Kodi Tikanatani Pakadapanda Abulu?
Kodi Tikanatani Pakadapanda Abulu?
YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU ETHIOPIA
KWA zaka zambiri, abulu akhala akugwira ntchito yofunika kwambiri yonyamula anthu ndi katundu ku Addis Ababa, likulu la dziko la Ethiopia, dziko lomwe ndi la nambala 16 pamayiko amene ali ndi anthu ochuluka kwambiri padziko lonse lapansi. Oyendetsa magalimoto ambiri angofika powazolowera abulu amenewa, chifukwa amati akangosankha kolowera sabwezeka. Ngakhale kuti abulu saopa mumsewu, katundu wawo sachedwa kukola zinthu za eni, ndipo abuluwo satembenuka n’komwe. Ndiye ngati simukufuna kuti akupakeni makala, ndowe zouma, kapena chilichonse chomwe anyamula, mungangofunikira kupereka njira!
Ku Ethiopia kuli abulu okwana pafupifupi mamiliyoni asanu, kutanthauza kuti tingati anthu 12 alionse a m’dzikomo ali ndi bulu mmodzi. Anthu ambiri ku Ethiopia amakhala pamwamba, pa mapiri koma motalikiranatalikirana, ndipo zigwa n’zimene zimagawanitsa midzi yawo. Malo a ku mapiri akuluakulu athyathyathya pamwamba, a ku chigawo chapakati agawanikagawanika ndi mitsinje ing’onoing’ono. Kumanga milatho kapena misewu yafumbi kukafika kumalo amenewa si chinthu chophweka potengera chuma cha dziko ngati limeneli. Choncho, abulu n’ngofunika kwambiri pakayendedwe chifukwa n’ngopirira ndipo savutika kuyenda malo ngati amenewa.
Abulu amakwanitsa bwino kwambiri kupirira nyengo zonse za ku Ethiopia, kuyambira nyengo youma ndi yotentha ya kuzigwa mpaka nyengo ya kumapiri. Ndipo savutika kuyenda m’zitunda zotsetsereka, m’tinjira ting’onoting’ono, m’miyala ya mphepete mwa mitsinje, m’matope, ndi m’njira zina zovuta kuyendamo. Abulu amatha kuyenda m’njira zoti hatchi kapena ngamila sizingadutse. Anthu ambiri amagwiritsa ntchito bulu akafuna kunyamula katundu, makamaka ku mizinda komwe magalimoto sangafike pa nyumba zambiri.
Abulu amatha kukhota mosavuta m’makona opindika kwambiri ndipo amatha kudzipanikiza n’kuyenda m’tinjira ting’onoting’ono tam’mphepete mwa mipanda ya nyumba za anthu. Sachita kufuna matayala okwera mtengo ndipo nthawi zambiri amatha kuyenda bwinobwino ngakhale m’malo oterera. Amanyamula katundu wamng’ono ndi wamkulu
yemwe komanso wooneka mosiyanasiyana, ndipo amatha kukafika pafupifupi pakhomo lililonse kukasiya katunduyo. Abulu amatha kulowerera mosavutikira n’kudutsa mumsewu wodzadza magalimoto, panthawi imene oyendetsa magalimoto apsa mtima n’kumaimbirana mahutala mokalipa. Palibe wapolisi amene angazenge bulu mlandu ngati atalowera kumbali yolakwika yamsewu. Komanso, abulu sasowa poima ngati magalimoto. Mutha kugula bulu ndi madola a ku United States okwana 50, ndipo ngati mutayerekeza mtengo umenewu ndi mtengo wa galimoto, muona kuti bulu ndi wotchipa kwambiri!Abulu M’likulu la Dziko
M’mawa, abulu masauzande ambiri amakhala ali pamsewu kulowera ku Addis Ababa, komwe kumakhala anthu oposa 3 miliyoni, ndipo akamafika ku mzindawu amakhala atayenda makilomita oposa 25. Makamaka Lachitatu ndi Loweruka ndiye kumakhala pikitipikiti, chifukwa amenewa ndi masiku a msika. Nthawi zambiri ulendowu umatenga maola oposa atatu ndipo amafunika kunyamuka kunja kusanache. Nthawi zina, eni ake amayendera nawo limodzi abuluwa koma nthawi zambiri amachita kuwathamangira.
Nthawi zambiri abuluwa amanyamula katundu ngati matumba a mbewu, ndiwo zamasamba, nkhuni, simenti, ndi makala, komanso migolo ya mafuta ophikira ndi mabotolo a zakumwa. Abulu ena amanyamula katundu wolemera makilogalamu 90 kapena kuposerapo. Katundu wam’talim’tali, monga mapolo a nsungwi kapena bulugamu amam’mangirira cham’phepete mwawo kuti azimukoka. Mwina katundu wochititsa chidwi kwambiri ndi udzu, chifukwa abulu amati akanyamula chimulu cha udzu iwowo saoneka n’komwe.
M’mawa, abulu akanyamula katundu wolemera popita ku msika amayenda mofulumira kwambiri. Koma pobwerera kunyumba, pambuyo pogulitsa katundu wawo yense, amayenda pang’onopang’ono, mwinanso kuima kumene n’kumadya zomera m’mphepete mwa njira. Ngati sakupita kumsika, abuluwa amawagwiritsa ntchito yotunga madzi ndi kunyamula nkhuni. Nthawi zina amawabwereketsa kwa munthu wina kapena kuwachititsa hayala. Anthu ena amakhala ndi abulu ambiri amene amachitira bizinesi yonyamula anthu ndi katundu. Kumadera ena abulu amakoka ngolo, ndipo nthawi zina abulu awiri amakoka ngolo yayikulu ndithu.
N’ngofunika Kuwalemekeza
Abulu savuta kuwasamalira. Amafufuza okha chakudya chawo ndipo sasankha chakudya, moti amadya pafupifupi chilichonse. Akamasamalidwa bwino, abulu amamukonda kwambiri mbuye wawo. Akuti ali ndi nzeru zambiri kuposa mahatchi. Alinso ndi nzeru zokumbukira okha njira. Ngakhale atapanda kuwatsogolera, atha kumakatunga okha madzi pa mtunda wa makilomita oposa 8, malinga ngati kuli anthu owasenza ndi owatula kumadzi ndi kunyumbako. Zimathekanso kuwamangirira mabelu kuchitira kuti anthu okhala m’mphepete mwa njirayo azitha kudziwa kuti bulu akubwera n’kutenga katundu wawo.
Ngakhale kuti abulu amagwira ntchito molimbika, safuna kugonjera akaona kuti katundu wawalemera kapenanso akafuna kupuma. Zikatero, mwinanso katundu akakhala kuti sanamangiriridwe bwino ndipo akuwapweteka, amangogona pansi. Nthawi ngati imeneyi, anthu satha kuwamvetsa abulu, ndipo ena amawakalipira kapena kuwamenya kumene. Mungakumbukire chochitika ngati chimenechi m’Baibulo.—Numeri 22:20-31.
Abulu amafunika kuwakonda ndi kuwasamalira. Zimakhala zomvetsa chisoni akagwera m’ngalande n’kuthyoka miyendo, chifukwa choti katundu wawo sanamangidwe bwino. Zilonda, tizilombo, matenda otupa mapazi, chibayo ndi matenda ena, amafoola nyama zogwira ntchito mwakhama zimenezi. N’chifukwa chake, pafupi ndi mzinda wa Addis Ababa, ku Debre Zeyit kwatsegulidwa chipatala chamakono cha abulu. Chipatala chimenechi chili ndi makompyuta, zipinda zosamalirira abulu, maambulansi, ndi chipinda chabwino kwambiri chochitira maopaleshoni. M’chaka cha 2002, pafupifupi abulu 40,000 analandira chithandizo chosiyanasiyana ku chipatala chimenechi.
Kholo lakale Abrahamu anadutsa m’mapiri atakwera bulu wake popita ku phiri la Moriya. (Genesis 22:3) M’mbiri yonse ya mtundu wa Isiraeli, abulu anali mbali ya moyo wawo wa tsiku ndi tsiku. Ngakhale Yesu pa ulendo wake waulemerero wolowa mu Yerusalemu, anayenda pa bulu.—Mateyo 21:1-9.
Ngakhalenso ku Ethiopia, abulu anayamba kalekale kugwiritsidwa ntchito. Ndipo m’dziko limeneli, mpaka pano anthu amaonabe abulu kukhala ofunika kwambiri. Ngakhale kuti magalimoto akhala akusintha kwambiri kapangidwe kake zaka zimenezi, abulu sanasinthe, akadali chimodzimodzi. Abulu n’ngofunikadi kuwalemekeza!
[Mawu a Chithunzi patsamba 26]
‘The Donkey Sanctuary’, Sidmouth, Devon, UK