Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mwambo Wosafunika Kuuphonya

Mwambo Wosafunika Kuuphonya

Mwambo Wosafunika Kuuphonya

“Muzichita zimenezi pondikumbukira ine.” Mawu amenewa a Ambuye wathu Yesu Khristu, opezeka pa Luka 22:19, ananenedwa pa nthawi imene Yesu anakhazikitsa mwambo wa Chikumbutso cha imfa yake. Imfa ya Yesu ndi imene inatsegula njira yakuti anthu akhale ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso. Choncho m’poyenera kuti tizikumbukira imfa yake.

Kodi mudzapezeka pa Chikumbutso cha chaka chino?

Dzapiteni ku mwambo wofunikawu womwe a Mboni za Yehova akukuitanirani. Mwambowu udzayamba dzuwa litalowa pa tsiku la Nisani 14, mu kalendala ya Baibulo. Chaka chino tsikuli ndi Lolemba, pa April 2. Mboni za Yehova za kwanuko zingakuuzeni malo ndi nthawi yeniyeni imene mwambowu udzakhaleko m’dera lanu.