Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mungathe Kuphunzira Chinenero China!

Mungathe Kuphunzira Chinenero China!

Mungathe Kuphunzira Chinenero China!

“Kunena zoona, pa zinthu zonse zimene ndachitapo palibe chinthu chabwino kuposa chimenechi,” anatero Mike. Nayenso Phelps anavomereza kuti: “N’chimodzi mwa zinthu zabwino kwambiri zimene ndachitapo pa moyo wanga.” Anthu onsewa akunena za ntchito yovuta yophunzira chinenero china.

M’MAYIKO ambiri padziko lonse, anthu ochuluka ayamba kuphunzira zinenero zina pa zifukwa zosiyanasiyana monga, zachuma, zachipembedzo ndi zina zambiri. Olemba Galamukani! anafunsa anthu angapo amene akuphunzira chinenero china. Ena mwa mafunso amene anafunsa ndi awa: Kodi zimakhala bwanji munthu akamaphunzira chinenero china atakula kale, ndiponso n’chiyani chingam’thandize kuti aphunzire? Nkhani ino yalembedwa mogwirizana ndi mayankho amene anthuwa anapereka. N’kutheka kuti mulimbikitsidwa ndiponso kuphunzirapo kanthu pa mfundo za m’nkhani ino, makamaka ngati mukuphunzira chinenero china kapena ngati mukuganiza zotero. Mwachitsanzo, taganizirani ena mwa makhalidwe amene anthu ofunsidwawo ananena kuti n’ngofunika kukhala nawo kuti munthu afike podziwa bwino chinenero china.

Kuleza Mtima, Kudzichepetsa ndi Kukhala Wokonzeka Kusintha

Ana amatha kuphunzira zinenero ziwiri kapena zingapo panthawi imodzi ndipo nthawi zambiri amaphunzira pongomvetsera basi. Koma kawirikawiri akuluakulu zimawavuta kwambiri kuphunzira chinenero china. Zimawavuta chifukwa nthawi zambiri kuphunzira chinenero kumatenga nthawi yaitali, motero pamafunika kuleza mtima. Ndipo chifukwa choti amakhala n’zochita zambiri, kawirikawiri amayenera kusiya kaye ntchito zawo zina.

George anati: “Pamafunika kudzichepetsa. Pophunzira chinenero china, osamachita manyazi kulankhula ngati mwana ndipo muzidziwa kuti nthawi zina anthu angakutengeni ngati mwana kumene.” Buku lakuti How to Learn a Foreign Language (Kuphunzira Chinenero China) limati: “Ngati mukufuna kupita patsogolo musiye kuganizira kwambiri za ulemu wanu ndi zofuna kuti ena azikupatsani ulemu kwambiri.” Motero, musamaope kulakwitsa popewa kuchita manyazi. Ben anati: “Ngati simukulakwitsa, ndiye kuti simukulankhula chinenerocho mokwanira.”

Musamadandaule anthu ena akamakusekani mukalakwitsa. Akamaseka, inunso muzingoseka nawo basi! Ndipotu, idzafika nthawi inayake imene muzidzasimbira ena nkhani zoseketsa za zimene mukulakwitsa panopa. Ndipo musamaope kufunsa mafunso. Mukamafunsa mafunso n’kumvetsa chifukwa chimene amanenera zinthu zina m’njira inayake, zimakuthandizani kuti musaiwale.

Popeza kuti mukamaphunzira chinenero china, nthawi zambiri mumafunikanso kuphunzira chikhalidwe cha anthu a chinenerocho, ndi bwino kukhala okonzeka kusintha chikhalidwe ndi maganizo anu pankhani zina. Julie anati: “Kuphunzira chinenero china kwandithandiza kuzindikira kuti pali njira zambiri zoonera zinthu ndiponso zochitira zinthu. Njira iliyonse siiposa njira zinazo ayi.” Jay anati: “Yesetsani kugwirizana ndi anthu amene amalankhula chinenerocho, ndipo muzisangalala kucheza nawo.” Akhristu ayenera kuonetsetsa kuti anthu amenewa ndi mabwenzi abwino, amene amalankhula mawu aulemu. (1 Akorinto 15:33; Aefeso 5:3, 4) Jay anati: “Anthuwo akaona kuti mumawakonda, mumakonda zakudya zawo, nyimbo zawo, ndi zinthu zawo zina, nawonso amayamba kukukondani.”

Kuti mupite patsogolo kwambiri m’pofunika kuti muziwerenga mabuku a chinenerocho komanso muzilankhula kwambiri chinenerocho. George anati: “Timaphunzira chinenero ngati mmene nkhuku imadyera. Imangojompha pang’onopang’ono mpaka kukhuta.” Bill ndi mmishonale amene anaphunzira zinenero zingapo ndipo anati: “Ndikamapita kulikonse ndinkakhala ndi kapepala ka mawu osiyanasiyana ndipo ndinkawerenga kapepalaka ndikapeza nthawi.” Anthu ambiri aona kuti kuwerenga kwa nthawi yochepa koma mwa kawirikawiri n’kothandiza kusiyana ndi kuwerenga kwa nthawi yaitali koma mwa apo ndi apo.

Pali zinthu zambirimbiri zothandiza munthu kuphunzira chinenero, monga mabuku, matepi kapena ma CD, ndi zina zotere. Ngakhale kuti pali zinthu zonsezi, anthu ambiri amaona kuti njira yabwino kwambiri yophunzirira chinenero ndiyo kuphunzirira pa gulu m’kalasi. Gwiritsani ntchito njira zilizonse zimene zingakuthandizeni. Komabe dziwani kuti palibe njira yachidule yophunzirira chinenero imene siifuna khama. Koma pali njira zimene mungatsate kuti musavutike ndiponso kuti musangalale pophunzira chinenero. Njira imodzi ndiyo kumva, kuwerenga, kapena kulankhula chinenerocho kwa nthawi yaitali komanso kukhala ndi anthu a chinenerocho.

George anati: “Mukadziwa zinthu zina ndi zina komanso mawu angapo a m’chinenerocho, ndi bwino kwambiri kukakhala m’dera limene anthu ake amalankhula chinenero chimene mukuphunziracho.” Barb anavomereza mfundo imeneyi ponena kuti: “Kupita ku dera la chinenerocho kumakuthandizani kuti chinenerocho chikulowerereni.” Komanso zimenezi zimakuthandizani kuti muziganiza m’chinenerocho. N’zoona kuti anthu ambiri sangakwanitse kupita dziko lina, komabe mungathe kupeza njira zophunzirira chinenerocho kwanu komweko. Mwachitsanzo, kwanuko kungathe kukhala mabuku kapena mapulogalamu abwino a pawailesi kapena pa TV a m’chinenero chimene mukuphunzira. Pezani anthu m’dera lanulo amene amalankhula bwino chinenerocho ndipo muzilankhula nawo. Buku lonena za kuphunzira chinenero china lija limati: “Pa zonsezi chinthu chofunika kwambiri kuti mupite patsogolo ndicho kugwiritsira ntchito chinenerocho.” *

Kuima Pamodzimodzi

Pophunzira chinenerocho, nthawi zina mungathe kuona kuti mwaima pamodzimodzi, osapitanso patsogolo ayi. Kodi pamenepa mungatani? Choyamba, kumbukirani zimene zinakuchititsani kufuna kuphunzira chinenerocho. A Mboni za Yehova ambiri amayamba kuphunzira chinenero china pofuna kuthandiza ena kuphunzira Baibulo. Kukumbukira cholinga chanucho kungakulimbikitseni kuti muchikwaniritse.

Chachiwiri n’chakuti musamafune kuchita zinthu zosatheka. Buku lonena za kuphunzira chinenero china lija limati: “N’zoona kuti simungafike pomalankhula chinenerocho ngati kuti mukulankhula chinenero chanu. Cholinga chanu si chimenechi ayi. Koma n’chakuti anthu azitha kukumvetsani bwinobwino.” Motero musamadandaule kuti chinenerocho simukuchilankhula ngati chinenero chanu, koma muzingoyesetsa kunena zimene mukudziwazo m’njira yomveka bwino.

Chachitatu, onani zinthu zimene zikusonyeza mmene mwapitira patsogolo. Kuphunzira chinenero chatsopano kuli ngati kukula kwa udzu. Udzu suoneka kuti ukukula, koma pang’onopang’ono umapezeka kuti watalika. Chimodzimodzinso, mukakumbukira nthawi imene munayamba kuphunzira chinenerocho, ndithu muona kuti mwapita patsogolo. Pewani kudziyerekeza ndi ena. Mfundo yabwino kuitsatira pa nkhani imeneyi ili m’Baibulo pa Agalatiya 6:4. Lembali limati: “Aliyense payekha ayese ntchito yake, aone ndi yotani, pamenepo adzakhala ndi chifukwa chosangalalira mwa iye mwini, osati modziyerekeza ndi munthu wina.”

Chachinayi n’chakuti zindikirani kuti kuphunzira chinenero kumatenga nthawi yaitali. Taganizirani izi: Kodi mwana wa zaka zitatu kapena zinayi amadziwa kufotokoza nkhani bwinobwino? Kodi amalankhula motsatira malamulo onse a chinenero? Ayi satero. Komatu mwanayo amatha kulankhula zomveka ndithu. Inde, ngakhale mwana amatenga nthawi kuti aphunzire chinenero.

Chachisanu n’chakuti muziwerenga, kulemba kapena kulankhula chinenerocho kawirikawiri. Ben anati: “Panthawi inayake ndinkangokhala pamodzimodzi, osapita patsogolo chifukwa chosagwiritsa ntchito chinenerocho kawirikawiri.” Choncho pitirizani kugwiritsa ntchito chinenerocho. Musatope n’kulankhula m’chinenerocho. N’zoona kuti zimagwetsa ulesi kulankhula chinenero china ngati ukudziwa mawu ochepa chabe monga amachitira mwana. Mileivi anadandaula motere: “Chimandipweteka kwambiri n’chakuti ndimalephera kunena zimene ndikufuna pa nthawi imene ndikufuna kutero.” Koma kupwetekedwa mtima kotereku n’kumenenso kungakuthandizeni kuti muchite khama. Mike amakumbukira kuti: “Zinkandipweteka kwambiri kuti chinenerocho sindinkachidziwa bwinobwino moti nkhani zimene anthu akusimba ndiponso nthabwala zinkangondipita. Koma ndikuona kuti zimenezi n’zimene zinandithandiza kulimbikira kwambiri kuti ndichidziwe bwino chinenerecho.”

Mmene Ena Angathandizire

Kodi anthu amene akudziwa kale chinenerocho angathandize bwanji anthu amene akuphunzira? Bill, amene tam’tchula kale uja anapereka malangizo akuti: “Muzilankhula nawo mwachifatse, koma mosalakwitsa, mosakhala ngati mukulankhula ndi mwana.” Julie anati: “Khalani oleza mtima, ndipo musamawadule pakamwa pomalizitsa mawu amene akuvutika kutchula.” Tony akukumbukira kuti: “Anthu achinenero chimene ndinkaphunzira, amene amalankhulanso chinenero changa, ankakonda kundilankhulitsa m’chinenero changacho. Koma zimenezi zinkangondibwezera m’mbuyo basi.” Motero, anthu ena ophunzira chinenero auzapo anzawo kuti panthawi inayake azingowalankhula m’chinenero chimene akuphunziracho basi ndiponso kuti aziwauza zinthu zosiyanasiyana zimene akulakwitsa. Chinanso, anthu amene akuphunzira chinenero amamva bwino ena akawamayamikira chifukwa cha khama lawo. George anati: “Sindikanatha kuphunzira chinenerocho popanda chikondi ndiponso kulimbikitsidwa ndi anzanga.”

Motero, kodi kuphunzira chinenero n’kopindulitsadi? Bill, amene tanena kale kuti amalankhula zinenero zingapo, anati: “Inde, n’kopindulitsa kwambiri! Ineyo kuphunzira chinenero kwanditsegula maso ndi kundithandiza kuona moyo mosiyana ndi mmene ndinkauonera poyamba. Phindu lalikulu n’lakuti kuphunzira Baibulo ndi anthu a zinenero zina n’kuwaona akuvomereza choonadi n’kuyamba kupita patsogolo n’kosangalatsa zedi. Ndipotu panthawi ina, katswiri wina wa maphunziro a zinenero, yemwe amalankhula zinenero 12 anandiuza kuti: ‘Ndimasirira zimene umachita. Ine ndimaphunzira zinenerozi chifukwa choti ndimangokonda kuphunzira zinenero basi; koma iweyo umaphunzira zinenero kuti uthandize anthu.’”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Onani Galamukani! ya Chingelezi ya January 8, 2000, tsamba 12-13.

[Mawu Otsindika patsamba 11]

Mtima wofuna kuthandiza ena ungakulimbikitseni kwambiri kuti muphunzire chinenero china