Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Mungachitire ndi Mavuto a Kuchuluka kwa Magalimoto Pamsewu

Mmene Mungachitire ndi Mavuto a Kuchuluka kwa Magalimoto Pamsewu

Mmene Mungachitire ndi Mavuto a Kuchuluka kwa Magalimoto Pamsewu

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU SPAIN

MUKUFUNIKA kukaonana ndi dokotala panthawi inayake, ndipo mwanyamuka panyumba panu mukuganiza kuti muli ndi nthawi yambiri. Koma simunaganizire kuti muyenda mu msewu wa magalimoto ambirimbiri. Nthawi ikutha ndipo galimoto yanu ikuyenda mwa pang’onopang’ono, mukuyamba kuda nkhawa kwambiri. Kenaka, mukufika pa ofesi ya dokotalayo mutachedwa ndi mphindi 30.

Kuchuluka kwa magalimoto n’chimodzi mwa zinthu zomwe zimavutitsa kwambiri anthu okhala m’mizinda, makamaka magalimoto akamayenda mothithikana m’misewu n’kumatulutsa utsi wowononga mpweya. N’zomvetsa chisoni kuti mavuto a tsiku ndi tsiku amenewa, amene anthu okhala m’mizinda amakumana nawo akuoneka kuti sadzatha.

Ponena za ku United States, bungwe loona za maulendo la Texas Transportation Institute, linati: “Vuto la kuchulukana kwa magalimoto lili ponseponse, m’mizinda ndi m’matawuni momwe.” Bungweli linapitiriza kunena kuti akuluakulu aboma akulephera kupeza njira zoyenerera zothandizira anthu oyenda m’mizinda pa vuto limene likukulirakulirali. Zimenezi n’zimene zikuchitikanso pa dziko lonse. Posachedwapa, anthu ambiri oyenda pa galimoto ku China anachedwa kwambiri pamsewu chifukwa choti magalimoto anapanga chimzere chotalika makilomita 100, ndipo apolisi zinawatengera masiku ambiri kuti akonze zinthu. Ndipo mumzinda wa Mexico City, ulendo wa makilomita 20 wodutsa m’katikati mwa mzindawo ungatenge maola oposa anayi kuyenda pa galimoto, pamene kuyenda wapansi ulendo womwewu ungatenge nthawi yocheperapo.

Si zovuta kudziwa chifukwa chimene chimachititsa kuti misewu ya m’mizinda ikhale yodzadza. Mizinda ikukulirakulira, ndipo masiku ano pafupifupi theka la anthu onse padziko lapansi amakhala m’mizinda kapena m’matawuni. Pamene mizindayi ikukula, chiwerengero cha magalimotonso chikuwonjezereka. Wolemba magazini wina analemba kuti: “Anthu okhala ndi magalimoto ambiri achuluka kwambiri, ndipo amafuna kuyendetsa magalimotowo m’misewu yomwe ili yodzadza kaleyi.”

Chifukwa Chake Mavutowa N’ngovuta Kuwathetsa

Mizinda iyenera kupeza njira zochepetsera vuto la kuchuluka kwa magalimoto, makamaka chifukwa choti anthu amadalira kwambiri magalimotowa. Mumzinda wa ku United States wa Los Angeles, momwe muli anthu pafupifupi mamiliyoni anayi, tsopano muli magalimoto ochuluka kuposa anthu. Ndipo m’mizinda ina mwina chiwerengero cha magalimoto sichinafike pamenepa, komabe ndi mizinda yochepa yokha imene sikuvutika chifukwa cha kuchuluka kwa magalimoto. Carlos Guzmán, yemwe ndi pulezidenti wa bungwe la Madrid’s Urban Commission ananena kuti: “Pomanga mizinda ina sanaganizire za magalimoto.” Mizinda yakale kwambiri, yomwe misewu yake ndi yaing’onoing’ono, ndi yomwe panopa imavutika kwambiri ndi vuto limeneli. Komabe, ngakhale misewu ikuluikulu ya m’mizinda yamakono sichedwa kudzadza, makamaka panthawi ya m’mawa ndi madzulo, anthu akamapita ndi kuweruka kuntchito. M’lipoti lake lotchedwa “Mavuto a Mayendedwe M’mizinda,” Dr. Jean-Paul Rodrigue ananena kuti: “Pafupifupi tsiku lonse, m’mizinda ikuluikulu tsopano mukumakhala magalimoto ochuluka, ndipo magalimotowo akuchulukirachulukirabe.”

Popeza kuti kuchuluka kwa magalimoto amene anthu akugula sikukulingana ndi misewu yatsopano imene boma lingathe kukonza, kuchuluka kwa magalimotoku kumachititsa kuti ngakhale misewu yabwino kwambiri izikhala yodzadza. Ndipo buku lonena za mavuto a pamsewu lotchedwa Stuck in Traffic—Coping With Peak-Hour Traffic Congestion, limati: “M’kupita kwa nthawi, kumanga misewu yatsopano kapena kukulitsa misewu yakale sikuchepetsa vuto la kuchuluka kwa magalimoto panthawi imene anthu akupita kapena kuweruka ku ntchito.”

Chinanso chimene chimawonjezera vutoli n’kusowa kwa malo oimikapo magalimoto. Panthawi ina iliyonse, magalimoto ambiri amangozungulirazungulira m’misewu ya mumzinda n’cholinga choti apeze malo abwino oimapo. Ndipo akuti utsi wowononga mpweya, umene magalimotowa amatulutsa, makamaka m’mizinda, umapha anthu pafupifupi 400,000 chaka chilichonse. Malinga ndi zomwe lipoti lina linanena, kukhala tsiku limodzi m’misewu ya mu mzinda wa Milan ku Italy n’kumapuma mpweya wake woipitsidwa ndi utsi wa magalimoto, n’chimodzimodzi ndi kusuta ndudu 15 za fodya.

Kuchuluka kwa magalimoto m’misewu kumabweretsanso mavuto ena monga kuwonongetsa anthu nthawi ndiponso kuchititsa madalaivala kusautsika m’maganizo. Kudziwa muyezo wa mmene anthu amavutikira m’maganizo mwawo chifukwa cha vutoli n’kovuta, koma kafukufuku wina anasonyeza kuti kuchuluka kwa magalimoto m’mizinda 75 ikuluikulu ya ku United States kumawonongetsa ndalama zokwana pafupifupi madola 70 biliyoni chaka chilichonse. Kodi pali chilichonse chimene anthu angachite kuti achepetse vutoli?

Njira Zina Zochepetsera Mavutowa

Mizinda yambiri yakhazikitsa malamulo okhwima ochepetsera mavutowa. Mzinda wa Singapore, womwe ndi umodzi mwa mizinda yomwe ili ndi magalimoto ochuluka kwambiri padziko lonse, unakhazikitsa malamulo ochepetsa chiwerengero cha magalimoto amene anthu angagule. Mizinda yachikalekale, ina mwa iyo ya ku Italy, inaletseratu magalimoto kufika m’katikati mwa mizinda imeneyi pafupifupi masana onse.

Njira ina imene yakhazikitsidwa m’mizinda ina ndiyo “kulipiritsa.” Madalaivala amayenera kulipira ndalama asanalowe m’katikati mwa mzinda. Ku London, njira imeneyi yathandiza kuchepetsa kwambiri vuto la kuchedwa, ndipo mizinda inanso ikufunitsitsa kuyamba kutsatira njira yomweyi. M’mizinda monga Mexico City m’dziko la Mexico, magalimoto amaloledwa kulowa m’katikati mwa mizinda imeneyi pamasiku enaake apadera okha, ndipo magalimotowo amaloledwa malinga ndi nambala imene ili pa galimotoyo.

Nawonso akuluakulu a mizinda apereka ndalama zochuluka zokonzetsera ntchito zokhudzana ndi kayendedwe, zokonzetsera misewu, ndiponso zomangira misewu yolambalala mizinda. Akuluakuluwa anaika nyali za pamsewu zoyendera makompyuta ndipo amagwiritsanso ntchito makompyuta podziwitsa apolisi pakachitika ngozi yochititsa kuti magalimoto ena azilephera kudutsa bwino pamsewupo. Misewu yapadera yodutsa mabasi okha, ndiponso ina yomwe amalola kutembenuza kayendedwe ka magalimoto kuti azilowera kwina malingana ndi kuchuluka kwa magalimoto pamsewupo, imathandiza kuchepetsako vutoli. Komabe, kuti vutoli lichepe anthu okhala ku deralo ayenera kuchita zinthu mogwirizanika.

Kodi Inuyo Panokha Mungachitepo Chiyani?

Yesu Khristu ananena kuti “zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zimenezo.” (Mateyo 7:12) Malangizo anzeru amenewa angathandize kuchepetsa ena mwa mavuto oipa kwambiri a pamsewu. Komano, ngati aliyense akungoganizira za iye mwini, ndiye kuti ngakhale njira zabwino kwambiri zochepetsera vutoli sizingathandize. Mfundo zotsatirazi zingakuthandizeni kuti musamavutike kwambiri ndi vuto la kuchuluka kwa magalimoto mumzinda wanu.

Pamaulendo afupiafupi, mungachite bwino kwambiri kungoyenda pansi kapena kukwera njinga. Nthawi zambiri, poyerekezera ndi kuyenda pa galimoto, kuchita zimenezi kumathandiza kwambiri chifukwa n’kosachedwetsa, n’kosavuta, ndiponso kumalimbitsa thupi. Pamaulendo ataliatali, mungachite bwino kwambiri kukwera basi kapena zinthu zina zotere. Mizinda yambiri ikuyesetsa kukonzanso bwino mabasi, sitima za pansi panthaka, ndi sitima za pamtunda n’cholinga chokopa anthu kuti azisiya magalimoto awo n’kumagwiritsa ntchito njira zimenezi. Ndipotu kugwiritsa ntchito njira zimenezi sikumawononga ndalama zambiri. Ngakhale kuti popita m’kati mwa mzinda wanuwo mungafunikire kukwera galimoto kuti mukafike ku malo okwerera mabasi kapena ku siteshoni ya sitima, mungathe kupitiriza ulendowo pokwera basi kapena zinthu zina zotere.

Koma ngati mungafunikirebe kukwera galimoto, ganizirani zoyendera pamodzi ndi anthu akudera lanulo amenenso akupita kumalo kumene inu mukupita. Imeneyi ndi imodzi mwa njira zothandiza kwambiri zochepetsera kuchuluka kwa magalimoto m’misewu, panthawi imene anthu akupita ndi kuweruka ku ntchito zawo. Ku United States, anthu 88 pa 100 aliwonse amene sakhala pafupi ndi kumene amagwira ntchito, amayenda pa galimoto, ndipo pafupifupi anthu awiri mwa anthu atatu aliwonse pa anthu amenewa, amayenda okhaokha m’galimoto yawoyo. Buku lonena za mavuto a pamsewu lija limati kulimbikitsa anthu ambiri kuti azikwera galimoto imodzi popita ndi pobwera kuntchito, “kungathandize kwambiri kuchepetsa vuto lochedwa pamsewu ndiponso la kuchulukana kwa magalimoto panthawi zimenezi.” Kuwonjezera apo, m’madera ambiri muli misewu yapadera imene mumayenda magalimoto omwe mwakwera anthu awiri kapena ochulukirapo. Magalimoto omwe mwakwera munthu mmodzi yekha saloledwa kuyenda m’misewu imeneyi.

Ngati mungathe, mungachite bwino kupewa kuyenda nthawi zimene magalimoto amakhala ochuluka kwambiri pamsewu. Zimenezi zimafewetsa zinthu kwa inu ndiponso kwa anthu ena oyenda pa magalimoto. Ndiponso ngati mumaimika bwino galimoto yanu, simuchititsa kuti magalimoto ena aziyenda movutikira. N’zoona kuti ngakhale anthu atatsatira njira zabwino kwambiri zochepetsera vutoli, sizingatanthauze kuti simudzachedwanso chifukwa cha kuchuluka kwa magalimoto pamsewu. Panthawi ngati zimenezo, kukhala ndi maganizo oyenera kungakuthandizeni kuti musapanikizike kwambiri.—Onani bokosi.

N’zodziwikiratu kuti ngati mumakhala mu mzinda waukulu, ndiye kuti mumachedwa pa msewu chifukwa cha kuchuluka kwa magalimoto. Komabe, inuyo panokha mukamatsatira njira zabwino zothandiza pa vutoli, mukamakonda ndi kuganizira ena, ndiponso mukakhala woleza mtima ndi madalaivala ena, ndiye kuti mungafike podziwa mmene mungalimbanirane ndi vuto limeneli.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 23]

Kukhazikitsa Mtima Pansi Panthawi Imene Magalimoto Achuluka Kwambiri Pamsewu

Jaime, yemwe amayendetsa galimoto la takisii mu mzinda wa Madrid ku Spain, kwa zaka zoposa 30 wakhala akupirira vuto la kuchedwa pa msewu chifukwa cha kuchuluka kwa magalimoto. Taonani njira zimene zimamuthandiza kukhazikitsa mtima pansi zinthu zikavuta pa msewu:

▪ Ndimatenga chinachake choti ndiziwerenga. Magalimoto akadzadzana mu msewu mpaka kufika poima, sindithamanga magazi ayi.

▪ Mzere wa magalimotowo ukamayenda pang’onopang’ono kwambiri, ndimatsegula wailesi ya m’galimotomo n’kumamvetsera nkhani kapena kaseti ya Baibulo. Kuchita zimenezi kumandithandiza kuti ndiziganizira zinthu zina m’malo mongoganizira za kuchuluka kwa magalimotoko.

▪ Sindimayimba wamba hutala, chifukwa imangosokoneza anthu ena ndipo siithandiza n’komwe. Posonyeza kuganizira ndi kulemekeza madalaivala ena, ndimapewa kuchita phuma, ndipo ndimathandizanso ena kuti azitero.

▪ Ndimayesetsa kukhala wodekha ndikakumana ndi madalaivala olusa, ndipo ndimayesetsa kuwapewa kwambiri. Kuleza mtima n’kofunika kwambiri.

▪ Ngakhale kuti ndimayesetsa kuyenda m’misewu ina yomwe mumadutsa magalimoto ocheperapo, ndimadziwitsabe anthu amene akwera m’galimoto yanga kuti nthawi zina tikhoza kuchedwa chifukwa cha kuchuluka kwa magalimoto mumsewu. Nthawi zina n’zosatheka kufulumira ngati mukuyenda mumzinda pagalimoto.