Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Matenda Onse Adzatha!

Matenda Onse Adzatha!

Matenda Onse Adzatha!

ANTHU ambiri amakhulupirira kuti moyo uno ukadzatha, adzakakhala ndi moyo wopanda zopweteka ndiponso matenda, kumwamba. Koma mosiyana ndi chikhulupiriro chotchukachi, chiyembekezo chenicheni chopezeka m’Baibulo n’choti anthu adzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi pano m’paradaiso. (Salmo 37:11; 115:16) Malonjezo a m’tsogolo amenewa akuphatikizapo moyo wopanda matenda, wachimwemwe, ndiponso wosatha.

N’chifukwa chiyani timadwala ndi kufa? Ndipo zidzatheka bwanji kuti dziko likhale lopanda matenda? Baibulo limayankha mafunso amenewa.

Chifukwa chenicheni chimene chimayambitsa matenda Makolo anthu oyambirira, Adamu ndi Hava, analengedwa ndi matupi angwiro. (Genesis 1:31; Deuteronomo 32:4) Anawalenga m’njira yakuti akhale ndi moyo kosatha. Koma matupi awo anakhala opanda ungwiro pamene analakwira Mulungu mwadala. (Genesis 3:17-19) Popeza anakana ulamuliro wa Mulungu, iwo anadula ubwenzi wawo ndi Mlengi, yemwe ndi Gwero la moyo wangwiro. Potero, anadzipatsa nthenya. Anayamba kudwala ndi kumwalira, mogwirizana ndi mmene Mulungu anawachenjezera.—Genesis 2:16, 17; 5:5.

Pambuyo poti Adamu ndi Hava apanduka, zomwe akanatha kupatsira kwa ana awo ndi kupanda ungwiro basi. (Aroma 5:12) Monga mmene talongosolera m’nkhani yapitayi, asayansi masiku ano amazindikira kuti pali zinthu zina zake zochita kuyamwira zimene zimachititsa kuti tizidwala ndi kufa. Ndipotu pambuyo pochita kafukufuku kwanthawi yaitali, gulu lina la asayansi lanena kuti: “Mfundo yosatsutsika yokhudza moyo ndi yoti, chinthu chamoyo chikangobadwa, m’thupi la chinthucho mumachitika zinthu zimene zimawononga thupilo.”

Si anthu amene angathetse matenda Kupita patsogolo kwa sayansi kukuthandiza kwambiri pantchito yolimbana ndi matenda. Komano asayansi sangathetseretu matenda chifukwa sakudziwa bwinobwino chimene chimayambitsa matendawo. Zimenezi sizodabwitsa kwa ophunzira Baibulo amene akudziwa bwino mawu ouziridwa a Mulungu oti: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye.”—Salmo 146:3.

Komabe monga mmene Baibulo limanenera, “zinthu zosatheka kwa anthu n’zotheka ndi Mulungu.” (Luka 18:27) Yehova Mulungu angathe kuchotsa chimene chimayambitsa matenda. Iye adzathetsa matenda athu onse. (Salmo 103:3) Mawu ake ouziridwa amalonjeza kuti: “Taonani! chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu. Iye adzakhala pamodzi nawo, ndipo iwo adzakhala anthu ake. Inde, Mulungu mwini adzakhala nawo. Iye adzapukuta msozi uliwonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4.

Zimene muyenera kuchita Yesu Khristu analongosola momveka bwino zimene tiyenera kuchita kuti tidzakhale m’dziko lopanda matenda lomwe lili m’tsogolomu. Iye anati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekha woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munam’tuma.”—Yohane 17:3.

Kudzera m’Baibulo, tingadziwe Mulungu ndiponso zinthu zimene Mwana wake, Yesu Khristu anaphunzitsa. Kudziwa zinthu zimenezi kumaphatikizaponso kudziwa malangizo othandiza amene angakupindulitseni panopa. Komanso phindu lalikulu kwambiri ndi lakuti, Mulungu akulonjeza anthu ake kuti m’dziko limene likubwera simudzakhala zopweteka zilizonse. Ndithudi, Mulungu akukulonjezani dziko limene “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.”—Yesaya 33:24.

[Bokosi/Zithunzi patsamba 11]

Nkhani Yathanzi Tiziiona Bwino

Baibulo limalimbikitsa kulemekeza moyo. Mboni za Yehova zimasonyeza kulemekeza moyo mwa kuyesetsa kusamalira moyo wawo. Mbonizo zimapewa zinthu zovulaza monga kugwiritsira ntchito mankhwala osokoneza bongo ndi kusuta fodya. Ndiponso Mulungu safuna kuti olambira ake akhale omwa mowa kwambiri, ndiponso osusuka ndi kudya kwambiri. (Miyambo 23:20; Tito 2:2, 3) Kupewa zinthu zimenezi, komanso kupumula mokwanira ndi kuchita masewera olimbitsa thupi, kungathandize kuchepetsa kapena kupewa matenda ambiri. Koma anthu amene akudwala angafunike kuthandizidwa ndi madokotala odalirika.

Baibulo limalimbikitsa anthu kukhala odekha ndi “a maganizo abwino.” (Tito 2:12, Afilipi 4:5) Anthu ambiri masiku ano amaiona mopambanitsa nkhani ya thanzi lawo ndipo amatanganidwa kwambiri ndi kufufuza njira zochizira matenda, ngakhale zitakhala zowononga moyo wawo wauzimu. Ena amatsata njira zokayikitsa, zomwe zingawavulaze. Ndipo anthu ena amawononga ndalama ndiponso nthawi pofunafuna thandizo la mankhwala osathandiza, kapena oopsa kumene.

Zoona zake n’zakuti m’nthawi inoyi, sizingatheke kukhala ndi moyo wopanda matenda alionse. Koma pamene mukudikirira moyo wa m’tsogolo wopanda matenda, malangizo anzeru amene ali m’Baibulo angakuthandizeni kuti mukhale wosamala kwambiri pamene mukufufuza chithandizo cha mankhwala.