Bwanji Zolumbira Kukhala Odzisunga?
Bwanji Zolumbira Kukhala Odzisunga?
M’ZAKA zochepa zapitazi, achinyamata ambiri akhala akulumbira kuti sadzagonana ndi wina aliyense asanalowe m’banja, kapena kuti adzakhalabe odzisunga, ndipo kawirikawiri amanena kuti, “Sindidzagonana ndi wina aliyense mpaka ndidzalowe m’banja.” Kulumbira kotereku kumasonyeza kuti achinyamatawo ali ndi zolinga zabwino ndipo kumagwirizana ndi malamulo a m’Baibulo. (1 Akorinto 6:18; Aefeso 5:5) Komabe, n’zokayikitsa ngati kulumbira kotero kukuthandiza achinyamatawo. Malinga ndi kafukufuku wina, pafupifupi achinyamata 60 pa 100 aliwonse amene analumbira anaphwanya lumbirolo chaka chisanathe n’komwe.
Kuwonjezera pamenepo, pali vuto lina lakuti achinyamata ena samvetsa tanthauzo la kukhala “odzisunga” ndiponso “kusagonana ndi wina aliyense mpaka kudzalowa m’banja.” Charlene C. Giannetti ndi Margaret Sagarese, analemba m’buku lawo lonena za atsikana ofuna kwambiri anyamata lotchedwa Boy Crazy! kuti: “Akatswiri akuona kuti khalidwe logonana m’kamwa, ngakhalenso kugonana kumbuyo lafala chifukwa cha achinyamata amene amafuna kuti ‘azidziwikabe’ kuti sanagonanepo ndi wina aliyense. Achinyamatawa amaganiza kuti ngati sanagonane m’njira yachilengedwe, ndiye kuti kwenikweni sanagonane ayi.”
Ndipo zikuonekeratu kuti maganizo amenewo n’ngofala. Atafunsa achinyamata oposa 1,000, wolemba mabuku wina anati: “Zikuoneka kuti mwina wachinyamata mmodzi kapena awiri okha pa 100 aliwonse ndi amene amaona kuti kugonana m’kamwa n’kugonana ndithu.” Ndipo anawonjezera kuti: “Ngati ndinu kholo, zindikirani kuti mwina mwana wanu amaganiza m’njira imeneyi, kaya ali zaka zopitirira 12 kapena ngakhale ngati sanafike zaka zimenezi.”
Anthu amene amatsatira mfundo za m’Baibulo amazindikira kuti kaya ndi kugonana m’kamwa kaya ndi kugonana kumbuyo, konseko n’kugonana basi. Baibulo limanena kuti tiyenera “kupewa dama,” zimene zimaphatikizapo mtundu uliwonse wa kugonana koswa lamulo la Mulungu.—1 Atesalonika 4:3.