Ndinasankha Ntchito Yabwino Kwambiri
Ndinasankha Ntchito Yabwino Kwambiri
Yosimbidwa ndi Sonia Acuña Quevedo
Ndinkagwira ntchito ku banki ndipo anandiuza kuti andikweza udindo. Ndikanalola, ndikanakhala bwana ndipo ndikanayamba kulandira ndalama zambiri. Komabe, ndinali nditangoitanidwa kumene kuti ndikachite upainiya wa nthawi zonse ku mpingo winawake wakutali. Tsopano padutsa zaka 32, ndipo ndikaganiza chimene ndinasankha pa zinthu ziwirizi, ndimadziwa kuti ndinasankha mwanzeru.
MAYI anga anali a tchalitchi cha Katolika koma ankakayikira ziphunzitso za tchalitchichi. Zinkawavuta kumvetsa kuti, n’chifukwa chiyani tchalitchichi chimalambira zinthu zosemedwa ndi anthu? Popeza kuti mayi ankaona kuti choonadi n’chofunika, anapita m’matchalitchi ambiri osiyanasiyana kuti amvetse bwino nkhani ngati zimenezi, koma sizinaphule kanthu.
Tsiku lina mayi anakhala panja pa nyumba yathu yomwe inali mumzinda wa Tuxtla, ku Mexico, kuti aziwombedwako kamphepo, ndipo munthu wina wa Mboni za Yehova anafika panyumbapo. Mayi anagoma kwambiri ndi mmene munthuyu anawayankhira mafunso awo kuchokera m’Baibulo, motero anavomera kuti adzabwerenso. Wa Mboniyo atabweranso, anapeza kuti mayi akum’dikirira ali limodzi ndi mkulu wa mpingo wa Angilikani, wansembe wa Katolika, ndiponso mlaliki wa tchalitchi cha Nazarene. Mayi anafunsa funso lokhudza za Sabata, ndipo pa anthu onse amene anali pamenepo, wa Mboni yekhayo ndi amene anayankha mogwira mtima kuchokera m’Malemba. Ndipotu, wa Mboni yekhayo ndi amene anali ndi Baibulo. M’chaka cha 1956, atangophunzira Baibulo kwa miyezi 6 yokha, mayi anabatizidwa n’kukhala Mboni ya Yehova. Panthawi imeneyo ine ndinali ndi zaka 8.
Bambo Ankada Nazo Nkhawa
Bambo sankaletsa mayi kuphunzira Baibulo. Koma bambo anawononga mabuku onse a mayi, mayiwo atayamba kutiphunzitsa Baibulo anafe (tinalipo ana anayi, amuna awiri akazinso awiri) ndiponso titayamba kupita ku misonkhano yachikhristu. Iwo ankaona kuti mayiwo akutiphunzitsa zabodza, ndipo anayesa kugwiritsa ntchito Baibulo la Katolika kuti atisonyeze kuti Mboni zinaika mwachinyengo dzina la Mulungu lakuti Yehova m’Baibulo lawo. Mayi atawasonyeza bambo dzina lakuti Yehova m’Baibulo lawo lomwelo, anadabwa kwambiri ndipo anasiya kudana ndi Mboni.—Salmo 83:18.
M’dziko la Mexico, mtsikana akakwanitsa zaka 15, mwambo wokondwerera tsiku lake lobadwa umakhala wapadera kwambiri. Koma popeza kuti mapwando okondwerera tsiku lobadwa sagwirizana ndi Malemba, ine ndinasiya kukondwerera tsiku langa lobadwa. * Koma bambo anga ankafunabe kuti andipangire chinthu chinachake chapadera. Nditaganizira za nkhaniyi ndinawauza bambo kuti: “Ndikufuna inuyo mukhale mphatso yanga mwakupita nane limodzi ku msonkhano waukulu wa Mboni za Yehova umene ukubwerawo.” Anavomera, ndipo anayamba kuchita chidwi kwambiri ndi Baibulo.
Usiku wa tsiku lina, pambuyo pa chimvula cha mphepo, bambo anavulala kwambiri atakhudza nthambo ya magetsi yomwe inagwa pansi. Ali m’chipatala, Mboni za kumeneko zinali kuwasamalira usana ndi usiku. Chikondi chachikhristu choterechi bambo sanachiiwale. Ndipo kenako, bambo anayamba kulalikira ndipo anadzipereka kwa Yehova. N’zachisoni kuti, pa September 30, 1975, patatsala mwezi umodzi wokha kuti abatizidwe, anamwalira. Timalakalaka kwambiri kudzawaonanso akadzauka, n’kudzawakupatira.—Machitidwe 24:15.
Kulimbikitsana Pachibale
Mchemwali wanga Carmen, wakhala akuona kuti utumiki wa nthawi zonse n’ngofunika kwambiri. Atangobatizidwa mu 1967, anakhala mpainiya wokhazikika, ndipo mwezi uliwonse ankathera maola pafupifupi 100 muutumiki. Patapita nthawi, anasamukira ku Toluca, m’chigawo chapakati cha dziko la
Mexico. Ine nditamaliza sukulu, ndinapeza ntchito ku banki, ndipo ndinabatizidwa pa July 18, 1970.Carmen ankasangalala kwambiri ndi utumiki wa nthawi zonse, ndipo anandilimbikitsa kuti nanenso ndikayambe utumikiwu ku Toluca komwe iye anali. Izi n’zimene ndinali kuganizira tsiku lina pamene ndinkamvetsera nkhani yosonyeza kuti otsatira a Yesu anayenera kugwiritsa ntchito chuma chauzimu chomwe anali nacho kulemekezera Mulungu. (Mateyo 25:14-30) Ndinadzifunsa kuti: ‘Kodi ndikugwiritsa ntchito kwambiri mphatso zauzimu zimene ndapatsidwa?’ Zimenezi zinandipatsa maganizo ofuna kutumikira kwambiri Yehova.
Ndinasankha Bwino
M’chaka cha 1974, ndinapempha kuti ndikakhale mpainiya ku dera lina. Posakhalitsa, ndinalandira telefoni ku ntchito, yochokera kwa mkulu wa mumpingo wina ku Toluca. Anafunsa kuti: “Takhala tikukudikiriranitu. Bwanji simukubwera?” Ndinadabwa kuti ndinali nditasankhidwa kuti ndikachite upainiya wapadera ku Toluca, koma zikuoneka kuti kalata yondidziwitsa zimenezi inasochera. (Apainiya apadera amavomera kukachita utumiki wawowu kulikonse kumene gulu la Yehova lawauza.)
Mwamsanga ndinauza bwana wanga kubankiko zoti ndikufuna kusiya ntchito. Koma iye anandidula pakamwa pondisonyeza pepala n’kunena kuti: “Sonia, tadikira kaye pang’ono, ifetu tauzidwa posachedwa pompano kuti iweyo uli m’gulu la akazi 7 omwe asankhidwa kuti akhale achiwiri kwa mamanijala. Kampani yathuyi sinayambepo yaika akazi pa udindo umenewu. Ndiye moti ukana?” Monga mmene ndinanenera poyambirira paja, ndikati ndivomere udindowu ndikanakhala bwana ndiponso bwenzi ndikulandira ndalama zambiri. Koma m’malo mwake ndinangom’thokoza bwana wanga uja n’kumuuza kuti ndatsimikiza kuti ndikufuna kuyamba kutumikira Mulungu kwambiri. Bwanayo anati: “Chabwino, pita, komabe nthawi iliyonse ukadzafuna ntchito udzabwere kuno.” Patapita masiku awiri ndinafika ku Toluca.
Kuchita Upainiya Wapadera Ku Mexico
Carmen anali atachita upainiya wapadera kwa zaka ziwiri pamene ine ndinam’peza ku Toluca. Tinasangalala kwambiri kukhalanso limodzi. Koma tinangokhala limodzi kwa nthawi yochepa. Patapita miyezi itatu, mayi anachita ngozi ndipo kenaka panafunika wina woti adziwasamalira ku nyumba. Titadziwitsa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova za nkhaniyi, Ine ndi Carmen tinagwirizana kuti Carmen abwerere ku nyumba kuti akasamalire mayiwo, ndipo anawasamalira kwa zaka 17. Panthawi imeneyo, iye ankachita upainiya wokhazikika, ndipo pofuna kuti azitha kusamalira mayi, anauza anthu amene ankaphunzira nawo Baibulo kuti azibwera ku nyumba.
M’chaka cha 1976, ananditumiza kukatumikira ku Tecamachalco. Mtauniyi anthu osauka ankakhala mbali ina ndipo anthu olemera ankakhala mbali inayo. Ndinayamba kuphunzitsa Baibulo mayi wina wachikulire yemwe anali asanakwatiwepo kwa moyo wake wonse. Mzimayiyu ankakhala ndi mlongo wake yemwe anali wolemera. Ndiyeno atamuuza mlongo wakeyo kuti akufuna kukhala Mboni, anamuopseza kuti am’thamangitsa kunyumba kwakeko. Komabe, mzimayi wodzichepetsayu sanachite mantha, ndipo atabatizidwa, mlongo wake uja anam’thamangitsadi. Ngakhale kuti panthawi imeneyo anali ndi zaka 86, anadalira Yehova ndi mtima wonse. Mpingo unamusamalira, ndipo anakhalabe wokhulupirika mpaka imfa yake.
Ndinapita ku Sukulu ya Gileadi, Kenaka ku Bolivia
Ndinasangalala kutumikira ku Tecamachalco kwa zaka zisanu. Kenaka anandiitana kuti ndikakhale nawo m’kalasi loyamba la Sukulu ya Gileadi Yowonjezera ku Mexico. Monga mmene dzina lakelo likusonyezera, sukuluyi inali nthambi ya sukulu imene inkachitikira ku New York. Mayi komanso Carmen anandikakamiza kuti ndivomere kupita, choncho ndinapita ku ofesi ya nthambi mu mzinda wotchedwa Mexico City. Inali kosi ya masabata l0, ndipo inandilimbikitsa kwambiri moyo wanga wauzimu. Titamaliza maphunziro athu pa February 1, 1981, ndinatumizidwa ku La Paz, ku Bolivia, limodzi ndi Enriqueta Ayala (tsopano ndi Enriqueta Fernández).
Titafika ku La Paz, abale odzatichingamira anali asanafike. Tinauzana kuti: “Tikutayiranji nthawi?” Choncho tinayamba kulalikira kwa anthu omwe anali pa bwalo la ndegepo. Titasangalala n’kulalikira kwa maola atatu, tinakumana ndi abale ochokera ku nthambi. Abale anapepesa kuti achedwa ndipo anati achedwa chifukwa choti m’misewu munali modzaza chifukwa cha zikondwerero.
Kulalikira M’dera Lokwera Kwambiri
Mzinda wa La Paz uli pa mtunda wokwera mamita 3,625 kuchokera pothera nyanja, choncho nthawi zambiri tinkakhala m’mitambo. Chifukwa cha kukwera kwa derali, mpweya unkakhala wochepa motero ndinkalalikira kwa nthawi yochepa chifukwa ndinkatopa mwamsanga. Ngakhale kuti zinanditengera
chaka chathunthu kuti ndizolowere kukhala m’dera lokwera chonchi, mavutowa ndinawaona kuchepa kwambiri poyerekezera ndi madalitso amene Yehova anandipatsa. Mwachitsanzo, tsiku lina m’mawa, m’chaka cha 1984, ndinakwera phiri linalake podutsa mbali imene kunali miyala yambiri ndipo ndinakafika pa nyumba yomwe inali pamwamba pa nsonga ina ya phirilo. Ndinatopa kwambiri ndipo nditagogoda, mzimayi anatuluka m’nyumbamo. Ndinacheza naye bwino kwambiri, ndipo ndinamuuza kuti ndidzabweranso pakapita masiku angapo.Mzimayiyo anati: “Aa, koma ine ndikukayikira.” Komabe nditapitakonso, mzimayiyo anandipempha kuti ndiziphunzira Baibulo ndi mwana wake wamkazi. Ndinayankha kuti: “Umenewo ndi udindo wa makolo, komabe ndikuthandizani ngati mukufuna.” Mzimayiyo anavomera kuti nayenso aziphunzira nawo Baibulo. Koma chifukwa choti sankadziwa kulemba ndi kuwerenga, tinayamba kuphunzira kabuku kakuti Phunzirani Kuŵerenga ndi Kulemba, kamene Mboni za Yehova zinakonza n’cholinga chothandiza anthu otere.
Patapita nthawi ana m’banjali anakwana 8. Ndikapita kunyumba kwawo, ena mwa anawa amapanga mzere atagwirana manja n’kumandikoka kuti andithandize kukwera phirilo. Pomaliza, banja lonselo linayamba kutumikira Yehova; bambo, mayi, ndi ana onse 8. Atsikana atatu m’banjalo ndi apainiya, ndipo mnyamata mmodzi ndi mkulu mumpingo. Bambo awowo anamwalira mu 2000, ndipo anali mtumiki wothandiza mumpingo. Ndimasangalala kwabasi ndikaganiza za banja labwino kwambirili ndiponso za kukhulupirika kwawo. Ndimayamika Yehova chifukwa chondilola kuthandiza banjali.
Ndinayambanso Kutumikira Limodzi ndi Carmen
Mayi atamwalira mu 1997, Carmen anaitanidwanso kuti akachite upainiya wapadera. M’chaka cha 1998 anapemphedwa kuti akatumikire kumene ndinkatumikira ineyo, ku Cochabamba, m’dziko la Bolivia. N’zoonadi, tinakhalanso limodzi pambuyo pazaka 18, ndipo Carmen anapatsidwa mwayi wokhala ngati mmishonale. Tinasangalala kwambiri ku Cochabamba, komwe kuli nyengo yabwino zedi moti akuti ngakhale mbalame zotchedwa namzeze sizifuna kuchokako. Panopo timakhala ku Sucre, m’dziko lomwelo la Bolivia, ndipo uwu ndi mzinda wokongola kwambiri wa anthu 220,000, womwe uli m’chigwa cha m’dera linalake lokwera. Poyamba unkatchedwa kuti mzinda wa Vatican waung’ono chifukwa kunali matchalitchi ambiri a Katolika. Tsopano mu mzindawu muli mipingo ya Mboni za Yehova yokwanira isanu.
Tikaphatikiza pamodzi zaka zimene ine ndi Carmen takhala tikuchita upainiya zikupitirira zaka 60, ndipo takhala ndi mwayi wothandiza anthu oposa 100 kubatizidwa. Ndithu, kutumikira Yehova ndi mtima wonse n’kopindulitsa kwambiri.—Maliko 12:30.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 8 Mapwando awiri okondwerera masiku akubadwa amene amatchulidwa m’Malemba anali achikunja ndipo panachitika zoipa. (Genesis 40:20-22; Maliko 6:21-28) Komabe, Mawu a Mulungu amalimbikitsa kuti tizipereka mphatso mochokera pansi pamtima, osati chifukwa cha anthu ena kapena anzathu ayi.—Miyambo 11:25; Luka 6:38; Machitidwe 20:35; 2 Akorinto 9:7.
[Chithunzi patsamba 15]
Ndinkakwera phiri linalake podutsa mbali imene kunali miyala yambiri kuti ndikaphunzitse banja ili
[Chithunzi patsamba 15]
Ndili muutumiki ndi mchemwali wanga Carmen (kumanja)