Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Chikhristu Chalephera Kusintha Zinthu?

Kodi Chikhristu Chalephera Kusintha Zinthu?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Chikhristu Chalephera Kusintha Zinthu?

PAFUPIFUPI munthu mmodzi aliyense pa anthu atatu padziko lonse amati ndi Mkhristu. Koma zikuoneka kuti, kuposa kale lonse, dziko lagawikana kwambiri pazandale ndipo ziwawa nazo zachuluka kwambiri. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Chikhristu chimene Yesu anaphunzitsa chili ndi vuto penapake? Kapena, kodi vuto ndi njira imene anthu ambiri amagwiritsa ntchito potsatira ziphunzitso za Khristu?

Nkhani ino ifotokoza zimene kwenikweni Khristu anaphunzitsa ndi chitsanzo chimene anasiyira anthu om’tsatira. Ifotokozanso maganizo enaake ofala pakati pa anthu ambiri amene amati ndi Akhristu; maganizo omwe kwenikweni ali otsutsana ndi tanthauzo lenileni la Chikhristu.

Chikhristu Chachinyengo

Patatha zaka zambiri Khristu atafa, anthu a mu Ufumu wa Aroma anayamba kukonda Chikhristu chinachake chachinyengo. Popeza kuti tsopano sanalinso anthu akunja osavomerezeka, posakhalitsa anthu otsatira Chikhristu chimenechi anapezeka kuti ayamba kukhala ndi mphamvu pa zandale ndi zachikhalidwe cha anthu mu ufumuwo. Atsogoleri atchalitchi, monga Augustine, anayamba kuphunzitsa ziphunzitso zoti zigwirizane ndi kusintha kwa zinthuku, motero ankaphunzitsa kuti Ufumu wa Mulungu, umene anthu anali kudikirira, unali utafika panthawiyo. Aphunzitsi amenewa ankaphunzitsa kuti ulamuliro ndiponso mphamvu zimene anali atangozipezazo ndizo zidzakwaniritse chifuniro cha Mulungu padziko lapansi. Motero, anagogomezera kwambiri mfundo yakuti anthu ndiwo ayenera kuyendetsa zinthu padziko lonse.

Chifukwa cha zimenezi, anthu ambiri akhala akukhulupirira kuti Mkhristu aliyense ali ndi udindo wake pa kayendetsedwe ka nkhani zandale. Ambiri amakhulupirira kuti, kuti Mkhristu akwaniritse mbali yakeyo, amayenera kuti nthawi zina azisiya kaye mbali zinazake za chikhulupiriro chake pofuna kuchita zimene anthu a kuderalo akufuna. Mwachitsanzo, anthu ambiri amanena mwa mawu okha kuti amakhulupirira zimene Khristu anaphunzitsa pa nkhani ya chikondi ndi mtendere, koma panthawi yomweyo amachita nawo nkhondo. Pachifukwa chomwechi, matchalitchi amatha kulimbikitsa anthu awo kuti azipempherera Ufumu wa Mulungu koma panthawi yomweyo akuchirikiza atsogoleri ankhanza.

Chikhristu chachinyengochi si chimene Yesu anakhazikitsa ayi. Chimenechi ndi Chikhristu chochita kupangidwa ndi anthu ndipo n’chimene ambiri amene amati ndi Akhristu masiku ano amatsatira. Chikhristuchi chalepheradi kusintha zinthu monga mmene tikuonera masiku ano, chifukwa m’matchalitchi ambiri achikhristu, anthu ambiri sakutsatira mfundo za m’Baibulo.

Kodi Yesu Anaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?

Ena angadabwe kumva kuti, kwenikweni Yesu anauza ophunzira ake kuti ‘asakhale mbali ya dziko, monganso iye sanali mbali ya dziko.’ (Yohane 17:15, 16) N’chifukwa chiyani Khristu analimbikitsa ophunzira ake kuchita zimenezi? Yohane, yemwe anali wophunzira wokondedwa wa Yesu, anayankha funsoli polemba kuti: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.”—1 Yohane 5:19.

Motero, ziphunzitso za Khristu siziuza anthu kuti mabungwe a anthu ndiwo adzabweretse dziko lolungama, koma zimati Ufumu wa Mulungu wakumwamba ndiwo udzatero. (Mateyo 6:10) Yesu mwiniwake sanasonyeze ngakhale pang’ono kuti anafunapo kulowerera m’nkhani zokonza zinthu m’nthawi yake. Anakana momveka bwino kuti sakufuna udindo wandale. (Yohane 6:15) Analetsanso kuchita zachiwawa pofuna kuthetsa mikangano. (Mateyo 26:50-53; Yohane 18:36) Yesu sanasiye buku lililonse la malamulo oyendetsera boma kapena mfundo zinazake za ufulu wa anthu. Sanatchulepo maganizo ake alionse pa nkhani zandale za m’nthawi yake. Mwachitsanzo, sanalimbane n’zomenyera ufulu wa akapolo a m’nthawi yake, ndipo sanalowererepo pa nthawi imene Ayuda amalimbana ndi Aroma.

Koma zimenezi sizikutanthauza kuti Yesu sankaganizira anthu pamavuto awo. Yesu anaphunzitsa zinthu zambiri zokhudza udindo wa munthu kwa munthu mnzake. Analimbikitsa kukhala oona mtima podula msonkho ndipo anagogomezera kuti kugonjera kwa anthu oikidwa pa udindo wovomerezeka n’kofunika kwambiri. (Mateyo 22:17-21) Iye anaphunzitsa mmene tingasonyezere kuti tikuganizira anthu ofunika thandizo. Anaphunzitsanso mmene tingalemekezere anthu ena ndi mmene tingakhalire anthu okoma mtima, achifundo ndi okhululuka. (Mateyo, chaputala 5 mpaka 7) Aliyense akudziwa kuti mfundo imene Khristu anaigomezera kwambiri ndi ya kukonda Mulungu ndi kukonda anthu anzathu.—Maliko 12:30, 31.

Chikhristu Choona cha Masiku Ano

Ndiyeno kodi wotsatira woona wa Khristu ayenera kuchita zinthu m’njira yotani? Ayenera kuchita zinthu mmene Yesu ankachitira. Ayenera kutsatira mokhulupirika malamulo a m’dziko limene akukhala, koma sayenera kulowerera m’nkhani zandale. (Yohane 12:47, 48) Iye sangasiye kutsatira mfundo zachikhristu, ngakhale zitavuta bwanji. (1 Petulo 2:21-23) Komabe, sayenera kupinda manja n’kumangoyang’ana zinthu zikuchitika. Mkhristu woona ayenera kukhala munthu wofunitsitsa kuthandiza anthu anzake, monga anachitira Yesu. (Maliko 6:34) Ayeneranso kuchita khama pothandiza anthu anzake kuti azikhala moyo wosangalala ndipo azitero powathandiza kumvetsetsa ndi kutsatira ziphunzitso za Khristu.—Yohane 13:17.

Mogwirizana ndi zimenezi, Mboni za Yehova masiku ano zakuyesetsa kutsatira Khristu pankhani ya ubwenzi wawo ndi dziko. Iwo ndi nzika zokonda mtendere ndiponso zomvera malamulo, koma sakhala mbali ya dziko. Monga anachitira Yesu, iwo amakana kuchita nawo zachiwawa ndiponso mikangano ya zandale imene yafala masiku anoyi. Amayembekeza Ufumu wa Mulungu ndi mtima wawo wonse podziwa kuti ndiwo udzathetse mavuto m’dzikoli. Chikhristu choona chimathandiza munthu kukhala moyo wosangalala ndipo chimathandiza anthu ake kukhala mogwirizana. (Yohane 13:34, 35) Ndithu, Chikhristu chotere sichinalephere kusintha zinthu.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ Kodi ndi bwino kuti Akhristu azichita nawo zandale?—Yohane 6:15.

▪ Kodi Khristu analimbikitsa anthu kuti chiwawa ndi njira yabwino yothetsera mikangano?—Mateyo 26:50-53.

▪ Kodi chizindikiro cha Chikhristu choona n’chiyani?—Yohane 13:34, 35.

[Mawu a Chithunzi patsamba 18]

EL COMERCIO, Quito, Ecuador