Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuthandiza Achinyamata Kukhalabe Okhulupirika

Kuthandiza Achinyamata Kukhalabe Okhulupirika

Kuthandiza Achinyamata Kukhalabe Okhulupirika

DZIKOLI, zochita zake, ndiponso mafashoni ake akhala akusinthasintha. Makamaka chifukwa cha luso la zopangapanga zamakono, kusintha kumeneku kukuonekera kwambiri panopa. Zinthu zimene zinali zotchuka dzulo, lero zimakhala zitatha fasho, ndipo zimene zatchuka lero, mawa zidzakhala zitatha fasho. Kusintha kwa zinthu kumeneku kwasinthanso kwambiri zochita za achinyamata.

Zinthu Zasintha

Posachedwapa, luso la zopangapanga lasintha kwambiri zochita za achinyamata. Mwachitsanzo, m’mayiko ambiri matelefoni am’manja ndi makompyuta asanduka njira zofunikira kwambiri zolankhulirana pakati pa achinyamata. Njira zochezera pa Intaneti zachititsa kuti anthu azilankhulana m’njira zambiri zatsopano. Mtsikana wina wa ku Australia wa zaka 19 anati: “N’zotheka kukhala wopanda mnzako aliyense koma tsiku limodzi lokha n’kupeza anzako ambirimbiri pa Intaneti.”

Palibe angatsutse kuti mafoni am’manja ndiponso Intaneti imathandiza m’njira zambiri. Komabe, zikuoneka kuti anthu ena afika pochita kumalephera kukhala bwinobwino popanda zinthu zimenezi. Donald Roberts, yemwe ndi pulofesa pa yunivesite ina anati, ana asukulu ena “sangakwanitse kukhala osalankhula pa telefoni zawo zam’manja pa kanthawi kochepa kamene amapuma akatuluka m’kalasi ya 10 koloko, kudikira kuti alowe m’kalasi ya 11 koloko.” Iye anapitiriza kuti: “Ndikuona kuti anawa samva bwino ngati palibe winawake woti azilankhula naye. Zimawavuta kuti angokhala phee.”

Achinyamata ena amachita kuvomereza okha kuti sangathe kungokhala phee basi. Stephanie, yemwe ali ndi zaka 16 anati: “Sindingakwanitse kungokhala osatumizira anzanga mauthenga pa Intaneti ndiponso pa foni yam’manja. Mmenemu ndi mmene ndimachezera nawo. Ndimati ndikangofika ku nyumba, ndimayatsa kompyuta n’kutsegula Intaneti ndipo ndimatha kuchezera . . . mpaka 3 koloko mbandakucha.” Mwezi uliwonse Stephanie amawononga ndalama zokwana madola 100 kapena mpaka 500 polipirira mafoni. Iye anati: “Pakali pano ndili ndi ngongole yokwana madola 2,000 yoti ndibweze kwa makolo anga chifukwa cha foni. Koma panopo ndazolowera kwambiri kukhala ndi foni moti sindingakhale bwinobwino popanda foni.”

Vuto la foni si kuwonongetsa ndalama kokha ayi. Elinor Ochs, yemwe ndi katswiri wa chikhalidwe cha anthu, anachita kafukufuku. Iye anapeza kuti mwamuna wapantchito akafika pakhomo, nthawi zambiri mkazi ndi ana ake amakhala otanganidwa kwambiri ndi zipangizo zamagetsi moti kawirikawiri samulonjera n’komwe. Amangoti maso dwii pa zipangizo zawozo. Katswiriyu anati: “Tinaonanso kuti n’zovuta kwambiri kuti makolo alowerere pa zochita za ana awo.” Ndiye anawonjezera kuti, pa kafukufukuyo anapeza kuti makolo akaona kuti ana awo atanganidwa ndi zipangizozo, amangowasiya basi poopa kuwasokoneza.

Kodi Kucheza pa Intaneti Si Koopsa?

Makolo ndiponso aphunzitsi ambiri akuda nkhawa poganizira nthawi imene achinyamata akuthera pa Intaneti pocheza ndi anthu ena. Kuti azicheza m’njira imeneyi, amakonza tsamba lawolawo pa Intanetipo lomwe amaikapo zithunzi, mavidiyo ndiponso amalembapo zinthu zochitika tsiku lililonse m’moyo wawo.

Chimene chimakopa anthu ambiri n’chakuti njira imeneyi imawathandiza kuti azicheza ndi anzawo mosavuta. Chinanso n’chakuti kukhala ndi tsamba lakelake pa Intaneti kumachititsa wachinyamata kumva kuti “akuuza ena maganizo ake.” M’pake kuti zimenezi zimakopa achinyamata, chifukwatu pamsinkhu umenewu munthu amakhala asanadzidziwe bwinobwino ndipo amafuna kuti aziuza ena maganizo ake n’cholinga choti azimumvetsa.

Komabe vuto limodzi limene limakhalapo n’lakuti, zimene anthu ena amalemba pa tsamba lawo la pa Intaneti zokhudza khalidwe lawo zimakhala zabodza. Sizisonyeza mmenedi iwowo alili koma zimene amalakalaka atakhala. Mnyamata wina wa zaka 15 anati: “M’kalasi mwathu muli kamwana kena kamene kamanama kuti kali ndi zaka 21 ndipo kamakhala ku Las Vegas.” Ana awiri onsewa amakhala kutali kwambiri ndi mzinda wa ku America umenewu, pa mtunda wa makilomita 1,600.

Chinyengo choterechi n’chofala kwambiri. Mtsikana wina wa zaka 18, wa ku Australia anati: “Mungathe kuchita china chilichonse pa Intaneti. Mungathe kudzisinthiratu kwabasi n’kukhala munthu winawina chifukwa palibe amene akukudziwani kuti ndinu ndani. Suopa chilichonse chifukwa ungathe kulemba zinthu zongopeka n’cholinga choti uoneke ngati munthu winawake. Mungathe kuikapo zithunzi zanu zomwe munajambulitsa mutavala zovala zinazake zoti simuvaladi kapena mukuchita zinazake zoti simuchitadi. Mungathe kulemba zinthu zimene simungathe kuuza munthu wina pamasom’pamaso. Mumaona kuti mungathe kuchita chilichonse popanda kuopa kanthu chifukwa choti palibe amene akukudziwani.”

Njira yocheza pa Intaneti ili ngati njira ina iliyonse yolankhulirana chifukwa nayonso ingathe kugwiritsidwa ntchito moyenerera kapena mosayenerera. Kodi makolonu mukudziwa zimene ana anu akuchita pa Intaneti? Kodi mukuonetsetsa kuti akuthera nthawi yawo pa zinthu zopindulitsa? * (Aefeso 5:15, 16) Komanso, kugwiritsa ntchito Intaneti molakwika kungalowetse wachinyamata m’mavuto ambiri oopsa. Kodi ena mwa mavuto amenewa ndi ati?

Intaneti Imafunika Kusamala Nayo

Chifukwa choti pa Intaneti munthu angathe kudzibisa mosavuta, zidyamakanda zimapezerapo mwayi wosakasaka tiana. Achinyamata angathe kugwa m’mavuto mosadziwa akamauza ena zinthu zachinsinsi zokhudza iwowo kapena akamalola kukumana ndi munthu amene anadziwana naye pa Intaneti. Buku lakuti Parenting 911 linati anthu ena amatsutsa mfundo imeneyi ponena kuti “n’zosavuta kuti ana avulazidwe kapena kuzunzidwa ku nyumba kwawo kapena pochita masewera kusiyana ndi kugwa m’mavuto otere chifukwa cha Intaneti. Komabe makolo ambiri amaona kuti n’zoopsa zedi kuti zidyamakanda zifike pa khomo pawo kudzera pa kompyuta n’kuipitsa khalidwe la ana awo.”

Pali njira zinanso zolankhulana pa Intaneti zomwe zikugwiritsidwa ntchito molakwika. Achinyamata ena akhala akugwiritsira ntchito Intaneti kuti azivutitsa anzawo, kuwasala, kuwazunza, kapena kuwawopseza. Ena amakonza masamba pa Intaneti omwe cholinga chake n’kungochititsa manyazi anzawo basi, ndipo ena akhala akutumiza makalata ndi mauthenga osiyanasiyana amiseche. Mkulu wa bungwe lina loyang’anira zachitetezo pa Intaneti anati iye akukhulupirira kuti ana okwana 80 pa 100 aliwonse a zaka zoyambira 10 mpaka 14 avutitsidwapo ndithu m’njira imeneyi.

N’zoona kuti khalidwe lovutitsa ena si lachilendo ayi. Kungoti masiku ano, mphekesera, miseche, ndi mabodza zingathe kufika patali kwambiri komanso mwachangu zedi. Chinanso, mphekesera, miseche ndiponso mabodza a masiku ano amakhala ovulaza kwambiri. Achinyamata ena amatenga mafoni awo am’manja n’kujambula zithunzi ndiponso mavidiyo ochititsa anzawo manyazi. Amatha kujambula zimenezi m’malo osiyanasiyana kusukulu kwawo, monga m’tizipinda tosungiramo katundu kapena m’bafa lomwe amasambiramo. Zithunzi zimenezi amaziika pa Intaneti n’kuzitumiza kwa aliyense amene angafune kuziona.

Zayamba Kudetsa Nkhawa Kwambiri

Nkhani ngati zimenezi zachititsa kuti Dipatimenti ya Zamalamulo ndi Zachitetezo ku New Jersey, m’dziko la United States, itumize kalata kwa makolo ndi anthu ena amene akusamalira ana. Kalatayo inali yowalimbikitsa “kuti athandize pa vuto lomwe layamba kudetsa nkhawa lokhudza kugwiritsira ntchito Intaneti pakati pa ana, akakhala kusukulu kapena kwina kulikonse.” M’kalatayo, dipatimentiyi inanena kuti ikuda nkhawa kwambiri ndi zomaika pa Intaneti nkhani kapena zithunzi zina zachinsinsi. Achinyamata ndi achikulire opulukira amakopeka kwambiri ndi masamba a pa Intaneti okhala ndi zinthu zimenezi. Kalatayo inapitiriza kuti: “Makolonu muyenera kudziwa kuti pali zifukwa zambiri zodera nkhawa ndi nkhani zimenezi. Muyeneranso kudziwa kuti mungathandize kwambiri kuteteza ana anu podziwa bwino nkhaniyi ndiponso kuona bwinobwino mmene anawo akugwiritsira ntchito Intaneti.”

Komatu n’zodabwitsa kuti makolo ena amadziwa zinthu zochepa zedi zokhudza zimene ana awo akuchita pa Intaneti. Mayi wina, amene amaonetsetsa zimene mwana wake wamkazi wa zaka 16 amachita pa Intaneti, anati: “Makolo angakhumudwe ndi kuchita manyazi kwambiri ngati atadziwa zimene ana awo amatumiza ndi kukambirana ndi ena pa Intaneti.” Malingana ndi katswiri wina woona zachitetezo pa Intaneti, achinyamata ena amatumiza zithunzi zochititsa munthu kuganiza za kugonana.

Zikusokoneza Achinyamata

Kodi tingati achikulirewa akungoda nkhawa monyanyira chifukwa choti anaiwala mmene moyo umakhalira paunyamata? Ayi, chifukwatu ofufuza apeza umboni wa zimenezi. Taganizirani izi: M’madera ena, pafupifupi wachinyamata mmodzi pa achinyamata atatu aliwonse a zaka zoyambira 15 mpaka 17 anagonanapo ndi winawake. Oposa theka la achinyamata a zaka zoyambira 13 mpaka 19 anati anagonanapo m’kamwa.

Kodi luso la zopangapanga zamakono lawonjezera vutoli? N’zosachita kufunsa. Lipoti lina la m’magazini ya New York Times linati: “Mafoni am’manja ndiponso Intaneti zimapereka mpata ochita zinthu mwachinsinsi moti sizivuta kufunsira munthu woti ungogonana naye basi.” Ndipotu munthu ungathe kukonza zokumana ndi mwamuna kapena mkazi podina mabatani angapo chabe pakompyuta. Ofufuza ena anati atsikana oposa 4 pa atsikana 5 aliwonse anavomereza kuti amachita zinthu motayirira akakhala pa Intaneti.

Anthu ena amene amapita pa Intaneti n’cholinga chokafuna chibwenzi kapena munthu woti angogonana naye amapalamula mavu pachisa. Jennifer Welch, wa mu Dipatimenti ya Polisi ku Novato m’boma la California anati: ‘Taona kuti anthu ochitidwa chipongwe monga kugwiriridwa akuchuluka.’ Iye anati ambiri amachitidwa chipongwe ndi munthu amene anam’dziwira pa Intaneti kenako n’kugwirizana zokumana naye pamasom’pamaso.

Chenjerani ndi “Nzeru za Dzikoli”

Nthawi zambiri nkhani zolangiza achinyamata m’manyuzipepala ndi m’magazini siziwapatsa malangizo amphamvu pankhani ya kugonana. N’zoona kuti zimawalimbikitsa kudziletsa ndi kukhala ndi khalidwe labwino, komano cholinga cha nkhanizo chimakhala chowalimbikitsa kuti “azidziteteza” osati azikana zogonana. Zikuoneka kuti opereka malangizowo amaganiza kuti: ‘Poti sitingaletse achinyamatawa khalidwe la kugonana, kuli bwino tingowaphunzitsa kukhala osamala.’

M’nkhani ina yomwe inalembedwa pa tsamba linalake lotchuka pa Intaneti lonena za achinyamata, inati mfundo zokhazo zimene achinyamata ayenera kuganizira pankhani ya kugonana ndi izi: (1) angathe kutenga mimba, (2) angathe kutenga matenda, (3) angathe kusokonezeka ngati onse awiri ali osakhwima maganizo. Nkhaniyo inati: “Zili ndi inuyo kusankha zimene mukufuna kuchita.” Inangotchulako pang’ono chabe za kukambirana nkhaniyi ndi makolo. Ndipo siinatchulepo m’pang’ono pomwe zoti kaya khalidweli n’labwino kapena n’loipa.

Ngati muli ndi ana, n’zosakayikitsa kuti mumafuna kuwapatsa malangizo anzeru osati “nzeru [zopusa ndi zosadalirika] za dzikoli.” (1 Akorinto 1:20) Kodi mungawathandize bwanji anawo kuti akule bwino n’kupewa mavuto amene tafotokoza m’nkhaniyi? Njira yake siyophweka ayi. Mwachitsanzo, kuchotsa kompyutayo kapena kulanda foniyo pakokha sikungathandize. Kuchita zinthu mopupuluma chonchi, sikungasinthe mtima wamwanayo. (Miyambo 4:23) Komanso ganizirani kuti n’zotheka kuti ana anu akugwiritsira ntchito mafoni ndi Intaneti pofuna kuthandizidwa pa nkhani zinazake zimene inuyo mungathe kuwathandiza bwino kwambiri. Kodi zina mwa nkhanizi n’ziti?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 13 Makolo asamathamangire kuletsa ana awo kukhala pa Intaneti koma aziona bwinobwino zinthu zimene ana awo amakonda kutsegula pa Intanetipo. Potero angawathandize anawo ‘kugwiritsa ntchito luntha lawo la kuzindikira.’ (Aheberi 5:14) Kuphunzitsa ana m’njira imeneyi kumawathandiza kwambiri akakula.

[Mawu Otsindika patsamba 4]

“Ndimati ndikangofika ku nyumba, ndimayatsa kompyuta n’kutsegula Intaneti ndipo ndimatha kuchezera . . . mpaka 3 koloko m’bandakucha”

[Mawu Otsindika patsamba 5]

“Mungathe kuchita china chilichonse pa Intaneti. Mungathe kudzisinthiratu kwabasi n’kukhala munthu winawina chifukwa palibe amene akukudziwani kuti ndinu ndani”

[Mawu Otsindika patsamba 7]

“Makolo angakhumudwe ndi kuchita manyazi kwambiri ngati atadziwa zimene ana awo amatumiza ndi kukambirana ndi ena pa Intaneti”

[Bokosi/Chithunzi patsamba 6]

Mtsikana Wina Akusimba za Vuto Locheza pa Intaneti

“Ndinayamba kucheza ndi ana asukulu anzanga komanso aphunzitsi pa tsamba lomwe sukulu yathu inakonza pa Intaneti. Poyamba ndinkacheza nawo kwa ola limodzi pamlungu. Posakhalitsa ndinayamba kucheza nawo tsiku lililonse. Zimenezi zinandilowerera kwambiri kufika poti ndinkangoganizira zomwezo ndikakhala kuti sindili pa Intaneti, moti ndinkalephera kuchita zinthu zina mokhazikika maganizo. Ndinayamba kulephera ku sukulu, ndipo sindinkamvetsera bwinobwino kumisonkhano yachikhristu, komanso anzanga ndinasiya kuwawerengera. Patapita nthawi makolo anga anatulukira vuto langali ndipo anandiletsa kumakhala pa Intaneti nthawi yaitali. Zinali zovuta kwambiri kuti nditsatire zimenezi, moti ndinalusa kwambiri. Koma panopo ndimaona kuti makolo anga anachita bwino kundiletsa, ndipo ndinasintha khalidweli. Sindifuna ngakhale pang’ono kuti khalidwe limeneli lidzandilowererenso!”—Anatero Bianca.