira buku limeneli ku msonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova ku Florida, banjali linakwera ndege kupita kutchuthi ku Bahamas. Mayi wina wogwira ntchito ya kasitomu akuona katundu wawo, anaona bukuli, anawerenga mutu wake, ndipo anati, “Ndakhala ndikufuna kudziwa yankho la funso limeneli kuyambira kalekale.” Banja la Mbonilo linapatsa mayiyo buku limodzi lowonjezera lomwe anali nalo, ndipo mayiyo anasangalala kwambiri.

Tsiku lotsatira, banja lomweli linkawerenga bukulo pa gombe la nyanja, ndipo mayi wina wa komweko wogulitsa katundu kwa alendo anachita nalo chidwi. Mayiyo anafotokoza kuti m’mawa wa tsiku lomwelo anapemphera kwa Mulungu kuti adziwe yankho la funso lomwelo, loti kodi Baibulo limaphunzitsa chiyani kwenikweni? Anafunsa za mmene angalipezere bukulo, ndipo anasangalala kwambiri pamene banjalo linamupatsa buku lomaliza lomwe linatsala nalo loti lingathe kupatsa munthu wina.

Buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? tsopano likupezeka m’zinenero zoposa 145, ndipo mabuku oposa 40 miliyoni asindikizidwa kale. Mukhoza kuitanitsa bukuli mwa kulemba zofunika m’mizere ili panoyi ndi kutumiza ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ino.

□ Popanda kulonjeza kuti ndidzachita chilichonse, ndikupempha kuti munditumizire buku lomwe lasonyezedwa panoli.

□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.