Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuchokera kwa Owerenga

Kuchokera kwa Owerenga

Kuchokera kwa Owerenga

Kodi Chikondi Chapita Kuti? (March 2006) Dziko limasokoneza tanthauzo la chikondi, ndipo Satana amafuna atachichotseratu. Nkhani ngati zimenezi zimatithandiza kukhala achikondi m’zochita zathu komanso kukhala osadzikonda. Zikomo kwambiri, mwandithandiza kumvetsa njira imene Yehova akufuna kuti tizigwiritsira ntchito khalidwe lamphamvu limeneli pamoyo wathu.

Y. B., United States

Anzanga awiri apamtima atandichokera n’kupita ku mpingo wa chinenero china, ndinkasungulumwa. Panthawi imene ndinasungulumwa kwambiri, m’pamene ndinalandira magazini imeneyi. Ndikuthokoza chifukwa chondikumbutsa mfundo yakuti, “Ngati mukufuna kuti anthu azikukondani, yambani inuyo kuwakonda.” Kuyambira panopa, ndikufuna kuti ‘ndifutukule mtima’ wanga ndipo ndikufuna kuti ndiyambe kukonda ena ndi mtima wanga wonse kuti ndikhale ndi anzanga atsopano.—2 Akorinto 6:12, 13.

M. T., Japan

Kupirira Mavuto a Ukalamba (February 2006) Nthawi zina ndimaona ngati kuti timaiwala anthu okalamba. Ndakhala ndikusamalira mwamuna wanga yemwe wakhala akudwala kwa zaka 11 tsopano. Nthawi zina ndimasungulumwabe. Ndawerenga ndi kumvetsera patepi nkhani ya mu Galamukani! imeneyi mobwerezabwereza. Ndinafunikiradi magazini imeneyi. Zikomo kwambiri.

S. T., Japan

Miyendo ndi Manja Zochita Kupanga (February 2006) Zikomo kwambiri chifukwa cha nkhani yanu yonena za miyendo ndi manja zochita kupanga. Pamene ndinali ndi pakati pa miyezi inayi, tinauzidwa kuti mwana wathu adzabadwa wopanda manja ndi miyendo ndi kuti adzachita kumuikira miyendo akadzafika chaka chimodzi. Nkhaniyi inatipeza mwezi womwe Daryl anakwanitsa chaka chimodzi. Tsopano akuphunzira kuima ndi kuyenda. Ine ndi mwamuna wanga tikuyembekezera nthawi yomwe Daryl “adzatumpha ngati nswala.”—Yesaya 35:6.

Y. A., France

Moyo N’ngokoma (November 8, 2001) Ndawerenga kambirimbiri Galamukani! ya November 8, 2001, ndipo ndimakonda kuiwerenga ndikafooka. Nkhani zoterezi zili ngati mankhwala amene satha mphamvu yake. Malangizo ndi mfundo zothetsera mavuto athu zimene mwapereka n’zothandiza kwambiri. Galamukani! imandilimbikitsa, zimene zimandichititsa kumva kuti mumaganizira anthu ngati ine. Ndine wosangalala kwambiri kuti mumatikumbutsa kuti moyo n’ngokoma!

P.  T., Madagascar

Kodi Angelezi Oyambirira Kusamukira ku America Anali Akristu Oona? (February 2006) Sindinasangalale ndi mmene munafotokozera mfundo zanu mu nkhani imeneyi. Pali chifukwa chachikulu chimene chimachititsa amwenye a ku North America kuti asamakondwerere Tchuthi Choyamikira koma inu simunafotokoze mfundo imeneyi momveka bwino.

Dzina labisidwa, United States

Galamukani!” ikuyankha: Tikukupemphani kumvetsa kuti cholinga chathu polemba nkhaniyi sichinali chofotokoza mwatsatanetsatane mbiri ya Tsiku la Tchuthi Choyamikira. Mabuku ambiri, kuphatikizapo la “Encyclopædia Britannica” amati, cha kumapeto kwa chaka cha 1621, Aulendo anasangalalira pamodzi ndi amwenye a ku America kwa masiku atatu. Zimenezi zatchulidwa m’kalata yolembedwa ndi Edward Winslow ya pa December 11, 1621. Komabe, m’zaka zotsatira anthu ankakondwerera tchuthi choyamikira pokumbukiranso zinthu zina kuphatikizapo kukolola. Mwambo woipa kwambiri wokondwerera tchuthi choyamikira ndi umene unakonzedwa mu 1637 ndi Bwanamkubwa John Winthrop wa ku Massachusetts Bay Colony pambuyo pa kuphedwa kwa Amwenye ambirimbiri otchedwa a Pequot. Choncho tikumvetsa chifukwa chake owerenga ena sangasangalale kumva za Tsiku la Tchuthi Choyamikira.