Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Achinyamata Avuta ndi Intaneti!

Achinyamata Avuta ndi Intaneti!

Achinyamata Avuta ndi Intaneti!

Kodi mungamve bwanji ngati mwana wanu atachita zinthu zotsatirazi: Kuyenda yekhayekha mumsewu usiku.

Kupanga phwando kunyumba kwanu, inu osadziwa chilichonse.

Kutenga makiyi a nyumba yanu n’kukapangitsa ena ofanana nawo ndendende kenaka n’kumapatsa anthu osawadziwa m’pang’ono pomwe.

NGATI mwana wanu amagwiritsira ntchito Intaneti, n’zotheka ndithu kuchita zinthu zofanana ndi zimene tafotokozazi. Magazini ya Science News inati: “Intaneti yathandiza kuti pakhale njira zambiri zedi zolankhulirana pogwiritsira ntchito kompyuta. Zina mwa njira zimenezi ndi monga kulandira kapena kutumizirana zinthu zosiyanasiyana monga nyimbo kapena zithunzi, kutumizirana mauthenga ofika nthawi yomweyo, ndiponso kucheza ndi ena.”

Sizinatenge nthawi kuti achinyamata adziwe kugwiritsira ntchito Intaneti. Tangoganizani kuti mu 2004, ku United States pafupifupi ana 9 pa ana 10 aliwonse a zaka zapakati pa 12 ndi 17 ankagwiritsira ntchito Intaneti. Masiku anotu Intaneti ikupezeka pafupifupi dziko lonse.

Palibe munthu amene angatsutse kuti Intaneti n’njofunikira. Koma aliyense amafunika kusamala nayo. Mwachitsanzo, achinyamata ambiri amakhala okhaokha akucheza ndi anthu osiyanasiyana pa Intaneti, ndipo ena mwa anthuwo ndi oti inuyo ngakhale mwana wanuyo sangalole kuti afike pakhomo panu.

Chifukwa cha chibwana, achinyamata ena amaulula zinthu zokhudza iwowo zosayenera kuuza ena, ndiponso amatumiza zithunzi zawo pa Intaneti. Pulofesa Zheng Yan wa ku yunivesite yotchedwa State University of New York, anati achinyamata “nthawi zambiri sazindikira kuti pali anthu ambiri amene amawerenga kapena kuona zimene amatumizazo, kuphatikizapo zidyamakanda.”

Tatiyeni tione zinthu zimene achinyamata ambiri akuchita pa Intaneti. Zimenezi zitithandiza kuona misampha imene achinyamatawo angagweremo, kuona zimene amafuna pa Intanetipo, ndiponso kuona mmene tingawathandizire pa zinthu zofunikiradi pamoyo wawo. Zithandizanso achinyamata amene ndi Akhristu kukhala okhulupirikabe kwa Mulungu m’nthawi zovuta zino.—2 Timoteyo 3:1-5.