Kachilombo Kopirira Modabwitsa
Kachilombo Kopirira Modabwitsa
YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU JAPAN
▪ FUFUZANI pafupifupi paliponse pamene pamapezeka madzi padziko pano, kaya ndi malo amene pamera ndere, kaya m’pachipale chofewa, m’mitsinje, mu akasupe a madzi otentha, m’nyanja, ndiponso ngakhale kuseri kwa nyumba yanu. Mwina mwamwayi mungathe kupeza kachilombo kam’madzi kofanana ndi chimbalangondo. Kachilomboka kali m’gulu la tizilombo topirira kwambiri m’chilengedwe chonse. N’kakang’ono kwambiri moti m’povuta kukaona. Kali ndi thupi lalifupi lomwe lili ndi tizigawo tinayi, ndipo n’lokutidwa ndi chikopa chomwe chimakateteza. Kalinso ndi miyendo 8 ndipo mwendo uliwonse uli ndi tizikhadabo kumapeto kwake. Maonekedwe a kachilomboka ndiponso mayendedwe ake n’ngofanana ndi a chimbalangondo.
Tizilomboti timayenda pang’onopang’ono. Tilipo ta mitundu yambirimbiri, ndipo panthawi imodzi yokha timatha kuikira dzira limodzi, awiri kapena mpaka 30. Mum’chenga kapena m’dothi lochepa chabe lachinyontho mungathe kupezamo tizilomboti mwina tokwana masauzande ambirimbiri. Malo abwino kwambiri amene mungapezeke tizilomboti ndi m’ndere zimene zimamera padenga la nyumba.
Tizilomboti tikhoza kukhalabe ndi moyo ngakhale m’malo oipa kwambiri. Buku la Encyclopædia Britannica linati: “Tizilombo tina totereti anatiika m’malo opanda chilichonse, ngakhale mpweya, kwa masiku 8. Kenako anatichotsa ndipo kwa masiku atatu anatiika m’malo ofundira bwino ndithu momwe munali gasi wa mtundu winawake. Atatichotsa mmenemu anatiika pa malo ozizira kwambiri, pafupifupi madigiri seshasi 272 kuposa kuzizira kwa madzi oundana. Komano atatichotsa mmenemu n’kutiika malo abwinobwino, tinakhalanso moyo.” Tizilomboti timathanso kukhala ndi moyo ngakhale atatiunika ndi mphamvu yowononga zinthu ya kuwala. Mphamvu yotereyi ingathe kupha munthu koma tizilomboti sitifa ngakhale ataichulukitsa nthawi mahandiredi ambirimbiri. Ndiponso akuti n’zotheka kuti tizilomboti tikhale ndi moyo kwa kanthawi ndithu ngakhale atakatiika kumalo komwe kulibe mpweya uliwonse m’mlengalenga.
Chinsinsi cha tizilomboti n’chakuti, timakhala ngati tafa ndipo sitigwiritsa ntchito chakudya m’thupi mwawo, moti zimangokhala ngati kuti thupilo lasiyiratu kugwira ntchito. Kuti tizilomboti tikhale ngati tafa, timalowetsa miyendo m’kati mwa thupi lawo ndipo madzi otayika a m’thupimo amalowedwa m’malo ndi mtundu winawake wapadera wa shuga. Kenako timatulutsa phula n’kudzimata n’kumaoneka ngati kampira kenakake kakang’ono. Madzi akayamba kupezekanso pamangopita mphindi kapena maola ochepa chabe, kuti tizilomboti tibwererenso mwakale n’kukhala bwinobwino. Panthawi ina, tizilombo tina totereti timene tinakhala ngati tafa kwa zaka 100, tinakhalanso ndi moyo bwinobwino.
N’zoonadi, tizilombo ‘tokwawa’ timeneti, timatamanda Yehova m’njira yawoyawo, ya phee komanso yodabwitsa.—Salmo 148:10, 13.
[Mawu a Chithunzi patsamba 30]
© Diane Nelson/Visuals Unlimited