Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Chikhristu Chili ndi Tsogolo Lotani?

Kodi Chikhristu Chili ndi Tsogolo Lotani?

Kodi Chikhristu Chili ndi Tsogolo Lotani?

KODI anthu onse padzikoli adzatembenuka n’kukhala Akhristu, kapena kodi Chikhristu chidzatha? Kodi Chikhristu chikanali nyali yowala m’dziko lamdima, kapena kodi chinadetsedwa? Awa ndi mafunso amene tiyenera kuwaganizira ngakhale masiku ano.

Pogwiritsira ntchito fanizo losavuta kumvetsa, Yesu anasonyeza kuti Iye atadzala mbewu za Chikhristu, mdani, yemwe ndi Satana, adzachita zosokoneza. (Mateyo 13:24, 25) Motero, sikuti kusintha kwa moyo wa anthu n’komwe kwachititsa kuti Chikhristu chisokonezeke zaka mahandiredi angapo pambuyo pa utumiki wa Yesu. Ayi, koma n’chifukwa cha zochita za mdani, Satana. Masiku ano matchalitchi a Chikhristu akupitiriza zolakwa zomwe zinayamba kalekale ndipo akukolola zimene akufesa.—2 Akorinto 11:14, 15; Yakobo 4:4.

Chiwembu Chosokoneza Chikhristu

Yesu analosera kuti ziphunzitso zake zidzasokonezedwa. Iye anati: “Ufumu wa kumwamba uli ngati munthu amene anafesa mbewu zabwino m’munda wake. Koma anthu ali m’tulo, kunabwera mdani wake ndi kudzafesa udzu m’munda wa tiriguwo, ndi kuchoka.” Antchito atauza mbuye wawoyo za zoipa zimene mdani uja anachita n’kupempha kuti akazule udzuwo, n’zodabwitsa kuti munthuyo anawayankha kuti: “Ayi; kuopera kuti mwina pozula udzu, mungazule pamodzi ndi tirigu. Zilekeni zonse zikulire pamodzi mpaka nthawi yokolola; ndipo m’nyengo yokolola ndidzauza okololawo kuti, Choyamba sonkhanitsani udzu ndi kuumanga m’mitolo kuti ukatenthedwe, ndipo mukatha mupite kukasonkhanitsa tirigu ndi kumuika m’nkhokwe yanga.”—Mateyo 13:24-30.

Monga mmene Yesu mwini anafotokozera, m’fanizo lakelo munthu amene anafesa tirigu m’munda akuimira Yesu yemweyo, ndipo mbewu zimene anafesa zikuimira Akhristu oona. Mdani amene anafesa udzu m’mbewu za tiriguzo akuimira “Mdyerekezi.” Udzu ukuimira anthu osamvera lamulo, anthu ampatuko amene amanamizira kuti ndi atumiki a Mulungu. (Mateyo 13:36-42) Mtumwi Paulo anatchulapo zinthu zinanso zimene zidzachitike. Iye anati: “Ndikudziwa kuti ine ndikachoka, mimbulu yopondereza idzalowa pakati panu ndipo siidzasamalira gulu la nkhosa mwachikondi. Ndipo pakati pa inu nomwe padzauka anthu amene adzayamba kulankhula zinthu zopotoka kuti akanganule ophunzira aziwatsatira.”—Machitidwe 20:29, 30.

Chikhristu Chisokonezedwa

Kodi fanizo limene Yesu anapereka ndiponso zimene Paulo analosera zinakwaniritsidwa? Inde zinakwaniritsidwadi. Anthu ongofuna maudindo anakula mphamvu mumpingo umene Yesu anakhazikitsa ndipo anaugwiritsa ntchito m’njira yowakomera iwowo. Yesu anali atauza ophunzira ake kuti: “simuli mbali ya dzikoli.” (Yohane 15:19) Komabe, amuna ongofuna mphamvu basi anagwirizana ndi olamulira n’kupanga matchalitchi ochirikizidwa ndi boma ndipo matchalitchiwa anapeza mphamvu ndiponso chuma chadzaoneni. Matchalitchiwa ankaphunzitsa “zopotoka.” Mwachitsanzo, ankaphunzitsa anthu kuti azilambira boma ndi kupereka moyo wawo ku boma pomenya nkhondo. Motero, anthu amenewa, omwe ankadzitcha kuti ndi Akhristu, anachita nawo nkhondo zomenyana ndi Asilamu n’kupha anthu amene ankaona kuti n’ngosakhulupirira. Ankapitanso ku nkhondo n’kumakapha anthu amene ankati ndi “abale” awo a chipembedzo chawo chomwecho. Ndithu, anthu amenewa anakanika kutsatira khalidwe lachikhristu losalowerera pankhondo ndiponso lokonda anansiwo.—Mateyo 22:37-39; Yohane 15:19; 2 Akorinto 10:3-5; 1 Yohane 4:8, 11.

N’zoonekeratu kuti matchalitchi amene kwa zaka zambiri akhala akudzitcha kuti ndi achikristu, kwenikweni Chikhristu chawo n’chonyenga. Zimenezi zingatithandize kumvetsa zimene tanena m’nkhani yam’mbuyo ija, zoti matchalitchi akugawanika n’kukhala timagulu tosiyanasiyana, akulowerera m’ndale, ndipo sakutsatira malamulo a Mulungu. Zipatso zoipa zimenezi si za Chikhristu choona ayi, koma n’za Chikhristu chonyenga, chimene chinadzalidwa ndi Mdyerekezi. Kodi zipembedzo zonyengazi zikulowera kuti? Monga Yesu anasonyezera m’fanizo lake lija, sikuti zidzangotha zokha chifukwa chosowa anthu ayi. Zidzachita kuweruzidwa ndi kuwonongedwa.

Akhristu Oona Akuwala Mumdima

Komabe, “udzu” wa Chikhristu chonyenga usanasonkhanitsidwe pamodzi n’kuwonongedwa, fanizo la Yesu lija likusonyeza kuti payenera kuchitika kaye chinachake. Kwa zaka mahandiredi ambiri “udzu” wa Chikhristu chonyenga unakula kwadzaoneni moti “tirigu” wa Chikhristu sankaoneka kwenikweni. Koma Yesu analongosola kuti tiriguyo adzam’siyanitsa ndi udzu pa nthawi ya “kukolola,” imene Yesuyo anati ikuimira ‘mapeto a dongosolo la zinthu.’ Yesu anatinso: “Panthawi imeneyo olungama adzawala ngwee ngati dzuwa.” (Mateyo 13:39-43) Pali umboni wosonyeza kuti takhala m’nthawi ya mapeto a dongosolo lino la zinthu kuyambira m’nthawi ya nkhondo yoyamba ya padziko lonse, yomwe inachitika zaka zoposa 90 zapitazo. (Mateyo 24:3, 7-12) Kodi mbali imeneyi ya fanizo laulosi la Yesu yakwaniritsidwanso?

Akhristu oona apatulidwa pa “udzu” wa matchalitchi achikristu. Mboni za Yehova ‘zikuwala ngwee ngati dzuwa,’ pothandiza ena kudziwa Mulungu woona, Yehova. Mbonizi sizilowetsa pansi miyezo ya Yehova. M’malo mwake, anthu amene amakhala Mboni za Yehova nthawi zambiri amafunika kusintha m’zinthu zambiri pamoyo wawo kuti amvere mfundo zachikhristu zopezeka m’Baibulo.

A Mboni za Yehova sachita zinthu zongosangalatsa anthu pamisonkhano yawo, koma amachititsa maphunziro aulere a Baibulo. Komanso amasonyeza ena chikondi ndi ubwenzi, ndipo makhalidwewa amawaphunzira m’Malemba. Iwo amakhulupirira kuti Mulungu adzasintha dzikoli kuti likhale paradaiso ndipo adzaonetsetsa kuti mukhale anthu ofatsa a padziko lapansi, monga mmene anafunira pachiyambi pomwe. Koma choyamba, dzikoli lidzafunika kuchotsamo zoipa zonse zobwera chifukwa cha zochita za zipembedzo zonyenga, zomwe m’Baibulo zimadziwika ndi dzina lakuti Babulo Wamkulu. Ulosi wa m’Baibulo umasonyeza kuti, posachedwa pompa Yehova asintha zinthu m’njira yaikulu imeneyi.—Mateyo 5:5; Chivumbulutso 18:9, 10, 21.

Anthu onse omvera akadzamasulidwa ku miyambo yosocheretsa ya zipembedzo zonyenga, kulambira koona kwachikhristu kudzagwirizanitsa anthu onse okhala padziko lapansi. Ilitu ndi tsogolo labwino kwambiri la mbewu ya Chikhristu choona imene Yesu anadzala. Paradaiso wa mu Edeni uja adzabwezeretsedwa m’dziko lomwe lidzakhale lamtendere, ndipo sipadzakhala zipembedzo zogawanitsa anthu zoti zidzafesenso mbewu zoyambitsa kusamvana.

[Chithunzi patsamba 7]

“Kunabwera mdani wake ndi kudzafesa udzu m’munda wa tiriguwo.”—Mateyo 13:25

[Zithunzi pamasamba 8, 9]

Tikukuitanani mwachikondi kuti mudzabwere ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova ina iliyonse, kumene amachita maphunziro aulere a Baibulo

[Chithunzi patsamba 9]

“Mukatha mupite kukasonkhanitsa tirigu ndi kumuika m’nkhokwe yanga.”—Mateyo 13:30