Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Pa miyezi 15 yokha, kwapezeka makanda 82 atatayidwa mumsewu ku Mexico City, ndipo makanda 27 pa makanda amenewa anali akufa.Zachokera m’nyuzipepala ya EL UNIVERSAL, KU MEXICO.

Atafufuza m’mapanga a ku malo awiri a ku California, m’dziko la United States, anapezako mitundu 27 yatsopano ya nyama. Joel Despain, yemwe ndi katswiri wofufuza m’mapanga m’bungwe la National Park Service anati: “Zimenezi zikungotsimikizira kuti tikudziwa zinthu zochepa chabe za padzikoli.”—Zachokera m’magazini ya SMITHSONIAN, KU UNITED STATES

Anthu 20 pa anthu 100 alionse padziko lonse akusowa madzi akumwa abwino. Anthu 40 pa anthu 100 alionse alibe zinthu zofunikira pa moyo waukhondo.—Zachokera m’nyuzipepala ya MILENIO, KU MEXICO.

M’nkhalango ya zachilengedwe ya Serengeti yokha mumaphedwa nyama 20,000 kapena 30,000 chaka chilichonse ndi anthu opha nyama mosaloledwa ndi boma.—Zachokera m’nyuzipepala ya THE DAILY NEWS, KU TANZANIA.

Atafufuza mumzinda wa Barcelona, ku Spain, apeza kuti mwana mmodzi pa ana atatu alionse a zaka 16 amasuta chamba nthawi zambiri.—Zachokera m’nyuzipepala ya LA VANGUARDIA, KU SPAIN.

Majeremusi Muofesi

Akatswiri a sayansi ya tizilombo tosaoneka ndi maso a pa yunivesite ya Arizona anapita m’mizinda ingapo ya ku America n’kuyeza kuchuluka kwa majeremusi amene amapezeka m’maofesi. Nyuzipepala ya Globe and Mail inati asayansiwo anapeza kuti “malo asanu amene mumakhala majeremusi ambiri koposa ndi awa: Oyamba ndi foni, kenako pamwamba pa desiki, zotsegulira mipopi, zotsegulira khomo la maikulowevu ndipo otsiriza ndiwo potaipira kapena kuti kiyibodi.” Lipotili linati: “Pamwamba pa madesiki ambiri pamakhala majeremusi ochuluka kuwirikiza ka 100 poyerekezera ndi pamwamba pa tebulo la m’khitchini kapena kuwirikiza ka 400 poyerekezera ndi pokhalira pa zimbuzi zambiri zogejemula.

“Akhristu M’mawu Okha”

Dziko la Philippines ndi limene amalitcha kuti dziko lokhalo “lachikhristu” ku Asia konse. Komabe, Bishopu Efraim Tendero wa bungwe la Philippine Council of Evangelical Churches anati: “Ambirife ndife Akhristu m’mawu okha koma osati m’zochita zathu.” Nyuzipepala ya Manila Bulletin, inati chifukwa chimodzi chimene chimachititsa zimenezi n’choti atsogoleri amatchalitchi “amalephera kuphunzitsa anthu kudziwa Baibulo ndi kuona kufunika kwake.” Akuti ulaliki wina kutchalitchi umangokhala wonena za ndale basi osati za Malemba.

Anthu ndi Nyama Akulimbanirana Chakudya

Nyuzipepala ya ku Nairobi ya The East African, inati: “Tayamba kulandira nkhani zambiri zonena kuti anyani ndi afisi akuvutitsa anthu ku Somalia, komwe kuli chilala.” Nthawi ina anthu ndi anyani ankalimbanirana madzi moti anyani angapo anaphedwa ndipo abusa ena aziweto anavulala. Akuti magulu a anyani amadikirira “m’mphambano zinazake za misewu kapena m’milatho inayake” pofuna kuti abe zakudya zimene galimoto zikuluzikulu zimanyamula popita kumisika. Nyuzipepalayo inati: “Si zodabwitsa kuona nyama zakutchire zikuthawa ndi phava la nthochi kapena mavwende [akuluakulu].”

Sitima Zam’madzi Zikusokoneza Nyengo ya Kumadera a M’mphepete mwa Nyanja

Nyuzipepala ya ku Germany ya Kölner Stadt-Anzeiger inati sitima ndi maboti zikusokoneza nyengo ya kumadera a m’mphepete mwa nyanja komwe kumadutsa sitima ndi maboti ambiri. Anthu ofufuza zanyengo m’bungwe la Max Planck Institute for Meteorology, ku Hamburg, anaunika kumwamba, pa nyanja ya English Channel, kuti aone kupangika kwa mabingu. Atatero anapeza kuti masiku ano, kumadera a m’mphepete mwa nyanja, mabingu ayamba kupangika ochepa, pamene kumadera amene kuli njira zodutsa sitima zapamadzi kwayamba kupangika mabingu ambiri. Akuti zimenezi zikuchitika chifukwa cha utsi umene sitima zapamadzi zimatulutsa. Akuti utsiwo umakoka thunzi n’kuchititsa kuti papangike timadontho tambirimbiri tamadzi. Nyuzipepalayo inati: “Sitima zayamba kugwiritsira ntchito mafuta ochuluka mowirikiza kanayi poyerekezera ndi mmene zinthu zinalili zaka 50 zapitazo.”