Zochitika Padzikoli
Zochitika Padzikoli
▪ Padziko lonse lapansi, anthu amayesera nthawi zoposa 5.7 miliyoni tsiku lililonse kuti abere anthu pa Intaneti.—MAGAZINE, SPAIN.
▪ “Mu 2005, chiwerengero cha anthu odzipha ku Japan chinaposa 30,000 kwa zaka 8 zotsatizana.” Japan ndi limodzi mwa mayiko amene anthu amadzipha kwambiri padziko lonse lapansi.—MAINICHI DAILY NEWS, JAPAN.
▪ “Pa zaka 500 zapitazi, zochita za anthu zachititsa kuti mitundu 844 ya zamoyo ithe (kapena ithe m’tchire).”—IUCN, WORLD CONSERVATION UNION, SWITZERLAND.
▪ Malinga ndi ziwerengero za boma, anthu 6 pa anthu 100 alionse ku Britain, amagonana amuna okhaokha kapena akazi okhaokha. Malamulo amene anakhazikitsidwa mu 2005 “amaloleza akazi okhaokha kapena amuna okhaokha kukwatirana,” ndipo amawapatsa ufulu wofanana ndi wa ukwati wa mwamuna ndi mkazi.—THE DAILY TELEGRAPH, ENGLAND.
Madzi Oundana Akuyenda Mofulumira
“Madzi oundana ochokera ku dwale lalikulu la madzi oundana a ku Greenland ayamba kuyenda mofulumira,” inatero magazini ya Science. Zithunzi zojambulidwira m’mlengalenga zikusonyeza kuti pa zaka zisanu zapitazi, madzi oundana a ku Greenland ayamba kuyenda mofulumira kuwirikiza pafupifupi kawiri kuposa kale, ndipo akumayenda makilomita oposa 12 pachaka. Pa zaka khumi zapitazi, madzi oundana omwe akusungunuka anawonjezeka kuchoka pa makyubiki kilomita 90 pachaka kufika pa makyubiki kilomita 220 pachaka. Choncho asayansi akuti “madzi a m’nyanja adzakwera kwambiri m’tsogolo muno kuposa mmene anali kuyembekezera.”
Matchalitchi Akumbukira Darwin
Mu February 2006, matchalitchi achikhristu pafupifupi 450 a ku United States anakondwerera kuti patha zaka 197 kuchokera pamene Charles Darwin anabadwa. Pa chikondwererochi panalinso “zochitika zina ndi ulaliki womwe cholinga chake chinali kutsindika kuti chiphunzitso cha Darwin, chakuti zamoyo zinachita kusanduka kuchokera ku zinthu zina n’chogwirizana ndi Chikhristu, ndi kuti Akhristu sakufunikira kuchita kusankha pakati pa chipembedzo ndi sayansi.” Malinga ndi nyuzipepala ya Chicago Tribune, Michael Zimmerman, katswiri wa sayansi ya zamoyo ndi mkulu wa pa koleji ya Letters and Sciences pa yunivesite ya Wisconsin-Oshkosh, amene anakonza chikondwererocho, anati: “Simukufunikira kusankha pa zinthu ziwirizi. Mukhoza kukhulupirira zonse ziwiri.”
Mwano Kuntchito
“Kuchita mwano kuntchito kungatayitse kampani nthawi, mphamvu, ndi luso,” inatero nyuzipepala ya The Wall Street Journal. Pa kafukufuku amene anafunsa anthu pafupifupi 3,000, anapeza kuti anthu oposa 90 pa 100 alionse “anachitiridwapo mwano kuntchito.” Theka la anthu amenewa anati “anawononga nthawi kuntchito chifukwa choganizira zimene zinawachitikirazo,” “anthu 25 pa 100 alionse analeka kulimbikira pantchito,” ndipo munthu mmodzi pa anthu 8 alionse anasiya ntchitoyo. Malinga ndi zimene ananena Christine Porath, pulofesa wa kayendetsedwe ka bizinesi pa yunivesite ya Southern California, “antchito akamachita ulesi, akamajomba kuntchito, ngakhalenso kuba, zonsezi zingakhale zizindikiro zoti pakampanipo anthu amachitirana mwano,” inatero nyuzipepalayo.
Mulu Waukulu wa Zinyalala za M’nyanja
Kumayambiriro kwa chaka cha 2006, mulu waukulu wa zinyalala za m’nyanja “unayenda molowera kum’mwera kumapita ku madzi ozungulira chilumba cha Hawaii, n’kumakankhira zosodzera nsomba zambiri zotayidwa ndi zinyalala za pulasitiki pa magombe a pa chilumbachi,” inatero nyuzipepala ya The Honolulu Advertiser. Madzi a panyanja amakankhira zinyalala zambiri zomwe zimayandama pa nyanja ya North Pacific ku mbali yabata ya nyanjayi, koma kunja kukakhala nyengo inayake, zinyalalazi zimakankhidwira ku Hawaii. M’chaka cha 2005, “anapeza zidutswa zoposa 2,000 za zinyalala,” kuphatikizanso maukonde oposa 100. Zinyalalazi zikhoza kuwononga zamoyo za m’nyanja. Charles Moore, yemwe anayambitsa bungwe la Algalita Marine Research Foundation anati: “M’nyanja mulibenso nsomba zachilengedwe. Zonse zikudya mapulasitiki.”