Kodi Mungayankhe Bwanji?
Kodi Mungayankhe Bwanji?
KODI ZINACHITIKIRA KUTI?
1. Kodi Mgonero wa Ambuye unachitikira kuti koyamba?
Lembani mzere mozungulira yankho lanu pa mapupa.
Nazarete
Yeriko
Yerusalemu
Betelehemu
◆ Kodi buledi wopanda chofufumitsa amaimira chiyani?
․․․․․
◆ Kodi vinyo wofiira amaimira chiyani?
․․․․․
▪ Kambiranani: Kodi Mgonero wa Ambuye umatikumbutsa chiyani? N’chiyani chimene chimakusangalatsani pa mwambo umenewu?
ZINACHITIKA LITI?
Tchulani anthu amene analemba mabuku a m’Baibulo amene ali m’munsiwa, ndipo lembani mzere wolumikiza buku ndi nthawi imene anamaliza kulilemba.
1077 B.C.E. 1040 B.C.E. 580 B.C.E 55 C.E 66 C.E
2. 2 Samueli
3. 2 Mafumu
4. 2 Akorinto
NDINE NDANI?
5. Anzanga anandibweretsera madzi kuti ndimwe, koma ndinawathira pansi ngati magazi.
NDINE NDANI?
6. Ena anati iwowo ndi anthu anga; ena anati iwowo ndi anthu a Paulo, a Apolo, kapena a Khristu.
KUCHOKERA M’MAGAZINI INO
Yankhani mafunso awa, ndipo tchulani mavesi a m’Baibulo omwe akusowa.
Tsamba 8 Kodi timafunikira kutsimikizira chiyani? (Afilipi 1:․․․)
Tsamba 9 Kodi mungakhale bwanji anzeru? (Miyambo 13:․․․)
Tsamba 20 Kodi ndani amene adzakhale wamkulu mu “ufumu wa kumwamba”? (Mateyo 18:․․․)
Tsamba 29 Kodi ndi ndani amene sadzalowa mu Ufumuwo? (Aefeso 5:․․․)
Zithunzi Zoti Ana Apeze
Kodi mungapeze zithunzi izi m’magazini ino? Fotokozani nokha zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.
(Mayankho ali patsamba 19)
MAYANKHO A MAFUNSO A PA TSAMBA 31
1.Yerusalemu—Mateyo 21:10, 17, 18; 26:17-19.
◆ Thupi la Yesu.—Mateyo 26:26.
◆ Magazi a Yesu.—Mateyo 26:27, 28.
2. Gadi, Natani, 1040 B.C.E
3. Yeremiya, 580 B.C.E.
4. Paulo, 55 C.E.
5. Davide.—2 Samueli 23:15-17.
6. Kefa, kapena Petulo.—Yohane 1:42; 1 Akorinto 1:12.