Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Matchalitchi Akulowera Kuti?

Kodi Matchalitchi Akulowera Kuti?

Kodi Matchalitchi Akulowera Kuti?

KODI n’chiyani chikuchitika m’matchalitchi amene amati ndi achikhristu? Kodi kwanuko matchalitchiwa ayamba kuchepa kapena kuchuluka? Mwina mwamvapo zakuti anthu ayambanso kukonda zopemphera, ndipo nthawi zina timamva kuti anthu akuwonjezeka kwambiri m’mipingo ya ku Africa kuno, ku Eastern Europe, ku United States, ndi kumadera ena. Koma nkhani zochokera m’madera ena a padziko lonse, makamaka ku Western Europe, zimati matchalitchi akutsekedwa, anthu akuchepa m’mipingo, ndipo ambiri alibe chidwi ndi zopembedza.

Matchalitchi ambiri asintha kachitidwe ka zinthu chifukwa choti anthu ayamba kuchepa. Matchalitchi ena amati iwo saweruza kapena kutsutsa zochita za munthu ndipo amakhulupirira kuti Mulungu amasangalala ndi khalidwe lililonselo. Matchalitchi ambiri ayamba kuchita zinthu zosiyanasiyana zosangalatsa ndiponso zokopa, koma zosakhudzana ndi kupemphera. Matchalitchiwa akuchita zimenezi m’malo mophunzitsa anthu Mawu a Mulungu. Anthu ena okonda kupita kutchalitchi amaona kuti matchalitchiwa akuchita zinthu mogwirizana ndi mmene zinthu zilili masiku ano, komano anthu ambiri oona mtima amaona kuti n’kutheka kuti zimene matchalitchiwa akuchita n’zosemphana ndi ntchito imene Yesu anapereka. Tiyeni tione zinthu zimene matchalitchi akhala akutsata m’zaka makumi angapo zapitazi.