Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kudzichepetsa ndi Mantha Kapena N’chamuna?

Kodi Kudzichepetsa ndi Mantha Kapena N’chamuna?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Kudzichepetsa ndi Mantha Kapena N’chamuna?

NTHAWI zambiri dzikoli limatama anthu odzikuza kapena kuti onyada kuti ndiwo tiyenera kuwatsanzira. Anthu odzichepetsa ndi ofatsa amaoneka ngati amantha, ochita zinthu zongofuna kusangalatsa ena. Koma kodi kudzichepetsa zenizeni ndi mantha? Ndipo kodi kudzikuza kapena kuti kunyada ndi chamuna? Kodi Baibulo limanenanji pa nkhaniyi?

Tisanapite patali, tineneretu kuti Baibulo limati pali kunyada kwina kumene sikolakwika. Mwachitsanzo, Akhristu ayenera kunyadira kuti Yehova ndi Mulungu wawo ndiponso kuti iye amawadziwa. (Salmo 47:4; Yeremiya 9:24; 2 Atesalonika 1:3, 4) Makolo ayenera kunyadira ana awo ngati anawo akupereka chitsanzo chabwino cha makhalidwe achikhristu ndi kukhala olimba mtima pochita zinthu zogwirizana n’kulambira koona. (Miyambo 27:11) Komabe, kunyada kuli ndi poipira pake.

Kuonetsetsa Khalidwe Lonyada ndi Lodzikuza

Tanthauzo limodzi la kunyada ndilo kudziona kuti ndiwe wofunika kuposa anthu ena. Kunyada kotereku kumam’patsa munthu maganizo odziona kuti n’ngoposa ena, mwina chifukwa cha kukongola, mtundu, udindo, luso, kapena chuma chake. (Yakobe 4:13-16) Baibulo limatchulapo za anthu “otukumuka chifukwa cha kunyada,” kapena kuti anthu amene amadzitukumula pa zifukwa zosamveka.—2 Timoteyo 3:4.

Komano anthu odzichepetsa amangodziona kuti n’ngofanana ndi munthu wina aliyense ndipo amadziwa kuti amalephera pena ndi pena chifukwa amavomereza kuti n’ngopanda ungwiro ndiponso n’ngapansi kwambiri podziyekezera ndi Mulungu. (1 Petulo 5:6) Komanso, amaona ndiponso kusangalala ndi makhalidwe abwino amene anzawo ali nawo. (Afilipi 2:3) Motero sachita njiru ndi zimenezi kapena kuchita kusowa tulo chifukwa cha nsanje. (Agalatiya 5:26) Motero m’pomveka kuti kudzichepetsa zenizeni kumatithandiza kuti tizigwirizana ndi anzathu ndiponso kuti tizikhala mtima uli m’malo.

Taganizirani chitsanzo cha Yesu. Asanabwere pa dziko lapansi, iye anali kumwamba komwe anali munthu wamphamvu wauzimu. Ndipo ali padziko pano, iye anali munthu wangwiro wopanga uchimo uliwonse. ( Yohane 17:5; 1 Petulo 2:21, 22) Anali munthu waluso losasimbika, wanzeru, ndiponso wodziwa zinthu kwabasi. Koma sankadzionetsera, m’malo mwake nthawi zonse ankakhala wodzichepetsa. (Afilipi 2:6) Nthawi ina iye anachita kufika posambitsa mapazi a atumwi ake; ndipo anachitanso zinthu zowaganizira kwambiri ana aang’ono. (Luka 18:15, 16; Yohane 13:4, 5) Ndipotu, Yesu anatenga kamwana n’kukaimika pambali pake, n’kunena mawu otsatirawa: “Aliyense amene adzichepetsa ngati mwana wamng’ono uyu ndi amene adzakhala wamkulu koposa mu ufumu wa kumwamba.” (Mateyo 18:2-4) Inde, Yesu ndiponso Atate wake amaona kuti munthu woposa ndi amene amadzichepetsa osati kudzikuza.—Yakobe 4:10.

Kudzichepetsa Ndiko Chamuna

Ngakhale kuti Yesu ndi chitsanzo cha kudzichepetsa, Iye sanali munthu wamantha wochita zinthu mongofuna kusangalatsa anthu. Iye anali wolimba mtima polankhula chilungamo mosayang’ana nkhope. (Mateyo 23:1-33; Yohane 8:13, 44-47; 19:10, 11) Chifukwa cha zimenezi, ngakhale anthu ena amene ankamutsutsa anayamba kum’patsa ulemu. (Maliko 12:13, 17; 15:5) Koma Yesu sankachita zinthu mopondereza ena. Mosiyana ndi anthu odzikonda, Yesu ankawafika anthu pamtima chifukwa cha kudzichepetsa, kukoma mtima, ndiponso chikondi chake. (Mateyo 11:28-30; Yohane 13:1; 2 Akorinto 5:14, 15) Ngakhalenso masiku ano, pali anthu ambiri amene amagonjera Khristu mokhulupirika chifukwa chomukonda zenizeni ndiponso chifukwa chomulemekeza kwambiri.—Chivumbulutso 7:9, 10.

Mawu a Mulungu amalimbikitsa anthu kukhala odzichepetsa chifukwa choti odzichepetsa amamva malangizo mosavuta ndipo zimakhala zosangalatsa kuwaphunzitsa. (Luka 10:21; Akolose 3:10, 12) Monga anachitira Apolo, yemwe anali Mkhristu waluso lophunzitsa, Iwo amakhala okonzeka kusintha maganizo awo, akauzidwa mfundo zolondola zatsopano. (Machitidwe 18:24-26) Chinanso anthu odzichepetsa saopa kufunsa, pamene nthawi zambiri anthu odzikuza amaopa kufunsa podziwa kuti ena azindikira kuti sakudziwa.

Taonani chitsanzo cha m’nthawi ya atumwi cha mdindo wa ku Aitiopiya, amene ankalephera kumvetsa mbali zinazake za Malemba. Mtumwi wachikhristu Filipo, anafunsa mdindoyu kuti: “Kodi mukumvetsa zimene mukuwerengazo?” Mwaitiopiyayo anayankha kuti: “Ndingamvetse bwanji popanda wondimasulira?” Kumenekutu kunali kudzichepetsa kwambiri, makamaka tikaganizira kuti munthuyu anali ndi udindo waukulu kwabasi m’dziko la kwawo. Chifukwa cha kudzichepetsa kwakeko anathandizidwa kumvetsa Malemba m’njira yozama kwambiri.—Machitidwe 8:26-38.

Mwaitiopiyayu anali wosiyana kwambiri ndi Alembi komanso Afarisi achiyuda, omwe panthawiyo ankadziona kuti anali pamwamba pa anthu ena onse pa zachipembedzo. (Mateyo 23:5-7) M’malo modzichepetsa, n’kumvetsera zonena za Yesu ndi otsatira ake, iwo ananyoza anthuwa n’kumayesetsa kuwapezera zifukwa. Motero, kudzikuza kwawo kunawatsekera mumdima wauzimu.—Yohane 7:32, 47-49; Machitidwe 5:29-33.

Kodi Muli Ngati Dongo Lofewa Kapena Louma?

Baibulo limati Yehova ali ngati woumba mbiya ndipo anthu ali ngati dongo loumbira mbiyazo. (Yesaya 64:8) Kudzichepetsa kumathandiza munthu kukhala ngati dongo lofewa, chifukwa Mulungu angathe kumuumba n’kukhala mbiya yokongola; pamene odzikuza ali ngati dongo louma lomwe limangofunika kuligamula basi. Munthu yemwe anatchuka kwambiri ndi khalidwe lodzikuza ndi Farao wa ku Aigupto amene anachitira mwano Yehova, mapeto ake n’kufa nazo. (Eksodo 5:2; 9:17; Salmo 136:15) Imfa ya Farao imamveketsa bwino kwambiri mfundo ya mwambi wakuti: “Kunyada kutsogolera kuonongeka; mtima wodzikuza ndi kutsogolera kupunthwa.”—Miyambo 16:18.

Zimene takambiranazi sizikutanthauza kuti anthu a Mulungu alibe vuto lililonse pa nkhani ya kunyada. Mwachitsanzo, atumwi a Yesu nthawi zambiri ankakangana pa nkhani yakuti wamkulu kwambiri ndani pakati pawo. (Luka 22:24-27) Komabe, iwo sanalekerere khalidweli, m’malo mwake anamvera malangizo a Yesu motero patsogolo pake anasintha khalidwe lawoli.

Solomo analemba kuti: “Mphotho ya chifatso ndi kuopa Yehova ndiye chuma, ndi ulemu, ndi moyo.” (Miyambo 22:4) Izitu ndi zifukwa zomveka zedi zokhalira ndi khalidwe la kudzichepetsa! Khalidwe limeneli limasonyeza chamuna ndiponso limachititsa kuti ena azitikonda. Koma chachikulu kwambiri n’chakuti Mulungu amasangalala nafe ndiponso tingathe kudzalandira mphotho ya moyo wosatha.—2 Samueli 22:28; Yakobe 4:10.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ Kodi kunyada kulikonse n’koipa?—2 Atesalonika 1:3,4

▪ Kodi khalidwe lodzichepetsa limathandiza bwanji pophunzira zinthu?—Machitidwe 8:26-38.

▪ Kodi atumiki a Mulungu amafunikira kuphunzira kukhala anthu odzichepetsa?—Luka 22:24-27

▪ Kodi anthu odzichepetsa ali ndi tsogolo lotani?—Miyambo 22:4

[Chithunzi pamasamba 20, 21]

Ana ankakonda Yesu chifukwa choti anali munthu wodzichepetsa