Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhwali Yachilendo ku Hawaii

Nkhwali Yachilendo ku Hawaii

Nkhwali Yachilendo ku Hawaii

INE NDI anzanga tinali osangalala kwambiri poganizira za ulendo wathu wopita ku chilumba cha Maui, ku Hawaii. Kwenikweni tinkafunitsitsa kukakwera pamwamba paphiri la Haleakala, lomwe n’lalitali mamita 3,055, kuti tikaone dzuwa likamatuluka. Tinamva kuti kuona zimenezi n’kochititsa chidwi zedi. Kungoti tinafunika kudzuka mbandakucha, nthawi ya 2 koloko, n’kuyenda pagalimoto kuchokera ku Kapalua, komwe tinali kukhala, n’kukafika mbali inayo ya chilumbachi. Kenaka tinafunika kuyendetsa galimoto pa chitunda chachikulu zedi pokwera phiri. Tinaganiza kuti poti tidzayenda mbandakucha ndiye kuti tikakhalako tokha. Komatu sizinatero ayi. Tinali pa chimzere cha magalimoto ambirimbiri amene anali kuyenda pang’onopang’ono mumsewu wokhotakhota wopita pamwamba pa phirilo. Mmene timafika pamwambapo, kunali kukuzizira kwambiri. Koma tinatenga mabulangete kuti tikafunde.

Anthu ambirimbiri anali kudikirira moleza mtima kuti dzuwa lituluke cha m’ma sikisi koloko. Aliyense ankaoneka kuti akuyembekezera zimenezi mwachidwi kwambiri, ndipo makamera anali atakonzeka kale kujambula zochititsa chidwizi. Koma tsoka ilo, nthawiyi itakwana tinakhumudwa kuona mitambo itayalana n’kumalowera m’chigwachi, n’kutilepheretsa kujambula zithunzi zosaiwalika zimene tinali okonzeka kujambula. Komatu umu ndi mmene mapiri a pafupi ndi nyanja ya Pacific alili; sapanganika ayi. Zitatero, tinangodzilimbitsa mtima n’kuyamba kudikirira kuti mitamboyo izimiririke pang’onopang’ono dzuwa likayamba kukwera. Kenaka panachitika zinanso zosayembekezeka. Titaponya maso patali, tinayamba kuona chigwa chopanda chilichonse chomwe chinali ndi tinjira tambirimbiri toyenda anthu apansi. Ayi, ulendowu wapindula ndithu.

Kenaka mwadzidzidzi tinamva kulira kodabwitsa kokhala ngati nkhuku ikutetera. Ndiyeno tinaona kuti ndi mbalame. Iyi ndi nkhwali yokongola kwambiri yopezeka ku Ulaya ndi ku Asia. Pachingelezi imatchedwa chukar, ndipo pa Chilatini imatchedwa Alectoris chukar. Panyengo yoswana, mbalamezi zimakonda kukhala pansi, chifukwa m’pamene zimamanga zisa zawo. Mbalame yomwe tinaonayo siinathawe mouluka ayi koma inangonjonjola basi.

Kodi mbalamezi zinapezeka bwanji pa chilumba chokongolachi? Zikuoneka kuti mbalamezi anachita kuzibweretsa kunoko. M’mayiko a ku North America omwe sizilumba, amaweta mbalamezi ndipo nthawi ndi nthawi amaziponyera m’tchire kuti anthu azikazisaka. Tinasangalala chifukwa choti ngakhale kuti sitinaone zimene tinabwerera, tinachitabe mwayi kwambiri kuonera pafupi chonchi mbalame yamanyaziyi.—Nkhaniyi tachita kutumiziridwa ndi munthu wina.