Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ukwati Wawo Unapulumutsidwa

Ukwati Wawo Unapulumutsidwa

Ukwati Wawo Unapulumutsidwa

Bwana wina ku South Africa anazindikira kuti wantchito wake wina wotchedwa Bella, anali ndi mavuto a m’banja. Choncho bwanayo anapempha Thandi, yemwe ndi wa Mboni za Yehova, kuti akalankhule ndi Bella. M’kucheza kwawo, Thandi anadziwa kuti Bella ankafuna kum’sudzula mwamuna wake.

Ndiyeno Thandi anam’patsa Bella mabuku awiri a Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja, ndipo anam’limbikitsa kuti akapereke buku limodzi kwa mwamuna wake. Bella anachitadi zimenezo. Patapita mlungu umodzi, Thandi anamva kuti mwamuna wa Bella akuwerenga bukulo ndipo tsopano zinthu zikuyendako bwino m’banja lawo. Patapita miyezi itatu Bella anauza Thandi kuti Mulungu wapulumutsa ukwati wawo kudzera m’mapemphero awo ndiponso buku la Chimwemwe cha Banja. Ndipotu nkhaniyi sinathere pomwepa.

Pamene bwana wa Bella anamva zimene zinachitikazi, bwanayo analimbikitsa anthu onse ogwira ntchito pa kampani yake kuti nawonso apeze bukuli. Pamapeto pake, mabuku oposa 100 a Chimwemwe cha Banja anagawidwa kwa anthu a pakampaniyo. Buku limeneli lili ndi masamba 192 ndipo ili ndi mitu yothandiza monga yakuti, “Ngati Ukwati Ukufuna Kusweka,” “Tetezerani Banja Lanu ku Zisonkhezero Zowononga,” ndi “Sungani Mtendere M’banja Mwanu.”

Mungaitanitse buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja polemba zofunika m’mizere ili m’munsiyi ndipo tumizani ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili pa tsamba 5 la magazini ino.

□ Popanda kulonjeza kuti ndidzachita chilichonse, ndikupempha kuti munditumizire buku lomwe lasonyezedwa panoli.

□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.