Zochitika Padzikoli
Zochitika Padzikoli
▪ “Pakati pa anthu okwatirana, akuti oposa theka ‘amakhala osakhulupirika kwa mnzawoyo pa nkhani ya ndalama’ ndipo amamunamiza pa ndalama zimene awononga.”—THE WALL STREET JOURNAL, U.S.A.
▪ “Malo aakulu kwambiri ku Greece, okwana 84 peresenti ya nthaka yonse ya m’dzikolo, ali pangozi yoti akhoza kusanduka chipululu ndipo ena okwana 8 peresenti asanduka kale chipululu.”—KATHIMERINI, GREECE.
▪ Mudzi wotchedwa Lateu, pa chilumba cha Tegua, mu mzinda wa Vanuatu m’dera limene limatchedwa Oceania, mwina ukhala mudzi woyamba kuusiya wabwinja, kapena kuti kuusamutsira kwina chifukwa cha kusintha kwa nyengo. Nyumba zakumeneko zakhala “zikumizidwa mobwerezabwereza ndi madzi kukaomba mphepo kapena kukakhala mafunde amphamvu.”—VANUATU NEWS, VANUATU.
Anthu Ambiri Akukwanitsa Zaka 100
Magazini ya New Scientist yanena kuti masiku ano sizachilendonso kuti munthu akwanitse zaka 100 ali ndi moyo. Pakali pano, padziko lonse pali pafupifupi anthu 200,000 amene akwanitsa kale zaka 100. Magaziniyi yatinso anthu 66 pa anthu amenewa apitirira kale zaka 110. Magazini ya New Scientist ikuvomereza kuti, kutsimikizira nkhani zonena za anthu amene akhala ndi moyo wautali kwambiri n’kovuta, koma “kusowa kwa umboni wodalirika wolembedwa kukutanthauzanso kuti chiwerengero cha anthu amene akwanitsa zaka 110 chitha kufika 450 masiku ano.”
Mlili Umene Unapha Anthu Wadziwika
Magazini ya ku Canada yotchedwa Maclean’s, inati: “Maselo a m’mano otengedwa m’manda ena ku Athens athandiza kutulukira” mlili umene unapha anthu zaka zamakedzana. M’buku lake lakuti History of the Peloponnesian War, mlembi wa Chigiriki wotchedwa Thucydides, anatchula za mlili umene unapululutsa anthu mu mzinda wa Athens m’chaka cha 430 B.C.E., umenenso unachititsa kuti mzinda wa Athens ugonjetsedwe ndi mzinda wa Sparta pa nkhondo ya pakati pa mizinda iwiriyo. Malinga ndi mmene Thucydides anafotokozera nkhaniyo, zinali zovuta kudziwa kuti unali mlili wanji. Koma tsopano, ataunika mnofu wa mkati mwa dzino umene umatha kusunga tizilombo toyambitsa matenda kwa zaka zambiri, akuti anatha kudziwa kuti mlili wakupha womwe sunkadziwika umenewu ndi nthenda ya tayifodi.
Zidole Zoyendetsa Ngamila
Zinali zokayikitsa ngati mpikisano wothamanga ndi ngamila, umene n’ngotchuka kwambiri ku mayiko a ku Persian Gulf, ungapitirire pamene magulu omenyera ufulu wa anthu anatsutsa kugwiritsa ntchito ana kuti aziyendetsa ngamila. Komabe, akatswiri ena akuti ngamila ziyenera kuyendetsedwa ndi chinthu cholemera makilogalamu osapitirira 27, zimene zikutanthauza kuti ngakhale achinyamata si oyenerera kuyendetsa ngamila. Ndiyeno yankho lake lingakhale chiyani? Zidole zoyendetsa ngamila. Akatswiri opanga zinthu a ku Switzerland, apanga kachidole kolemera makilogalamu osapitirira 27, koyendera limoti koti kazikhala pa msana wa ngamila. Kuti kasamaopseze ngamila, kachidoleka akapanga ngati munthu ndipo kazilankhulanso ngati munthu. Kazithanso kuwerama, kukhazikika bwino kakafuna kugwa, kugwiritsa ntchito chikwapu, ndi kuwongolera ngamila. Eniake a ngamila akuona kuti kugwiritsa ntchito kachidoleka kuwathandiza.
Njere Imera Patatha zaka 2,000
Migwalangwa yakale ya ku Yudeya yomwe inali yofunikira kwambiri chifukwa cha kukongola kwake, mthunzi wake, yomwenso ankaigwiritsa ntchito ngati mankhwala, inawonongedwa pa nkhondo ya pakati pa Akhristu ndi Asilamu m’zaka za m’ma 500 mpaka m’ma 1500. Koma panopa, malinga ndi kunena kwa nyuzipepala ya New York Times, “akatswiri ena ophunzira kwambiri ku Israel akwanitsa kumeretsa njere ya mgwalangwa yomwe yakhalako zaka 2, 000. Akuti “njere imeneyi, yomwe anaipatsa dzina loselewula lakuti Metusela, inakumbidwa m’nthaka ku Masada,” yomwe ndi nyumba yapaphiri yokhala ndi malinga imene inagonjetsedwa ndi Aroma mu 73 C.E. Katswiri wina wa ulimi wa kumalo opanda madzi, dzina lake Dr. Elaine Solowey, amene anagwira ntchito yomeretsa njereyi, akuti zitenga zaka ndithu kamtengo ka mgwalangwa kameneka kasanayambe kubereka zipatso, ndipo zitengeranso ngati kali kakakazi. Akuti “ngati kali kakamuna, kadzangokhala ngati maluwa ochititsa chidwi basi.”